Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Kuyambira pa December 13, 2010 mpaka pa January 9, 2011, m’Malawi muno mwakhala mukuchitika Sukulu za Utumiki wa Ufumu zokwana 54 za akulu ndi atumiki othandiza. Akulu oposa 5,500 ndi atumiki othandiza okwana 4,900 apindula ndi maphunziro amenewa. Zimenezi zichititsa kuti mipingo imene abale amenewa akutumikiramo ipindule. Kunena zoona, atate wathu wachikondi Yehova amasamaliradi anthu ake.