Mmene Mungakonzekerere Kugawira Magazini
1. Kodi n’chifukwa chiyani timafunikira kukonzekera ulaliki wathuwathu wogawira magazini m’malo mongoloweza chitsanzo cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu?
1 Mwina mungafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani timafunikira kukonzekera ulaliki wogawira magazini pamene mu Utumiki Wathu wa Ufumu uliwonse mumakhala kale zitsanzo za zomwe tinganene pogawira magazini?’ Ngakhale kuti ambiri aona kuti zitsanzo zimenezi n’zothandiza, m’pofunikabe kukonzekera patokha. Ulaliki umene ungakhale wogwira mtima m’gawo limodzi, ungathe kukhala wosathandiza kwenikweni m’gawo lina. Choncho, tisakakamizike kugawira magazini potsatira ndendende mawu a m’zitsanzo zimene tapatsidwa. Ngakhale titasankha kugwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe tapatsidwa, m’pofunikabe kunena mfundozo m’mawu athuathu.
2. Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kusankha nkhani imene mudzafotokoze pogawira magazini?
2 Sankhani Nkhani: Mukawerenga magazini, sankhani nkhani yomwe ndi yoyenerera m’gawo lanu komanso yomwe yakusangalatsani kwambiri. Mwininyumba adzakhala ndi chidwi chofuna kuwerenga nkhani imene mukufotokoza ngati akuona kuti mukukhulupiriradi zimene mukunena ndipo mukuzikamba kuchokera mumtima. Ngakhale kuti nthawi zambiri muzifotokoza ndi kusonyeza nkhani zimene anthu ambiri angasangalale nazo m’gawo lanu, ndi bwino kuwerenga ndi kumvetsanso nkhani zina zonsezo. Zimenezi zingakuthandizeni kusintha ulaliki wanu ngati mwapezana ndi munthu amene angasangalale kwambiri ndi nkhani zina.
3. Kodi mumagwiritsa ntchito mawu oyamba otani kuti ulaliki wanu ukhale wogwira mtima?
3 Funsani Funso: Kenako konzekerani bwino mawu anu oyamba. Mawu anu oyamba ndi ofunikira kwambiri. Zingakhale zothandiza kufunsa mwininyumba funso loti aliganizire n’cholinga choti achite chidwi ndi nkhani imene mwasankha kumusonyeza. Mafunso ofuna kuti munthuyo apereka maganizo ake ndi amene amakhala bwino kwambiri. Pewani kufunsa zinthu zimene zingam’chititse mwininyumba manyazi kapena zimene zingabutse mkangano.
4. Ngati mwininyumba ali ndi mpata, kodi ubwino womuwerengera lemba n’ngotani?
4 Werengani Lemba: Pomaliza, sankhani lemba limene mungakawerenge ngati mwininyumba ali ndi mpata, mwina limene lili m’nkhani imene mukufuna kukamusonyeza. Kuwerenga lemba kungathandize mwininyumba kuona kuti uthenga wanu ukuchokera m’Mawu a Mulungu. (1 Ates. 2:13) Komanso kuwerenga lemba kudzam’patsa umboni ngakhale atakana kulandira magazini. Pofuna kuti mwininyumba achite chidwi, ena amayamba kuwerenga lemba asanafunse funso. Musanawerenge lemba munganene kuti, “Ndikufuna kumva maganizo anu pa vesi ili.” Kenaka werengani naye mfundo zogwirizana ndi lembalo m’magaziniyo, ndi kunena mawu angapo ochititsa chidwi musanam’patse magaziniyo.
5. Kodi muyenera kuganizira mfundo zofunika ziti mukamakonzekera ulaliki wa magazini?
5 Palibe malamulo okhwima a zomwe munganene pogawira magazini. Komabe, ndi bwino kuti ulaliki wanu uzikhala wosavuta kumva ndi waufupi. Sankhani ulaliki wosavuta kwa inu komanso umene ungakhale ndi zotsatirapo zabwino. Atsimikizireni anthuwo kuti magazini athu ndi othandiza kwambiri, ndipo lankhulani mochokera mumtima. Ngati mutakonzekera bwino mudzatha kugawira mosavuta magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anthu amene ali ndi “maganizo oyenerera moyo wosatha.”—Mac. 13:48.