Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati munthu ali ndi chidwi, m’patseni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo kwa munthuyo. June: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli ndipo sakufuna phunziro la Baibulo, mungamupatse magazini yakale kapena kabuku kalikonse kamene kangamuthandize. July: Gawirani timabuku tamasamba 32 timene anthu angachite nato chidwi m’gawo lanu, monga: Dikirani!, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani?, Kodi Iyo Ilikodi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! ndiponso kakuti, Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano
◼ Kuyambira mwezi wa May, Loweruka loyamba la mwezi uliwonse lidzakhala tsiku loyambitsa maphunziro a Baibulo. Choncho, mipingo yonse iziyesetsa kuyambitsa maphunziro pa tsikuli. Nkhani za mu Nsanja ya Olonda za mutu wakuti, “Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena,” zakonzedwa kuti zitithandize kuyambitsa maphunziro. Kumapeto kwa Utumiki Wathu wa Ufumu kuzikhala zitsanzo za ulaliki umene tingagwiritsire ntchito mwezi wotsatira. Kuzikhalanso zimene tinganene pofuna kuyambitsa phunziro la Baibulo pa Loweruka loyambirira.