Magazini Amalengeza Ufumu
1 Monga Mboni za Yehova, anthu ambiri amatidziŵa chifukwa cha kulalikira kwathu mwachangu za Ufumu wa Mulungu. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amene timafalitsa amachita zamphamvu kuthandiza anthu mamiliyoni kudziŵa za zifuno za Mulungu. Uthenga wake ulidi uthenga wabwino, pakuti umalengeza kuti Ufumu wakumwamba wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu.
2 Nkhani zimene magaziniwo amafotokoza zimakhudzana ndi zosoŵa zenizeni za anthu—za maganizo, chikhalidwe, ndi zauzimu. Popeza makhalidwe abwino ndi mwambo wa banja zikuwonongeka kulikonse, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimathandiza anthu kuwongolera moyo wawo mwa kuwasonyeza mmene angagwiritsire ntchito mapulinsipulo a Baibulo. Zidzakhala zosangalatsa kugaŵira magazini m’April ndi May.
3 Amakopadi: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zili m’zinenero pafupifupi zonse zomwe anthu amalankhula padziko. Chifukwa cha zimenezo, magazini athu ngodziŵika kwambiri. Nazi zifukwa zina zomwe amakopera anthu:
◼ Monga magazini ochirikiza kukhulupirika ndi choonadi, iwo amasonyeza bwino lomwe kusiyana kwa chabwino ndi choipa.
◼ Amapatsa chiyembekezo cha paradaiso wolungama wakudzayo, malinga ndi lonjezo la Mulungu la kudzetsa ulamuliro wa Ufumu wake padziko lapansi.
◼ Amafotokoza nkhani zosiyanasiyana za panthaŵi yake, zimene zimakopa anthu a moyo ndi chikhalidwe zosiyanasiyana.
◼ Nkhani zake nzachidule, zophunzitsa, zoona, ndi zopanda kukondera kapena kululuza zinthu.
◼ Zithunzi zake zokopa zimadzutsa chidwi mwamsanga, ndipo kalembedwe kake kofeŵa kamachititsa kuti magaziniwo akhale osavuta kuŵerenga.
4 Gaŵirani Magazini Ambiri: Kugaŵira magazini ambiri kumadalira makamaka pa khama lathu pokonzekera maulaliki, kulinganiza nthaŵi yathu, ndi ntchito yathu yolalikira. Malingaliro othandiza anaperekedwa mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1995 ndi October 1996, amene angathandize ngati titawaŵerenganso ndi kuwagwiritsira ntchito.
5 Adziŵeni Bwino Magazini: Poŵerenga kope lililonse, lingalirani za wina wake amene angakonde kopelo. Funafunani mfundo zakutizakuti kapena malemba amene mungagwire mawu ake mu ulaliki wanu. Ganizani za funso lomwe mungafunse kuyambitsa makambitsirano ndi kudzutsa chidwi m’nkhaniyo.
6 Sinthani Ulaliki Wanu Malinga ndi Munthuyo: Konzekerani ulaliki wosavuta umene mungasinthe kwa mwamuna, mkazi, munthu wachikulire, kapena wachinyamata, kaya mnansi kapena mlendo.
7 Khalani Atcheru Nthaŵi Zonse Kugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!: Popeza magaziniwo savuta kuloŵa m’chola, chikwama, kapena m’thumba, tinganyamule angapo pamene tili paulendo kapena pokagula zinthu. Agaŵireni polankhula kwa achibale, anansi, anzanu akuntchito, anzanu akusukulu, kapena aphunzitsi. Patulani tsiku mlungu uliwonse kaamba ka umboni wa magazini.
8 Yamikirani Magaziniwo: Iwo samatha phindu lake. Kupita kwa nthaŵi sikumachepetsa kufunika kwa uthenga umene ali nawo. Inde, tikayesetsa ndithu kugaŵira magazini onse amene timaombola, makope akale sadzaunjikana pamashelufu athu.
9 Umboni wa m’Khwalala Umayenda Bwino: Iyi ndi imodzi ya njira zabwino koposa zogaŵira magazini kwa anthu ambiri. Ofalitsa ena nthaŵi zambiri amagwira ntchito m’misewu yokhala ndi anthu ambiri masiku ogula zinthu.
10 Gawo la m’Malo Amalonda Limatulutsa Zabwino: Pochitira umboni kusitolo ndi sitolo, ndi oŵerengeka okha omwe sitiwapeza. Anthu ambiri amalonda ngaulemu, ndipo ambiri amalandira magazini mokondwera. Sonyezani nkhani zoyenerera wamalonda wakutiwakuti amene mwamfikira.
11 Njira za Magazini Zimapereka Mpata Wabwino: Popeza kuti magazini amafalitsidwa kaŵiri pamwezi, zili bwino kupitanso kwa anthu amene amawaŵerenga ndi kuwagaŵira makope otsatira. Tiyenera kupanga maulendo obwereza nthaŵi zonse, osati kungoti tigaŵire magazini komanso kukulitsa chidwi cha munthuyo m’Baibulo. Njira za magazini zimapereka mpata wabwino koposa woyambitsa maphunziro a Baibulo.
12 Gwiritsirani Ntchito Mwaŵi Umene Udzakhalako m’April ndi May: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zakopa mitima ya aŵerengi oyamikira mamiliyoni ambiri. Ali ogwira mtima kwambiri polengeza Ufumu koti tiyenera kutsimikiza kuwanyamula ndi kuwagaŵira pampata uliwonse. Miyezi ya April ndi May ikhale yapadera pogaŵira magazini!