Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/13 tsamba 8
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 6/13 tsamba 8

Zitsanzo za Ulaliki

Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa July

“Pafupifupi munthu aliyense angakonde kukhala ndi moyo wautali komanso wosangalala. Ndiye ndikufuna kumva maganizo anu pa funso ili: Kodi mukuganiza kuti tsiku lina padzapezeka anthu asayansi kapena mankhwala amene angathandize anthu kuti azikhala ndi moyo wosatha? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena.” Musonyezeni nkhani imene ili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya July 1, 2013, ndipo kambiranani ndime imene ili pansi pa funso loyamba komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimeyo. Mugawireni magaziniyo ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.

Dziwani izi: Mudzachite chitsanzochi pa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda pa July 6.

Nsanja ya Olonda July 1

“Anthu ambiri amene timakumana nawo, ali ndi zipembedzo zawo. Koma ena amanena kuti alibenso chidwi ndi chipembedzo chilichonse. Kodi inuyo mumaona bwanji?” [Yembekezani ayankhe.] Yesu anatiuza zimene zingatithandize kudziwa chipembedzo chabwino. [Werengani Luka 6:44a.] Magazini iyi ikufotokoza zipatso zina zoipa zimene zipembedzo zimatulutsa. Ilinso ndi yankho la funso lakuti, Kodi pali chipembedzo chimene mungachikhulupirire?”

Galamukani! July

“Tikucheza ndi anthu m’dera lino kukambirana nawo za vuto la kupanda chilungamo. Anthu ena amachita zionetsero chifukwa chosakondwa ndi zinthu zopanda chilungamo zimene zili m’dzikoli. Koma kodi mukuganiza kuti zimenezi zimathandizadi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likunena kuti n’zomwe zidzabweretse mtendere padzikoli. [Werengani Mateyu 6:9, 10.] Magazini iyi ikuyankha funso lakuti, Kodi zionetsero zimathetsadi mavuto m’dziko?”

Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu

“Tikucheza ndi anthu m’dera lanu lino ndipo tikukambirana nawo mfundo imodzi yosangalatsa yochokera m’Baibulo. Anthu ambiri amene takumana nawo amadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu yemwe ndi wachikondi, amalola kuti anthufe tizivutika? Kodi mukuganiza kuti Mulungu polenga anthu anakonzeratu kuti azivutika?” Yembekezani ayankhe. Ndiyeno pitani pa Phunziro 5, ndipo werengani ndi kukambirana ndime ziwiri zoyambirira komanso malemba amene awadetsa. Agawireni kabukuko ndipo konzani zoti mudzabwerenso kudzakambirana funso lotsatira lomwe lili ndi mawu akuda.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena