Gawirani Magazini Amene Amachitira Umboni Choonadi
1. Kodi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi othandiza pantchito yanji?
1 Magazini a Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova ndi Galamukani!, ndi othandiza kwambiri pantchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timasangalala kugawira nthawi zonse magazini awiri a panthawi yake amenewa pamene tikuchita mbali zosiyanasiyana za utumiki wa Ufumu.
2. Kodi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akhala akusintha motani, ndipo chifukwa chiyani?
2 M’kupita kwa zaka taona magaziniwa akusintha kukula kwake, nkhani zake, ngakhalenso njira za kagawiridwe kake. Cholinga cha kusinthaku ndi chakuti magaziniwa akhale ochititsa chidwi komanso ogwira mtima kuti uthenga wa Ufumu uwafike pa mtima ‘anthu onse, napulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.’—1 Tim. 2:4.
3. Kodi magazini tiziwagiritsa ntchito motani muutumiki wathu?
3 M’mbuyo monsemu takhala tikugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pogawira magazini ya Galamukani! yotuluka kamodzi pamwezi. Tsopano tizichitanso zomwezi ndi Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Mwa magazini awiri a Nsanja ya Olonda amene azituluka mwezi ndi mwezi, tizigawira imodzi yokha muutumiki wakumunda. Zitsanzo za kagawiridwe ka magazini iliyonse zimakhala pa tsamba lomaliza la mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Nthawi zambiri zitsanzo zimenezi zimakhala za nkhani zoyambirira za m’magaziniyo, koma nthawi zina pamakhalanso zitsanzo za nkhani zina zomwe anthu ambiri angazikonde. Zitsanzo zimenezi zingakhale zogwira mtima ngati ifeyo taidziwa bwino nkhani yotchulidwa m’chitsanzocho komanso tikagwirizanitsa ulalikiwo ndi gawo lathu.
4. Kodi n’chifukwa chiyani kungakhale kothandiza kugwiritsa ntchito ulaliki wina wosiyana ndi zitsanzo zoperekedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu?
4 Ngakhale kuti Utumiki Wathu wa Ufumu uzikhala ndi zitsanzo ziwiri za magazini iliyonse, muli ndi ufulu wogwiritsa ntchito ulaliki wosiyana kotheratu. Chifukwa chimodzi chochitira zimenezi n’chakuti pangakhale nkhani ina m’magaziniyo imene ingakope anthu ambiri m’gawo lanu. Kapenanso inuyo mungaone kuti mutha kugawira bwino magaziniyo ngati mutagwiritsa ntchito nkhani imene mwaikonda.
5. Tisanakonzekere ulaliki wogawirira magazini, kodi tiyenera kuchita chiyani?
5 Mmene Mungakonzekerere: Choyamba muyenera kuidziwa bwino nkhani imene mukufuna kukaigwiritsa ntchito pogawira magaziniwo. Sinthawi zonse pamene mungamalize kuwerenga nkhani zonse za m’magazini musayambe kuwagawira. Komabe, nkhani imene mwaisankhayo muyenera kuifotokoza mwaumoyo koma mosakokomeza. Kuti muchite zimenezi, muyenera kuidziwa bwino nkhani imene mukufuna kukaifotokozayo.
6. Kodi tingakonzekere bwanji ulaliki wathuwathu?
6 Kenako, konzekerani mawu oyamba osavuta kuwasintha. Mungayambe ndi funso lopatsa chidwi komanso logwirizana ndi nkhani imene mukufuna kusonyeza. Nthawi zonse dalirani mphamvu ya Mawu a Mulungu kuti ndi imene imakhudza mtima wa munthu. (Aheb. 4:12) Muzisankha lemba loyenererana ndi ulaliki wanu, ndipo ndi bwino kutenga lemba lomwe lasonyezedwa kapena kugwidwa mawu m’nkhani imene mukufuna kusonyezayo. Muziganiziranso mmene mungamagwirizanitsire lembalo ndi nkhaniyo.
7. Kodi n’chiyani chimene tingamachite kuti ulaliki wathu uzikhala wabwino kwambiri?
7 Gwiritsirani Ntchito Mpata Uliwonse: Kuti ulaliki umene mwakonzekera ukhaledi waphindu, muyenera kuugwiritsira ntchito. Gawirani magazini limodzi ndi mpingo patsiku Loweruka. Agawireninso kwa anthu amene analandirapo mabuku athu ena. Ndiponso nthawi zonse gawirani magazini kwa ophunzira Baibulo anu ndi anthu enanso amene mungawapeze paulendo wobwereza. Mungathenso kuwagawira kwa anthu amene mungalankhule nawo pamene muli kokagula zinthu, paulendo, kapena podikira chithandizo kuchipatala. M’kati mwa mweziwo, muzikonzanso ulaliki wanu kuti ukhale bwino kwambiri pamene mukuugwiritsira ntchito.
8. Kodi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi apadera chifukwa chiyani?
8 Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi magazini apadera kwambiri. Amalemekeza Yehova monga Mfumu ya chilengedwe chonse. (Mac. 4:24) Amalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso amawathandiza kukhulupirira Yesu Khristu. (Mat. 24:14; Mac. 10:43) Kuwonjezera apo, amaunika mmene zochitika za padziko zikukwaniritsira ulosi wa Baibulo. (Mat. 25:13) Choncho, khalani okonzekera nthawi iliyonse kuthandiza anthu m’gawo lanu kuti apindule ndi magazini amenewa.
9. Kodi tingatani kuti tiyale maziko a ulendo wobwereza?
9 Ngati mwatha kugawira magazini, kapena ngati mwangocheza nkhani yauzimu ndi munthu, konzekerani kufunsa funso kapena kunenapo mawu ena othandiza munthu kuganiza. Zimenezi zingatsegule mpata wa ulendo wobwereza kuti mudzakambiranenso naye nkhani zauzimu. Ngati ndife anthu achangu pofesa mbewu za choonadi, tikhale otsimikiza kuti Yehova adzatsegula mitima ya anthu ofunadi kumudziwa ndi kumutumikira.—1 Akor. 3:6.