Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa August
“Pafupifupi munthu aliyense amapemphera nthawi zina. Ngakhale anthu omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu nthawi zina akakhala pa mavuto amapemphera. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amayankha mapemphero onse?” Yembekezani ayankhe. Musonyezeni nkhani imene ili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya August 1, 2013, ndipo kambiranani ndime imene ili pansi pa funso loyamba komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimeyo. Mugawireni magaziniyo ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Dziwani izi: Mudzachite chitsanzochi pa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda pa August 3.
Nsanja ya Olonda August 1
“Masiku ano anthu ambiri akuda nkhawa chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zolaula, zomwe zikupezeka paliponse. Komabe anthu enanso ambiri amaona kuti kuonera zolaula kulibe vuto lililonse. Inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Yesu ananena kuti tingathe kudziwa ngati chinthu chili chabwino kapena ayi poona zipatso zake. [Werengani Mateyu 7:17.] Magazini iyi ikufotokoza mavuto omwe anthu amene amaonera zolaula amakumana nawo. Ilinso ndi malangizo othandiza kwa munthu amene akufuna kusiya kuonera zolaula.”
Galamukani! August
“Ambirife timafuna kukhala ndi moyo wautali. Kodi mukuganiza kuti kupita patsogolo kwa sayansi kungathandize kuti zimenezi zitheke? [Yembekezani ayankhe.] Taonani lonjezo losangalatsa ili. [Werengani 1 Akorinto 15:26.] Koma kodi Mulungu adzakwaniritsa bwanji lonjezo limeneli? Kodi adzagwiritsa ntchito sayansi kapena pali njira ina? Komanso n’chifukwa chiyani anthufe timakalamba ndiponso kufa? Magaziniyi ili ndi mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa.”