Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 6
Wophunzira Akafunsa Funso
1 Tikangoti takhazikitsa phunziro la Baibulo, nthawi zonse ndi bwino kuphunzira ziphunzitso za m’Baibulo m’ndondomeko yake osati kumadumpha mitu. Zimenezi zimathandiza wophunzira kumanga maziko odalirika odziwa Mawu a Mulungu molondola ndi kupita patsogolo mwauzimu. (Akol. 1:9, 10) Ophunzira nthawi zambiri amafunsa mafunso okhudza nkhani zosiyanasiyana pa nthawi imene tikuphunzira nawo. Kodi tingatani nawo mafunso amenewa?
2 Khalani Wozindikira: Mafunso ogwirizana ndi nkhani imene tikuphunzira panthawiyo tingawayankhiretu nthawi yomweyo. Ngati funsolo nkhani yake ili m’mutu wa kutsogolo m’buku limene tikuphunziralo, kungakhale bwino kumuuza kuti tidzaphunzira zimenezo m’mutu wa kutsogolo. Koma ngati funso lili losagwirizana ndi zimene tikuphunzira panthawiyo kapena n’lofunika kukafufuza kuti tidzaliyankhe momveka bwino, zingakhale bwino kulikambirana pambuyo pa phunzirolo kapena kudzaliyankha nthawi ina. Ena aona kuti kulemba funsolo kumatsimikizira wophunzirayo kuti funso lakelo simukulitenga mopepuka ndipo kumathandiza kuti musasokoneze zimene mukuphunzira panthawiyo.
3 M’mabuku athu ophunzirira, ziphunzitso zambiri za m’Baibulo zimafotokozedwa mwachidule. Ndiyeno tingatani ngati wophunzira akukana kuvomereza chiphunzitso chinachake kapena akuumirira kwambiri chikhulupiriro chinachake chonama? Kungakhale kothandiza kudzakambirana naye nkhaniyo kuchokera m’buku lina limene limafotokoza momveka bwino zimene Baibulo limafotokoza pa nkhaniyo. Ngati wophunzirayo sakumvetsabe, isiyeni nkhaniyo kuti mudzaione nthawi ina koma pitirizani kuchita naye phunziro monga mwa nthawi zonse. (Yoh. 16:12) Akamadziwa zambiri zimene zili m’Baibulo ndi kupita patsogolo mwauzimu, akhoza kudzayamba kumvetsetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa.
4 Khalani Wodzichepetsa: Ngati mukukayikira za yankho la funso, pewani kuyankha za m’mutu mwanu. (2 Tim. 2:15; 1 Pet. 4:11) Muuzeni kuti mukafufuza za nkhaniyo ndipo mudzamuyankha. Mwina mungathe kugwiritsa ntchito mwayi umenewu kuphunzitsira wophunzira mmene timafufuzira. Pang’ono ndi pang’ono m’phunzitseni mmene angagwiritsire ntchito mabuku osiyanasiyana amene gulu la Yehova lapereka pamene akufuna kufufuza. Mwanjira imeneyi, iye m’kupita kwa nthawi akhoza kumadzipezera yekha mayankho a mafunso amene angamakhale nawo.—Mac. 17:11.