Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira May 14
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, kusonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya May 15 ndi Galamukani! ya May. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa, gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.20: Kupereka Chithandizo pa Ntchito ya Ufumu Kwanuko ndi Padziko Lonse. Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 12.
Mph.15: “Iye Alimbitsa Olefuka.”a Malingana ndi nthawi imene muli nayo, pemphani omvetsera kuthirirapo ndemanga pa malemba amene asonyezedwawo.
Nyimbo Na. 1 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 21
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani mwachidule Bokosi la Mafunso.
Mph.15: Ndandanda ya Banja Yochitira Phunziro la Banja. Nkhani yochokera mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2005, tsamba 5. Fotokozani kufunika kochititsa phunziro la banja logwira mtima.
Mph.20: “Kodi Mumadalira Mawu a Mulungu?”b Phatikizanipo ndemanga zochokera m’mabokosi amene ali pa tsamba 143 ndi 144 m’buku la Pindulani.
Nyimbo Na. 202 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 28
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa May. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa, gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.20: Gawirani buku la Chimwemwe cha Banja m’mwezi wa June. Tchulani mbali zina za bukuli zomwe zili zoyenerera kwambiri panthawi ino, ndipo khalani ndi zitsanzo za mmene tingagawire bukuli. Zitsanzozo zikhale zogwirizana kwambiri ndi kwanuko. Malingana ndi nthawi imene muli nayo, pemphani omvetsera kuti anene mmene apindulira ndi bukuli pokambirana ndi anzawo komanso achibale awo.
Mph.15: Zokumana Nazo. Fotokozani zinthu zimene apainiya othandiza komanso ofalitsa akumana nazo pantchito yaikulu imene achita muutumiki m’miyezi ya March, April, ndi May. Fotokozaninso zimene akumana nazo onse amene anabwerera kwa anthu amene anagawirako magazini, n’cholinga chokayambitsa phunziro la Baibulo. Mungathe kuchita chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosangalatsa kwambiri cha zimene zinachitikadi.
Nyimbo Na. 21 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 4
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Phunzitsani Ana Anu Kutamanda Yehova.”c Pokambirana ndime 4, phatikizanipo ndemanga zochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 2005, tsamba 3.
Nyimbo Na. 169 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.