Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa March
“Anthu ambiri amakondwerera kubadwa kwa Yesu. Kodi mukuganiza kuti n’zofunikanso kuti tizikumbukira imfa yake?” Yembekezani ayankhe. Kenako m’patseni mwininyumbayo Nsanja ya Olonda ya March 1 ndipo werengani ndi kukambirana nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi lokha. Kenako, konzani zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda March 1
“Masiku ano pali matchalitchi ndiponso zipembedzo zambiri zimene zimachita ndiponso kukhulupirira zinthu zosiyanasiyana. Kodi mukuganiza kuti Akhristu enieni tingawadziwe bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Malinga ndi zimene Yesu ananena, pali chizindikiro chimodzi chokha chodziwira Akhristu oona. [Werengani Yohane 13:34, 35.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zisanu zimene Yesu ananena zotithandiza kuzindikira otsatira ake enieni.”
Galamukani! March
“Lero tikucheza ndi anthu osiyanasiyana za khalidwe limene limasokoneza mtendere. Zikuoneka kuti masiku ano anthu akungokhala okwiya ndiponso sachedwa kupsa mtima. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chikuchititsa zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kupsa mtima. [Werengani Salimo 37:8.] Magazini iyi ikufotokoza zinthu zina zimene zikuchititsa kuti anthu azipsa mtima ndiponso zimene tingachite kuti tipewe kupsa mtima.”