Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
1, 2. Kodi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akhudza bwanji miyoyo ya anthu?
1 “Ndi osangalatsa, apanthawi yake, ndi olimbikitsa.” “Ndi magazini olimbikitsa kwambiri amene sindinawerengepo n’kale lonse.” Ndemanga zimenezi zikufotokoza bwino kwambiri mmene anthu owerenga magazini athu padziko lonse amaonera Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Zoonadi, magazini athu akhala zipangizo zothandiza kwambiri zofikira “anthu onse” ndi uthenga wabwino.—1 Tim. 2:4.
2 Mwamuna wina amene amagwira ntchito anatenga magazini ya Galamukani! chifukwa cha nkhani ina imene inam’sangalatsa kwambiri. Kenako, anawerenganso magazini ya Nsanja ya Olonda imene anatengera limodzi mmene munali nkhani imene inam’pangitsa kupendanso mokhazikika bwino chikhulupiriro chake cha Utatu chimene anali atakhala nacho kwa nthawi yaitali. Izi zinalimbikitsa chidwi chake. Patatha miyezi isanu ndi umodzi anabatizidwa. Mwamuna winanso ankalandira magazini nthawi zonse koma sanali kuwawerenga. Mkazi wakenso naye, ankakana kulankhula ndi Mboni koma ankawerenga magazini aja amene mwamuna wake ankalandira. Kenako anakhudzidwa mtima ndi lonjezo la m’Baibulo lakuti kudzakhala dziko lapansi la paradiso lodzala ndi anthu olungama. M’kupita kwa nthawi, mkaziyo ndi mwana wake wamwamuna, ndiponso mng’ono wake wa mkaziyo anakhala atumiki a Yehova.
3. Kodi ubwino wogawira magazini onse awiri pamodzi ndi wotani?
3 Gawirani Onse Awiri Pamodzi: Monga mmene zitsanzo zapitazi zasonyezera, sitingadziwe amene angakawerenge magazini athu kapena nkhani imene ingadzutse chidwi chawo. (Mlal. 11:6) Pachifukwa chimenechi, ndi bwino kugawira magazini onse awiri pamodzi, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ngakhale kuti pogawira tidzafotokoza za magazini imodzi yokha. M’zochitika zina, kungakhale bwino kugawira mitundu yosiyanasiyana ya magazini athu.
4. Kodi tingakonze bwanji ndandanda yogawira magazini?
4 Kukonza zoti tsiku limodzi mlungu uliwonse muzichita ulaliki wa magazini n’kothandiza kwambiri. Pa Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, anaika Loweruka lililonse kukhala “Tsiku la Magazini.” Popeza kuti timakhala kosiyanasiyana ndiponso kuti zochitika pa moyo zimakhala zosiyanasiyana, ena angasankhe tsiku lina loti azigawira magazini. Kodi pa ndandanda yanu munaikapo tsiku logawira magazini mlungu uliwonse?
5. Kodi ndi mipata iti imene tiyenera kukhala nayo tcheru kuti tigawire magazini, ndipo kodi n’chiyani chingatithandize kuti tithe kuchita zimenezi?
5 Chikhale Cholinga Chanu: Kukhala ndi cholinga choti tizigawira magazini mwezi uliwonse kungatithandize kuti tiziona kufunika kochita zimenezo. Kodi muli ndi anthu amene mumakawapatsa magazini? Kodi anthu amene mumakumana nawo mu utumiki mumawagawira magazini? Kodi mungagawireko magazini mu ulaliki wa mumsewu, m’gawo la malonda, ndi m’malo ena amene mumapezeka anthu ambiri? Kodi mumanyamula magazini mukakhala pa ulendo, mukamapita kokagula zinthu, ndiponso mukamapita ku zochitika zina? Gwiritsani ntchito mpata uliwonse kuthandizira anthu ena kupindula ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
6. Kodi magazini akale tingawagwiritse ntchito bwino motani?
6 Tingakonzenso zogawira magazini akale amene tili nawo kukhala cholinga chathu. Ngakhale magaziniwo akhale kuti atha mwezi umodzi kapena miyezi iwiri musanagawire, nkhani zake zimakhalabe zothandiza kwambiri. Choncho agawireni kwa anthu achidwi. Kwa anthu mamiliyoni ambiri, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akhala ‘mawu . . . a pa nthawi yake.’ (Miy. 25:11) Tiyeni tiwagwiritse ntchito kuthandizira anthu ena mamiliyoni ambiri kuti adziwe Yehova ndi kum’tumikira.