Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/12 tsamba 2
  • Tetezani Maganizo Anu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tetezani Maganizo Anu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Msonkhano Wadera Umene Udzatithandize Kuteteza Moyo Wathu Wauzimu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Tetezani Chikumbumtima Chanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Msonkhano Umene Umathandiza Atumiki Achikhristu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 8/12 tsamba 2

Tetezani Maganizo Anu

1. Kodi msonkhano wadera wachaka chautumiki cha 2013 uli ndi mutu woti chiyani, ndipo cholinga cha msonkhanowu n’chiyani?

1 Yesu anauza ophunzira ake kuti azikonda Yehova ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse ndi maganizo awo onse. (Mat. 22:37, 38) Misonkhano yachigawo, yadera komanso yapadera ya chaka chino, yakonzedwa n’cholinga chotithandiza kulimbitsa umunthu wathu wamkati. Paja mutu wa msonkhano wachigawo ndi wakuti, “Tetezani Mtima Wanu!” Msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2013 uli ndi mutu wakuti, “Tetezani Chikumbumtima Chanu.” Ndipo misonkhano yadera yomwe iyambe mwezi wamawa ili ndi mutu wakuti, “Tetezani Maganizo Anu,” wochokera pa Mateyu 22:37. Msonkhano umenewu wakonzedwa kuti uthandize aliyense wa ife kuunika bwinobwino maganizo ake n’cholinga choti azisangalatsa Yehova.

2. Kodi pamsonkhanowu tidzayesetse kupeza mayankho a mafunso ati?

2 Mfundo Zimene Zikakambidwe: Tikamadzamvetsera nkhani pamsonkhano wadera tidzayesetse kupeza mayankho a mafunso otsatirawa, omwenso ndi mfundo zikuluzikulu za pamsonkhanowu:

• Kodi tingapewe bwanji kuganiza ngati mmene ‘anthu amaganizira’?

• Kodi tingathandize bwanji kuchotsa chophimba m’maganizo a anthu osakhulupirira?

• Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani?

• Kodi kusinkhasinkha zinthu zabwino kuli ndi phindu lanji?

• Kodi tingatani kuti tilole Yehova kuumba maganizo athu?

• Kodi amuna, akazi, makolo komanso ana angathandize bwanji kuti banja likhale losangalala?

• Kodi tingakonzekere bwanji tsiku la Yehova?

• Kodi kukonzekeretsa maganizo athu kuti tigwire ntchito kumafuna chiyani?

• Kodi anthu amene amatsatira zimene amaphunzira amapeza madalitso otani?

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzapezeka pamsonkhanowu masiku onse awiri, kudzamvetsera mwachidwi ndiponso kudzagwiritsa ntchito zomwe tidzaphunzire?

3 Satana ali pa nkhondo yolimbana ndi maganizo athu ndipo cholinga chake ndi kusokoneza maganizo athuwo. (2 Akor. 11:3) Chotero tiyenera kuteteza maganizo athu n’cholinga choti tizisangalatsa Mulungu. Tiyenera kupitiriza kukhala ndi maganizo a Khristu ndiponso kulimbana ndi mayesero amene timakumana nawo m’dziko la anthu osamvera malamuloli. (1 Akor. 2:16) Choncho yesetsani kuti mudzapezeke pa zigawo zonse za msonkhano waderawu ndipo muzidzamvetsera mwachidwi. Komanso kugwiritsa ntchito malangizo amene tidzamve pamsonkhano umenewu kudzatithandiza kuti tizilalikira uthenga wa Ufumu mwakhama.—1 Pet. 1:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena