Ndandanda ya Mlungu wa April 12
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 12
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 19-22
Na. 1: 1 Samueli 21:1-9
Na. 2: Kodi Tiyenera Kuona Motani Zinthu Zimene Yehova Amadana Nazo? (Miy. 6:16-19)
Na. 3: Kodi Tiyenera Kutsatira Mfundo Ziti pa Nkhani ya Zikondwerero Zilizonse? (rs tsa. 241 ndime 4–tsa. 242 ndime 3)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Afikeni Omvera Anu Pamtima Mwa Kuwalimbikitsa Kulingalira. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, kuyambira patsamba 58 ndime 3, mpaka kumapeto kwa kamutu patsamba 59.
Mph. 20: “Kopani Chidwi Pophunzitsa.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana ndime 4, pemphani mpainiya kuti achite chitsanzo cha mmene tingayambire phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo agwiritse ntchito mfundo za m’nkhani ino.