Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 27, 2012. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo ikuyenera kukambidwa n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. Kodi n’zolondola kunena kuti chifundo cha Yehova chimachepetsa chilungamo chake? (Yes. 30:18) [Jan. 9, w02 3/1 tsa. 30]
2. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa kuchotsedwa ntchito kwa Sebina monga woyang’anira nyumba? (Yes. 36:2, 3, 22) [Jan. 16, w07 1/15 tsa. 8 ndime 6]
3. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya pa Yesaya 37:1, 14-20 yokhudza kuthana ndi mavuto? [Jan. 16, w07 1/15 tsa. 9 ndime 1-2]
4. Kodi fanizo limene lili pa Yesaya 40:31 limalimbikitsa bwanji atumiki a Yehova? [Jan. 23, w96 6/15 tsa. 10-11]
5. Kodi mawu a Yehova opezeka pa Yesaya 41:14 ndi olimbikitsa makamaka masiku ano, pomwe tikuyembekezera kuukiridwa kotani? [Jan. 23, ip-2 tsa. 24 ndime 16]
6. Kodi tingamusonyeze bwanji Yehova kuti ‘tikufunafuna chilungamo’? (Yes. 51:1) [Feb. 6, ip-2 tsa. 165 ndime 2]
7. Kodi “ambiri” amene akutchulidwa pa Yesaya 53:12 ndi ndani ndipo tikuphunzira mfundo yolimbikitsa iti pa mmene Yehova amachitira ndi anthu amenewa? [Feb. 13, ip-2 tsa. 213 ndime 34]
8. Kodi anthu a Yehova akhala akukumana ndi zotani m’masiku omaliza omwe anawafotokoza mophiphiritsira pa Yesaya 60:17? [Feb. 20, ip-2 tsa. 316 ndime 22]
9. Kodi “chaka cha Yehova chokomera anthu mtima” chimene Yesu ndi otsatira ake analamulidwa kulengeza ndi chiyani? (Yes. 61:2) [Feb. 20, ip-2 tsa. 324 ndime 7-8]
10. Kodi mawu a pa Yesaya 63:9 akusonyeza khalidwe lalikulu liti la Yehova? [Feb. 27, w03 7/1 tsa. 19 ndime 22-23]