Kopani Chidwi Pophunzitsa
1. Kodi kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mokopa mu utumiki kumaphatikizapo chiyani?
1 Aphunzitsi aluso, monga mtumwi Paulo, amadziwa kuti ‘kulondoloza bwino mawu a choonadi’ kumafuna zambiri osati kungotchula mawu okha a m’Malemba Oyera. (2 Tim. 2:15) Pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, kodi tingatani kuti ‘tikope’ chidwi pophunzitsa?—Mac. 28:23.
2. Kodi mungatani kuti muthandize anthu kulemekeza Mawu a Mulungu?
2 Sonyezani Omvera Anu Zimene Mawu a Mulungu Amanena: Choyamba, awerengereni zimene Baibulo likunena n’cholinga choti azililemekeza kuti ndi Mawu a Mulungu. Tikamadalira kwambiri Mawu a Mulungu, nawonso omvera athu amamvetsera mwachidwi tikamawerenga malemba. (Aheb. 4:12) Tikamakambirana ndi munthu Mawu a Mulungu, tinganene kuti: “Ndikuona kuti kuyendera maganizo a Mulungu pankhaniyi n’kothandiza. Taonani zimene Mawu ake akunena.” Ngati n’kotheka, muziyesetsa kuwerenga Baibulo kuti omvera anu aone zimene Mawu a Mulungu akunena.
3. Mukawerenga lemba, kodi mungatani kuti muthandize omvera anu kumvetsa mfundo ya lembalo?
3 Chachiwiri, fotokozani lemba limene mwawerenga. Anthu ambiri akangowerenga vesi koyamba zimawavuta kumvetsa tanthauzo lake. Choncho, tiyenera kufotokoza mfundo ya lembalo. (Luka 24:26, 27) Tsindikani mawu ofunika palembalo amene akugwirizana ndi zimene mukukambirana. Kuwafunsa funso kungathandizenso kuti mudziwe ngati omvera anu amvetsa mfundo ya lembalo.—Miy. 20:5; Mac. 8:30.
4. Kodi ndi mfundo yomaliza iti imene ingathandize kuti tikope chidwi cha anthu pophunzitsa?
4 Fotokozerani Malemba: Chachitatu, yesetsani kuti muwafike pamtima omvera anu. Thandizani eninyumba kuti aone mmene lembalo lingawathandizire paokha. Kufotokozera malemba kungathandize munthu kusintha maganizo ake. (Mac. 17:2-4; 19:8) Mwachitsanzo, mukawerenga Salmo 83:18, fotokozani mmene kudziwa dzina la munthu winawake kulili kofunika kuti mukhale naye paubwenzi wabwino. Ndiyeno, m’funseni kuti, “Kodi mukuganiza kuti kudziwa dzina la Mulungu kungathandize kuti mapemphero anu azikhala ogwira mtima?” Kugwirizanitsa lembalo ndi moyo wa munthuyo, kungamuthandize kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundozo pamoyo wake. Kukopa chidwi cha anthu pophunzitsa mwa kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kumapangitsa anthu oona mtima kuyamba kulambira Yehova, yemwe ndi Mulungu woona ndiponso wamoyo.—Yer. 10:10.