Zimene Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda March 1
“Anthu amasiyana maganizo pa nkhani ya Yesu. Kodi inu mumaona kuti Yesu ndi mwana wa Mulungu kapena ndi munthu wabwino basi?” Yembekezerani ayankhe. Kenako werengani limodzi zimene zalembedwa m’munsi mwa funso lakuda kwambiri patsamba 16 ndi 17 ndiponso lemba limodzi limene lili pamenepo. Ndiyeno mugawireni magazini n’kukonza zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Galamukani! March
Mukakumana ndi wachinyamata, musonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 26. Musonyezeni kamutu koyamba n’kumufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti izi ndi zoona kapena ndi zabodza? [Yembekezerani ayankhe. Kenako werengani 2 Akorinto 7:1.] Nkhani iyi ikufotokoza zimene uyenera kudziwa pa nkhani yosuta fodya ndiponso zimene munthu angachite kuti asiye kusuta.”
Nsanja ya Olonda April 1
“Anthu ambiri ali ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana zonena za Yesu. Kodi mukuganiza kuti n’zofunikadi kudziwa zoona za Yesu? [Yembekezerani ayankhe. Kenako werengani Yohane 17:3.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena za Yesu. Ikufotokozanso kumene anachokera, moyo umene anakhala, ndiponso chifukwa chake anafa.”
Galamukani! April
“Kodi mukuvomereza kuti kumwalira kwa munthu amene timam’konda ndi nkhani yovuta kwambiri imene anthufe timakumana nayo pa moyo wathu? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ambiri aona kuti malangizo awa ndi othandiza. [Werengani Salimo 55:22.] Magazini iyi ikufotokoza njira zina zothandiza kulimbana ndi chisoni, komanso mmene tingatulire nkhawa zathu kwa Mulungu.”