Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa July
“M’zaka zaposachedwapa, anthu akhala akukamba kwambiri nkhani za angelo. Kodi mukuganiza kuti angelo ndi enieni? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena pa nkhaniyi.” M’patseni Nsanja ya Olonda ya July 1 ndipo mukambirane naye mfundo zimene zili pa kamutu koyamba patsamba 16. Komanso muwerenge lemba ngakhale limodzi lokha pa malemba amene akupezeka pa kamutu koyambaka. Mugawireni magaziniyo n’kupangana naye tsiku limene mudzayankhe funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda July 1
Werengani Salimo 65:2. Kenako munene kuti: “Anthu ambiri amavomereza kuti Mulungu ndi ‘Wakumva pemphero,’ ndipo amapemphera tsiku lililonse. Koma anthu ena amadabwa kuti, ‘Ngati kuli Mulungu, n’chifukwa chiyani dziko lapansili lili ndi mavuto ambirimbiri chonchi?’ Inu mukuganiza bwanji? Kodi Mulungu amamvadi mapemphero athu? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena poyankha funso lakuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amene amamva mapemphero athu amalola kuti tizivutika?’”
Galamukani! July
“Ngati mutapatsidwa mwayi woti musinthe zinazake padzikoli, kodi mungasinthe chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limafotokoza chimene chimachititsa kuti tizilephera kukwaniritsa zimene timafuna. [Werengani Yeremiya 10:23.] Magazini iyi ikufotokoza zinthu zimene Mulungu akufuna kusintha.”