Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda March 1
Werengani Eksodo 20:15. Ndiyeno nenani kuti: “Anthu ambiri amayesetsa kutsatira lamulo limeneli, koma ena amaona kuti zinthu zikavuta kwambiri, sikulakwa kuba kapena kuchita zinthu zina zachinyengo. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Nkhaniyi ikufotokoza chifukwa chake ndi bwino kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse.” M’sonyezeni nkhani imene yayambira patsamba 12.
Galamukani! March
“Anthu ambiri amalemekeza Baibulo, komabe amaona kuti mfundo zake zambiri n’zachikale ndipo n’zosathandiza masiku ano. Kodi inuyo mumaona bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Aroma 15:4.] Nkhaniyi ikufotokoza chifukwa chake mbali zina za Baibulo, ngakhale zakale kwambiri, zilili zothandiza kwambiri masiku ano.” M’sonyezeni nkhani yomwe yayambira patsamba 28.
Nsanja ya Olonda April 1
“Anthu ambiri akafunsidwa kuti atchule munthu wotchuka kwambiri m’mbiri yonse, amayankha kuti ndi Yesu. Kodi inunso mumaona choncho? [Yembekezani ayankhe.] Onani chifukwa chake tiyenera kufufuza zoona zenizeni za Yesu kuti tidziwe choonadi. [Werengani Yohane 17:3.] Nsanja ya Olonda iyi, yomwe ndi magazini yapadera ikusonyeza zoona zenizeni zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu ndiponso zimene ankaphunzitsa.”
Galamukani! April
“Zikuoneka kuti tili ndi nthawi yochepa yochitira zinthu zonse zimene timalakalaka titachita. Kodi inunso mukuona choncho? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri aona kuti malangizo awa ndi othandiza. [Werengani Afilipi 1:10.] Magazini iyi ili ndi mfundo zothandiza kuti tizigwiritsa tchito nthawi mwanzeru.”