Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Maulaliki
1. Kodi zitsanzo za maulaliki zimene timapatsidwa tiyenera kuziona motani?
1 Zitsanzo za maulaliki a mmene tingagawire magazini ndi mabuku ena, nthawi zambiri zimaikidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Tikamalalikira, sitifunika kubwereza mfundo za m’zitsanzo za maulaliki amenewa ndendende monga mmene zalembedwera. Amaziikamo kuti zitipatse chithunzi cha zimene tinganene. Timakhala ogwira mtima kwambiri nthawi zonse ngati tilankhula zimene zili m’zitsanzozo m’mawu athuathu. Kulankhula mwachibadwa kumathandiza mwininyumba kukhala womasuka. Kumaonetsanso kuti zimene tikulankhulazo zikuchokeradi pansi pa mtima ndipo timazikhulupirira.—2 Akor. 2:17; 1 Ates. 1:5.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira miyambo ya kumaloko tikamakonzekera ulaliki?
2 Sinthani Ulaliki Wanu: Kalalikidwe kathu ka uthenga wabwino kamakhudzidwa kwambiri ndi miyambo ya kumene tikukhala. Kodi muyenera kupatsana moni ndi mwininyumba kenako n’kulowetsapo ulaliki pokambirana, kapena anthu a m’gawo lanu amafuna kuti mungofikira kunena zimene mwabwerera? Zimenezi zimasiyanasiyana mogwirizana ndi malo ndipo nthawi zina mogwirizana ndi munthu. Kuzindikira bwino n’kofunikanso ndi mmene timagwiritsira ntchito mafunso. Mafunso abwinobwino m’madera ena, sangawakhalire bwino anthu a m’madera ena. Choncho, timafunika kukhala ozindikira bwino ndiponso otha kusintha ulaliki wathu mogwirizana ndi zimene zili zololeka kumaloko.
3. N’chifukwa chiyani tifunika kuganizira zimene anthu amene timalankhula nawo amakhulupirira ndi mmene amaganizira?
3 Kuwonjezera apo, tikamakonzekera utumiki wa kumunda tifunika kulingalira zimene anthu m’gawo lathu amakhulupirira ndi mmene amaganizira. Mwachitsanzo, mukhoza kukambirana Mateyu 6:9, 10 ndi Mkatolika wodzipereka mosiyana kwambiri ndi munthu amene sadziwa nkomwe za pemphero la “Atate Wathu.” Mwa kulingalira kaye, tikhoza kusintha maulaliki athu kuti akhale osangalatsa kwa anthu amene timakumana nawo mu utumiki.—1 Akor. 9:20-23.
4. N’chifukwa chiyani kukonzekera mokwanira bwino kuli kofunika?
4 Ngakhale pamene tikuganiza zogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki monga mmene chalembedwera, m’pofunikabe kukonzekera mokwanira bwino. Tiyenera kuwerenga mosamala nkhani yonse imene tikufuna kukakambirana ndi anthu ndi kupeza mfundo zimene zili zochititsa chidwi, ndiyeno n’kuziphatikiza mu ulaliki wathu. Ngati tikuzidziwa bwino nkhani zimene zili m’mabuku athu m’pamenenso tidzatha kuwagawira kwa ena mokangalika.
5. N’chifukwa chiyani tingakonzekere ulaliki wina, ndipo tingachite motani zimenezi?
5 Maulaliki Ena: Kodi tizingogwiritsa ntchito maulaliki okhawo amene tapatsidwa osatinso ena? Ayi. Ngati mumatha bwinobwino kugwiritsa ntchito ulaliki winawake kapena lemba lina, gwiritsani ntchito zimenezo. Makamaka pogawira magazini, pezani mipata yogwiritsa ntchito nkhani zina zilizonse za m’kati mwake zimene zingakhale zochititsa chidwi m’gawo lanu. Ngati pa Msonkhano wa Utumiki padzakhala zitsanzo za utumiki wa kumunda, m’poyenera kukonza zitsanzo zosonyeza ulaliki uliwonse wogwira mtima m’gawo lanu. Mwanjira imeneyi aliyense akhoza kuthandizidwa kulalikira uthenga wabwino mogwira mtima.