Kodi Mumadalira Mawu a Mulungu?
1 Akhristu oona amalimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwakhama ngakhale kuti m’dzikoli anthu ambiri amanyoza Baibulo. Chifukwa choti sitikayika ngakhale pang’ono kuti “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu,” timagwirizana ndi mfundo imene Yesu Khristu anatchula m’pemphero yakuti: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (2 Tim. 3:16; Yoh. 17:17) Kodi tingatani kuti tizilimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu?
2 Dziwani Malemba: N’zosakayikitsa kuti Yesu anachita khama pophunzira Mawu a Mulungu. Zimenezi zinam’thandiza kuti aziphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito Malemba pautumiki wake wonse. (Luka 4:16-21; 24:44-46) Kodi tingatani kuti tizitha kukumbukira malemba ambiri ofunikira? Tingatero powerenga Baibulo tsiku lililonse, kenaka n’kusinkhasinkha lemba limene tikuona kuti n’lolimbikitsa kapena n’lothandiza kwambiri muutumiki. Tikamakonzekera misonkhano tiziwerenga m’Baibulo malemba onse osagwidwa mawu ndipo tiziyesetsa kupeza ndemanga yoti tikanenepo. Tikakhala pa misonkhano, tizitsegula malemba onse amene okamba nkhani akuwerenga. Kudziwa malemba a m’Baibulo kungatithandize ‘kulondoloza bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15.
3 Baibulo Lizilankhula Lokha: Tikalowa mu utumiki tizililola Baibulo kulankhula lokha. Mwachitsanzo, ngati n’zotheka tiziyesetsa kuwerengera mwininyumba ngakhale lemba limodzi chabe. Ngati atatifunsa mafunso enaake kapena akatsutsa mfundo inayake ndibwino kumuyankha pogwiritsira ntchito Baibulo. Mwininyumbayo akakhala wotanganidwa, n’zotheka ndithu kumusonyeza mfundo inayake ya m’Baibulo ponena kuti: “Ndisanapite, ndiloleni kuti ndingokuwerengerani lemba ili basi.” Ngati zingatheke werengani lembalo kuchokera m’Baibulo ndipo mwininyumbayo aziona pamene mukuwerengapo.
4 Mwininyumba wina atasonyezedwa Malemba otsutsa chiphunzitso cha Utatu, anadabwa n’kunena kuti: “Ndakhala ndikupita ku tchalitchi kwa moyo wanga wonse, koma ndithu, sindinamvepo kuti Baibulo limatchula mfundo imeneyi.” Iye anavomera kuti Mboni ziziphunzira naye Baibulo. Yesu anati nkhosa zake zimamva mawu ake. (Yoh. 10:16, 27) Ndiyetu njira yabwino yothandizira anthu oona mtima kuzindikira choonadi ndiyo kuwalola kuti aone okha choonadicho m’Malemba. Motero tiyeni tiyesetse kudalira kwambiri Mawu a Mulungu a choonadi polalikira.