Ndandanda ya Mlungu wa August 13
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 13
Nyimbo Na. 133 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 10 ndime 10-21 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 28-31 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 28:17-26 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Muzisiyanitsa Nkhani Zoona ndi Zabodza Zokhudza Yesu Khristu (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Malemba Ati Amene Amachititsa Kuti Akhristu Asamalowerere Ndale?—rs tsa. 371 ndime 4 mpaka tsa. 372 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Yalani Maziko a Ulendo Wobwereza. Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mafunso otsatirawa: (1) N’chifukwa chiyani ndi bwino kuyala maziko a ulendo wobwereza pa ulendo wanu woyamba, ndipo mungachite bwanji zimenezi? (2) Kodi tingatani kuti timusiyire mwininyumba funso limene lingamuchititse chidwi, lomwe tingadzaliyankhe pa ulendo wotsatira? (3) N’chifukwa chiyani m’poyenera kuti nthawi zonse tizigwirizana nthawi yeniyeni ndi mwininyumba, yomwe tingadzabwerenso kuti tidzapitirize kukambirana? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kutenga nambala yake ya foni kapena adiresi yake ya imelo ngati zili zotheka kutero? (4) N’chifukwa chiyani tiyenera kubwererako mwamsanga, mwina patangopita masiku angapo? (5) Kodi tiyenera kulemba zinthu zotani tikamaliza kukambirana ndi munthu pa ulendo woyamba?
Mph. 10: Funsani mafunso munthu mmodzi kapena awiri amene akuchita utumiki wanthawi zonse. N’chiyani chinawalimbikitsa kuti ayambe utumiki umenewu? Kodi amakumana ndi mavuto otani pamene akuchita utumiki wanthawi zonse, ndipo n’chiyani chawathandiza kuti apitirizebe? Nanga apeza madalitso otani? Limbikitsani ofalitsa kuti aganizire zoyamba upainiya wokhazikika m’chaka chautumiki chikubwerachi.
Mph. 10: “Tetezani Chikumbumtima Chanu.” Mafunso ndi mayankho. Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ngati ladziwika.
Nyimbo Na. 65 ndi Pemphero