Ndandanda ya Mlungu wa February 15
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 15
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 15-18
Na. 1: Oweruza 16:1-12
Na. 2: Kodi ‘Gehena wa Moto’ Amene Yesu Anatchula Ndi Chiyani? (rs tsa.148 ndime 1–tsa.149 ndime 1)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Yesu Anatcha Mdyerekezi “Tate Wake wa Bodza”? (Yoh. 8:44)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kambiranani mwachidule nkhani za m’magaziniwa ndipo tchulani nkhani zimene anthu a m’gawo lanu angasangalale nazo. Sonyezani wofalitsa akulankhula yekhayekha pokonzekera kugawira magaziniwa. Iye asankhe nkhani zimene akuona kuti anthu a m’gawo lanu angachite nazo chidwi kwambiri. Ndiyeno akonze funso ndiponso asankhe malemba amene angagwiritse ntchito. Pomaliza, iye ayerekezere kugawira magazini iliyonse payokha.
Mph. 15: “Msonkhano Wadera Umene Udzatithandize Kuteteza Moyo Wathu Wauzimu.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.