Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa August
“Anthu ali m’zipembedzo zosiyanasiyana ndipo amapembedza Mulungu m’njira zosiyanasiyananso. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamva bwanji ndi zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu anaphunzitsa pa nkhani imeneyi.” M’patseni mwininyumba Nsanja ya Olonda ya August 1, ndiyeno kambiranani zimene zili pansi pa kamutu koyamba patsamba 16 komanso werengani lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Gawirani magaziniwo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda August 1
“Kodi ana ayenera kuphunzitsidwa za Mulungu ali aang’ono, kapena ndi bwino kuyembekezera kaye kuti akule kenako adzasankhe okha chipembedzo chawo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limalangiza bambo kuti azichita. [Werengani Aefeso 6:4.] Magazini iyi ili ndi mfundo zothandiza za mmene makolo angaphunzitsire ana awo nkhani za Mulungu.”
Galamukani! August
“Ndikufuna kudziwa maganizo anu pa zimene lemba ili limanena. [Werengani 1 Samueli 16:23.] Malinga ndi zimene lembali likunena, nyimbo ndi zamphamvu kwambiri. Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kuti nyimbo zina zikhoza kusokoneza munthu? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mmene tingasankhire nyimbo mwanzeru ndiponso mmene tingathandizire ana athu kuchita chimodzimodzi.”