Tetezani Chikumbumtima Chanu
1. Kodi msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2013 uli ndi mutu woti chiyani, ndipo cholinga cha msonkhanowu n’chiyani?
1 Tsiku lililonse timakumana ndi zinthu zimene zingatichititse kuti tisamvere chikumbumtima chathu. N’chifukwa chake mutu wa msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2013, chomwe chiyambe pa September 1, 2012, ndi wakuti, “Tetezani Chikumbumtima Chanu.” (1 Tim. 1:19) Msonkhanowu wakonzedwa n’cholinga chothandiza aliyense wa ife kuona bwino mmene amagwiritsira ntchito mphatso yamtengo wapatali imeneyi yochokera kwa Mlengi wathu.
2. Kodi ndi mafunso ati ofunika kwambiri amene adzayankhidwe pamsonkhano wapaderawu?
2 Mudzayesetse Kupeza Mfundo Zotsatirazi: Nkhani za pamsonkhanowu zidzatithandiza kupeza mayankho a mafunso 7 otsatirawa okhudza chikumbumtima, omwe ndi ofunika kwambiri:
• Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingasokoneze chikumbumtima chathu?
• Kodi chikumbumtima chathu tingachiphunzitse bwanji?
• Kodi zingatheke bwanji kukhala woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse?
• Kodi kuchita zinthu ndiponso kuganiza mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, kumasonyeza chiyani za ifeyo?
• Kodi tingatani kuti tipewe kuvulaza ena pa nkhani zokhudza chikumbumtima?
• Achinyamata, kodi mungatani kuti musagonje mukakumana ndi mayesero?
• Kodi tikamamvera chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino Baibulo timapeza madalitso otani?
3. Kodi msonkhanowu udzatithandiza bwanji?
3 Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kukhalabe olimba Satana akamatiyesa kuti tichite zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chathu. Pogwiritsa ntchito Mawu ake komanso gulu lake, Atate wathu wakumwamba yemwenso ndi wachikondi akutiuza kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mmenemu.” (Yes. 30:21) Msonkhano umenewu ndi imodzi mwa njira zimene Yehova akugwiritsa ntchito potitsogolera. Choncho, yesetsani kuti mudzapezekepo pa zigawo zonse za msonkhanowu. Muzidzamvetsera mwachidwi komanso kuona mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukaphunzire pa moyo wanu. Mudzakambirane mfundo za pamsonkhanowu ndi banja lanu. Kutsatira mfundo zimene tidzaphunzire kumsonkhanowu kudzatithandiza kuti ‘tikhalebe ndi chikumbumtima chabwino’ komanso tidzapewa kukopedwa ndi zinthu zosangalatsa za m’dziko la Satanali.—1 Pet. 3:16.