Zitsanzo za Ulaliki
Kuti Muyambitse Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa May
“Kodi munadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika ndiponso kuti anthu azivutika? [Yembekezani ayankhe.] Ndikufuna ndikusonyezeni mfundo yosangalatsa pa nkhani imeneyi.” Kenako werengani limodzi zimene zili pakamutu koyamba patsamba 16 mu Nsanja ya Olonda ya May 1 ndiponso lemba limodzi limene laikidwa pamenepo. Mukatero apatseni magaziniyo ndipo mupangane zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane yankho la funso lotsatiralo.
Nsanja ya Olonda May 1
Werengani Salimo 37:10, 11. Ndiye funsani kuti: “Kodi mukuganiza kuti lonjezo limeneli likwaniritsidwa posachedwapa? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza maulosi 6 a m’Baibulo amene akukwaniritsidwa panopo. Maulosi amenewa akusonyeza kuti lonjezo tawerengali latsala pang’ono kukwaniritsidwa.”
Galamukani! May
“Anthu ena amanena kuti anthufe tinachokera ku nyama. Inu mumaganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Salimo 139:14.] Wolemba Masalimoyu sankadziwa zinthu zambiri zodabwitsa zokhudza thupi la munthu ayi. Magazini iyi ikufotokoza zimene zikudziwika panopo ndiponso zimene zimatisiyanitsa ndi nyama.”