Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/95 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya July

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya July
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira July 3
  • Mlungu Woyambira July 10
  • Mlungu Woyambira July 17
  • Mlungu Woyambira July 24
  • Mlungu Woyambira July 31
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 7/95 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya July

CHIDZIŴITSO: Utumiki Wathu Waufumu udzasonyeza Msonkhano Wautumiki mlungu uliwonse mkati mwa nyengo ya msonkhano wachigawo. Mipingo ingapange masinthidwe ofunikira kuti ikapezeke ku Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” ndiyeno kubwereramo m’mfundo zazikulu za programuyo kwa mphindi 30 pa Msonkhano Wautumiki mlungu wotsatira. Kubwereramo m’programu ya tsiku ndi tsiku ya msonkhano wachigawo kuyenera kugaŵiridwa pasadakhale kwa abale okhoza bwino aŵiri kapena atatu amene adzafotokoza mfundo zazikulu. Kubwereramo kokonzedwa bwino kumeneku kudzathandiza mpingo kukumbukira mfundo zazikulu zoti agwiritsire ntchito paokha ndi m’munda. Kukambapo kwa omvetsera ndi kusimba zokumana nazo kuyenera kukhala kwachidule ndi kolunjika pamfundo.

Mlungu Woyambira July 3

Nyimbo Na. 194

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Fotokozani za “Mkupiti Wapadera wa July.”

Mph. 17: “Khalani Odikira.” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 18: “Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana mu Utumiki Wanu.” Kambitsiranani ndi omvetsera malingaliro osonyezedwa. Kambanipo mwachidule pa mbali zosangalatsa za mabrosha amenewo. Khalani ndi zitsanzo zachidule ziŵiri kapena zitatu zosonyeza mmene angagaŵiridwire.

Nyimbo Na. 213 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 10

Nyimbo Na. 110

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: “Kodi Zikumbutso za Yehova Zikutitsitsimutsa Mwauzimu?” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 20: Kupeza Mipata ya Kuchitira Umboni. M’nyengo ino yachilimwe, ambirife timakhala ndi mpata wa maulendo akumisonkhano ndi matchuthi, ndipo pamakhala mipata yabwino ya umboni wamwamwaŵi. Mwa kugwiritsira ntchito Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 81-2, ndime 11-16, pendani malingaliro a mmene kukambitsirana ndi munthu wachilendo kungayambitsidwire. Sonyezani mmene kukonzekera pasadakhale kumathandizira kupeza zotulukapo zabwino. Ofalitsa atatu osiyana asonyeze zitsanzo zachidule za mmene angayambire kukambitsirana ndi womwetsa mafuta pa malo omwetsera galimoto mafuta, amene akwera naye basi, ndi munthu amene waima pamzera mu supamaliketi. Kumbutsani ofalitsa kusunga cholembapo aja osonyeza chikondwerero ndi kupanga makonzedwe akuti wina akawafikire pambuyo pake.

Nyimbo Na. 154 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 17

Nyimbo Na. 192

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Pendani “Mkupiti Wapadera.”

Mph. 20: “Pangani Maulendo Obwereza pa Mabrosha Onse Amene Munagaŵira.” Mbale wopatsidwa mbali imeneyi adzakambitsirana ndi ofalitsa atatu za chifukwa chake kuli kofunika kubwererako kwa osonyeza chikondwerero ndi omwe anasiyako zogaŵira. Iwo akambitsirana maulaliki osonyezedwa ndipo achitira chitsanzo maulalikiwo mwa kulalikirana.

Mph. 15: Kuchititsa Phunziro la Baibulo Lapanyumba. Nkhani yokambidwa ndi mkulu amene amachititsa maphunziro opita patsogolo. Limbikitsani onse kuyesayesa kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Tchulani malingaliro operekedwa mu Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 90-91. Mungaphatikizepo zokumana nazo zachidule za pamalopo.

Nyimbo Na. 164 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 24

Nyimbo Na. 126

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Pendani “Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.”

Mph. 15: Fotokozani mwachidule za kufunika kwa kupanga maulendo obwereza: Mbali yaikulu ya ntchito yathu yophunzitsa imachitidwa pamene tibwerera kukakulitsa chikondwerero. Ndi anthu oŵerengeka chabe amene angapite patsogolo mwa kuŵerenga buku pa iwo okha. Pamene tilephera kubwerera, timaphonya mwaŵi wathu wabwino kwambiri wa kuwathandiza. Maulendo obwereza amatulutsa maphunziro a Baibulo. Ofalitsa ambiri akhala ndi zotulukapo zabwino koposa mwa kubwereranso patapita tsiku limodzi kapena masiku aŵiri m’malo mwa kuyembekezera mlungu wonse kutha.—Onani buku la Uminisitala Wathu, masamba 88-9.

Mph. 20: Zosoŵa za pamalopo. Kapena kambani nkhani yamutu wakuti “Kusonyeza Chikondi Chachikristu kwa Okalamba,” yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya August 1, 1994, masamba 27-30.

Nyimbo Na. 169 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 31

Nyimbo Na. 136

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Tchulani mmene mpingo ukuchitira pa mkupiti wapadera wa buku la Moyo wa Banja. Mbiri Yateokrase.

Mph. 15: “Khalani Womangirira.” Kukambitsirana ndiponso nkhani yokambidwa ndi mkulu.

Mph. 20: Kambitsiranani za Buku Logaŵira mu August. Tchulani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha limene lingagaŵiridwe. Pemphani ofalitsa kusimba zokumana nazo zilizonse zimene anakhala nazo pogaŵira buku limeneli m’June. Sonyezani chitsanzo cha mmene mungayambire phunziro la Baibulo mwa kugwiritsira ntchito buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Funsani funso lofunsidwa m’ndime yoyamba ya mutu 11. Pemphani mwininyumba kukambapo zimene akuganiza pa malingaliro osonyezedwa m’ndime 2-4. Fotokozani kuti bukuli limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ndiye anayambitsa kuipa, koma Yehova wakulola kupitiriza chifukwa cha nkhani yofunika imene iyenera kuthetsedwa. Muuzeni kuti mudzabweranso kudzakambitsirana zowonjezereka.

Nyimbo Na. 179 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena