Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March ndi April: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba. May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati pakufunikira, gawira kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?
◼ Nkhani ya onse yapadera imene idzakambidwe mlungu wotsatira, Chikumbutso chitachitika, ili ndi mutu wakuti, “Kodi Mapeto Ayandikiradi?”
◼ Ngati mukukonza zokacheza kudziko lina limene silinaikidwe pam’ndandanda wa mayiko palipoti la chaka chautumiki la posachedwapa mu Utumiki Wathu wa Ufumu, chonde funsani kaye ku ofesi yanu ya nthambi kuti mutsimikizire zinthu zofunika kusamala kapena malangizo ena aliwonse amene mungafunike kutsatira. N’kutheka kuti ntchito yolalikira za Ufumu m’dziko limenelo ndi yoletsedwa. (Mat. 10:16) M’mayiko ena, sizingakhale bwino kuti alendo akumane ndi Mboni za m’dzikolo kapena kukasonkhana ndi mipingo ya kumeneko. Mungapatsidwenso malangizo ena okhudza kulalikira mwamwayi kapena kutenga mabuku athu popita kumayiko amenewa. Kutsatira malangizo amenewa kudzathandiza kuti mupewe mavuto amene mungakumane nawo ndiponso amene angalepheretse ntchito ya Ufumu m’dziko limene mukufuna kupitakolo.—1 Akor. 14:33, 40.