Ndandanda ya Mlungu wa March 5
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 5
Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 3 ndime 1-3 ndi mabokosi pamasamba 23 mpaka 27 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 1-4 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 3:14-25 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Timanyadira Kudziwika Ndi Dzina la Yehova?—Yes. 43:12 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kuthetsa Banja ndi Kukwatiranso?—rs tsa. 386 ndime 1-tsa. 387 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Pindulani Ndi Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2012. Kambani nkhani mwachidule pogwiritsa ntchito mawu oyamba a m’kabukuka. Kenako pemphani omvera kuti afotokoze nthawi imene amawerenga lemba la tsiku ndiponso mmene apindulira. Pomaliza, kambiranani lemba la chaka cha 2012.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa March. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, fotokozani nkhani zochepa zimene zili m’magaziniwo zimene zingakhale zothandiza m’gawo la mpingo wanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo, mungachitenso zimenezi ndi nkhani imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero