Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa July
“Anthu ambiri amanena mobwerezabwereza mawu a m’Pemphero la Ambuye akuti: ‘Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.’ Kodi mukuganiza kuti Ufumu umenewo n’chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Lemba ili la m’Baibulo lingatithandize kupeza yankho.” Werengani Danieli 2:44. Kenako m’patseni Nsanja ya Olonda ya July 1 ndipo werengani ndi kukambirana naye nkhani imene ili pakamutu koyamba patsamba 16. M’gawireni magaziniyo n’kukonza zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda July 1
“Chifukwa chakuti moyo ndi waufupi komanso wamavuto okhaokha, anthu ambiri amadzifunsa kuti kodi cholinga chokhalira ndi moyo n’chiyani? Kodi inuyo munadzifunsapo funso limeneli? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatilonjeza kuti moyo supitiriza kukhala wotere mpaka kalekale. [Werengani Chivumbulutso 21:4.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu analengera dziko lapansi komanso zinthu zina zimene tingachite kuti tikhale ndi moyo wabwino ngakhale panopa.”
Galamukani! July
Tchulani tsoka lodziwika kwambiri limene langochitika kumene. Kenako funsani kuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zinthu zotere zizichitika? [Yembekezani ayankhe.] Malinga ndi zimene Baibulo limanena, Mulungu amamvera chisoni anthu amene akuvutika. [Werengani Ekisodo 3:7.] Baibulo limatiuzanso chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika ndiponso kuti posachedwapa athetseratu mavuto onse. Magazini iyi ikufotokoza zimenezi.”