Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini Apanthaŵi Yake a Chowonadi
“Mwandiwombola, Inu Yehova, Mulungu wa chowonadi.”—SALMO 31:5.
1, 2. (a) Kodi mlongo wina anamva motani ponena za kanthu kena kamene anaŵerenga mu Nsanja ya Olonda? (b) Kodi ndimafunso otani amene akufunsidwa ponena za magazini athu?
“ZIKOMO kwambiri,” analemba motero mlongo Wachikristu, “kaamba ka chidziŵitso chabwino koposa cha nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yakuti ‘Mungathe Kupeza Chitonthozo m’Nthaŵi ya Nsautso.’a Mfundo zambiri zimene munafotokoza zinalidi zogwirizana ndendende ndi malingaliro amene ndakhala ndikulimbana nawo; kuli ngati kuti nkhani imeneyi inalembedwera ineyo mwachindunji. Pamene ndinaiŵerenga kwanthaŵi yoyamba, misozi inatuluka m’maso mwanga. Nkotonthoza kwambiri kudziŵa kuti munthu wina akuzindikira mmene ndimamvera! Ndine woyamikira kwambiri kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Kodi nkuti kwina kumene tingapeze malonjezo a moyo wosatha m’Paradaiso mtsogolo posachedwa ndipo, tsopano lino, chitonthozo cha miyoyo yathu! Zikomo. Zikomo kwambiri.”
2 Kodi munayamba mwadzimvapo motero? Kodi zinachitikapo kuti munaona kanthu kena mu Nsanja ya Olonda kapena m’magazini anzake a Galamukani!, kukhala katalembedwera makamaka inuyo? Kodi nchiyani chimene magazini athu ali nacho chimene chimakopa mitima ya anthu? Kodi ndimotani mmene tingathandizire ena kupindula ndi uthenga wake wopatsa moyo?—1 Timoteo 4:16.
Magazini Amene Amachirikiza Chowonadi
3. Kodi pali pachifukwa chabwino chotani chimene magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ayambukirira mitima ya oŵerenga ake ambiri?
3 Yehova ndi “Mulungu wa chowonadi.” (Salmo 31:5) Mawu ake, Baibulo, ndibuku la chowonadi. (Yohane 17:17) Anthu owona mtima amalabadira chowonadi. (Yerekezerani ndi Yohane 4:23, 24.) Chifukwa chimodzi chimene Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! yayambukira mitima ya oŵerenga ake mamiliyoni ambiri nchakuti ali magazini a umphumphu ndi chowonadi. Ndithudi, Nsanja ya Olonda inayamba kufalitsidwa chifukwa cha nkhani ya kukhulupirika ku chowonadi Chabaibulo.
4, 5. (a) Kodi ndimikhalidwe iti imene inachititsa C. T. Russell kufalitsa Watch Tower? (b) Kodi magazini a Nsanja ya Olonda akugwiritsiridwa ntchito motani ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?
4 Mu 1876, Charles T. Russell anagwirizana ndi Nelson H. Barbour, wa ku Rochester, New York. Russell anapereka ndalama kuyambitsanso kusindikizidwa kwa magazini achipembedzo a Barbour a Herald of the Morning, okhala ndi Barbour monga mkonzi wamkulu ndi Russell monga wachiŵiri kwa mkonzi. Komabe, patapita pafupifupi chaka chimodzi ndi theka, m’kope la August 1878 la Herald, Barbour analemba nkhani imene inakana mphamvu yowombola ya imfa ya Kristu. Russell, amene panthaŵiyo anali wachichepere kwa Barbour ndi zaka pafupifupi 30, anayankha mwa kulemba nkhani m’kope lotsatira lenilenilo imene inachirikiza dipo, limene anati lili “limodzi la ziphunzitso zofunika koposa za Mawu a Mulungu.” (Mateyu 20:28) Atayesayesa mobwerezabwereza kulingalira Mwamalemba ndi Barbour, Russell pomalizira pake anasiyiratu kugwirizana ndi Herald. Kuyambira ndi kope la June 1879 la magazini amenewo, dzina la Russell silinaonekerenso monga wachiŵiri kwa mkonzi. Patapita mwezi umodzi, Russell wa zaka 27 anayamba kufalitsa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence (yodziŵika tsopano kukhala Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova), imene kuyambira pachiyambi yachirikiza chowonadi Chamalemba, chonga dipo.
5 Kwa zaka 114 zapitazo, Nsanja ya Olonda, mofanana ndi loya waluso, yadzisonyeza kukhala yochirikiza chowonadi Chabaibulo ndi ziphunzitso zake. Pakuchita motero, yachititsa oŵerenga ake oyamikira mamiliyoni ambiri kukhala ndi chidaliro mwa iyo. Imachirikizabe dipo mwamphamvu. (Mwachitsanzo, onani kope la February 15, 1991.) Ndipo ikupitirizabe kukhala chiŵiya chachikulu cha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi Bungwe lake Lolamulira cholengezera Ufumu wokhazikitsidwa wa Yehova ndi kugaŵira chakudya chauzimu “panthaŵi yake.”—Mateyu 24:14, 45.
6, 7. Kodi cholinga chimene chinatchulidwa cha The Golden Age chinali chotani, ndipo kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti anthu oganiza analabadira uthenga wake?
6 Bwanji ponena za magazini a Galamukani!? Kuyambira pachiyambi chake, Galamukani! nayonso yachirikiza chowonadi. Otchedwa The Golden Age poyamba, magazini ameneŵa analinganizidwa kuti azigaŵiridwa kwa anthu. Ponena za cholinga chake, kope loyamba la October 1, 1919, linati: “Chifuno chake ndicho kufotokoza mogwirizana ndi nzeru Yaumulungu tanthauzo lenileni la zochitika zazikulu za masiku ano ndi kusonyeza anthu oganiza mwa umboni wosatsutsika ndi wotsimikizira kuti nthaŵi ya madalitso aakulu a mtundu wa anthu yayandikira.” Anthu oganiza analabadira uthenga wa The Golden Age. Kwa zaka zambiri, chiŵerengero cha makope ofalitsidwa chinali chachikulu kuposa cha Nsanja ya Olonda.b
7 Komabe, chifukwa chimene Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zakhalira zokopa kwambiri sichili chabe chenicheni chakuti amafalitsa chowonadi chonena za chiphunzitso ndi kufotokoza tanthauzo laulosi la mikhalidwe yadziko. Makamaka m’zaka khumi kapena makumi aŵiri zapitazo, magazini athu akopa mitima ya anthu pachifukwa chinanso.
Nkhani Zapanthaŵi Yake Zimene Zimayambukira Miyoyo ya Anthu
8. Kodi ndikusintha kotani kumene Yuda anachita polemba, akumafulumiza oŵerenga ake kukaniza zisonkhezero zoipitsa zotani mkati mwa mpingo?
8 Pafupifupi zaka 30 pambuyo pa imfa ndi kuuka kwa Yesu Kristu, wolemba Baibulo Yuda anayang’anizana ndi mkhalidwe wovuta. Anthu achisembwere, amakhalidwe auchinyama anakwaŵira mtseri pakati pa Akristu. Yuda anafuna kulembera Akristu anzake za nkhani yachiphunzitso—chipulumutso chimene Akristu odzozedwa onse ali nacho. Mmalo mwake, motsogozedwa ndi mzimu woyera, anakuona kukhala kofunika kufulumiza oŵerenga ake kukaniza zisonkhezero zoipitsa mkati mwa mpingo. (Yuda 3, 4, 19-23) Yuda anasinthira kumkhalidwewo napereka uphungu wapanthaŵi yake umene unakwaniritsa zosoŵa za abale ake Achikristu.
9. Kodi kukonza nkhani zapanthaŵi yake za m’magazini athu kumaloŵetsamo chiyani?
9 Mofananamo, kukonza nkhani zapanthaŵi yake za m’magazini athu kuli thayo lovuta kwambiri. Nthaŵi zimasintha, anthu nawonso amasintha—zosoŵa zawo ndi zofuna zawo tsopano sindizo zimene anafuna zaka khumi kapena makumi aŵiri zapitazo. Posachedwapa woyang’anira woyendayenda anati: “Pamene ndinakhala Mboni kalelo m’ma 1950, njira yathu yophunzirira Baibulo ndi anthu kwakukulukulu inali ya chiphunzitso—kuwaphunzitsa chowonadi ponena za Utatu, moto wahelo, moyo, ndi zina zotero. Koma tsopano, kukuoneka kuti, pali mavuto ambiri ndi zovuta zambiri m’miyoyo ya anthu kotero kuti tiyenera kuwaphunzitsa mmene angakhalire ndi moyo.” Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili choncho?
10. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kudabwa kuti pakhala kunyonyotsoka kosalekeza m’zochita za anthu chiyambire 1914?
10 Ponena za “masiku otsiriza,” Baibulo linalosera kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Timoteo 3:1, 13) Nchifukwa chake, sitiyenera kudabwa kuti pakhala kunyonyotsoka kosalekeza m’zochita za anthu kuyambira pamene nthaŵi ya mapeto inayamba mu 1914. Satana, amene nthaŵi yake yotsala ili yaifupi kwambiri koposa ndi kalelonse, akutsanulira mkwiyo wake pachitaganya cha anthu kuposa ndi kalelonse. (Chivumbulutso 12:9, 12) Chotero, makhalidwe ndi miyezo yabanja zili zosiyana kwambiri ndi mmene zinalili zaka 30 kapena 40 zokha zapitazo. Anthu ambiri sakonda chipembedzo monga momwe kunalili m’zaka makumi ambiri kalelo. Upandu ngwofala kwambiri kwakuti anthu akutenga njira zodzitetezera zimene zinali zosadziŵika zaka 20 kapena 30 zokha zapitazo.—Mateyu 24:12.
11. (a) Kodi ndinkhani zamtundu wotani zimene zili m’maganizo a anthu, ndipo ndimotani mmene kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kachitira ndi zosoŵazo? (b) Tchulani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! imene yayambukira moyo wanu.
11 Pamenepatu, nkosadabwitsa kuti nkhani zochita ndi maganizo, ndi zakakhalidwe ka anthu, ndi za banja zili m’maganizo a anthu ambiri. Kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kachitapo kanthu molimba mtima mwa kufalitsa nkhani zapanthaŵi yake mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimene zafotokoza zosoŵa zenizeni za anthu ndi zimene zayambukiradi miyoyo yawo. Talingalirani zitsanzo zotsatirazi.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji nkhani zonena za mabanja a kholo limodzi zinakonzedwa mu Nsanja ya Olonda mu 1981? (b) Kodi ndimotani mmene mlongo wina anasonyezera chiyamikiro chake kaamba ka nkhani za mabanja a kholo limodzi?
12 Nkhani zabanja. Pamene malipoti a padziko lonse anasonyeza kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha mabanja a kholo limodzi, nkhani zatsopano kotheratu za mutu wakuti “Mabanja a Kholo Limodzi—Kulimbana ndi Mavuto” zinakonzedwa m’kope la Nsanja ya Olonda ya March 15, 1981. Nkhanizo zinali ndi chifuno cha mbali ziŵiri: (1) kuthandiza makolo amene ali okha kulimbana ndi mavuto amene amakumana nawo ndi (2) kuthandiza ena kukhala ndi chidziŵitso chabwino kotero kuti asonyeze “chifundo” ndi “kusamalira” mowona mtima mabanja a kholo limodzi. (1 Petro 3:8; Yakobo 1:27, NW) Oŵerenga ambiri analemba makalata kusonyeza chiyamikiro kaamba ka nkhanizo. “Misozi inatuluka m’maso mwanga pamene ndinaona chikutocho,” linalemba motero kholo limene lili lokha, “ndipo pamene ndinatsegula magaziniwo ndi kuŵerenga nkhanizo, mtima wanga unadzala ndi chiyamiko kwa Yehova kaamba ka kupereka nkhani zoterozo panthaŵi imene zinali kufunikira.”
13. Kodi ndinkhani iti ya chidziŵitso chakuya ya kuchita tondovi imene inafalitsidwa mu Awake! mu 1981, ndipo kodi woŵerenga wina ananenanji za izo?
13 Nkhani zochita ndi maganizo. Nkhani ya kuchita tondovi yakhala ikufotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! chiyambire mma 1960. (1 Atesalonika 5:14) Koma kupenda kwatsopano ndi kopatsa chiyembekezo kwa nkhaniyo kunachitidwa mumpambo wa nkhani ya pachikuto yakuti “Mungathe Kulimbana ndi Kuchita Tondovi!” mu Awake! ya September 8, 1981. Posapita nthaŵi makalata oyamikira anafika ku Watch Tower Society kuchokera kumbali zonse za dziko. “Kodi ndimotani mmene ndingasonyezere papepala zimene zili mumtima mwanga?” analemba motero mlongo wina. “Ndili ndi zaka 24, ndipo m’zaka khumi zapitazo, ndakhala ndi nyengo zambiri za kuchita tondovi. Koma tsopano ndikudzimva kukhala woyandikana kwambiri ndi Yehova ndipo ndiyamikira kuti iye wachitapo kanthu pa zosoŵa za anthu ochita tondovi kupyolera m’nkhani zosonyeza chikondi zimenezi, ndipo ndangoti ndikuuzeni zimenezo.”
14, 15. (a) Kodi ndimotani mmene nkhani ya nkhanza yogona ana yasamalidwira m’magazini athu? (b) Kodi ndinkhani ziti za m’magazini zimene zinakondweretsa katswiri wa mpikisano wa akavalo ku Australia?
14 Nkhani za kakhalidwe ka anthu. Baibulo linalosera kuti mu “masiku otsiriza” anthu akakhala “odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1-3) Chotero, sitiyenera kudabwa kuti nkhanza yogona ana ikuchitidwa pamlingo waukulu lerolino. Nkhani imeneyi inafotokozedwa mosabisa m’nkhani yakuti “Chithandizo cha Mikhole Yogonedwa ndi Achibale” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1984. Pambuyo pa zaka zisanu ndi ziŵiri, mpambo wankhani ya pachikuto yakuti “Kupoletsa Mabala a Kuchitira Nkhanza Ana” mu Galamukani! ya October 8, 1991 unakonzedwa mosamalitsa kupereka chitonthozo ndi chiyembekezo kwa mikholeyo limodzinso ndi kudziŵitsa ena kuti nawonso apereke chithandizo chofunikira. Mpambo wankhani umenewu unachititsa oŵerenga ambiri kutilembera makalata ambiri koposa ndi kalelonse m’mbiri ya magazini athu. Woŵerenga wina analemba kuti: “Zimene zayambukira kwambiri kuchira kwanga ndizo malingaliro otonthoza ndi Malemba osonyezedwa m’nkhani zimenezi. Kudziŵa kuti Yehova sanandione kukhala wopanda pake kunandidzetsera mpumulo waukulu kwambiri. Kudziŵa kuti sindinali ndekha kunalinso kotonthoza.”
15 Katswiri wa mpikisano wa akavalo ku Melbourne, Australia, anaimbira foni kutali ku ofesi ya ku Sydney ya Watch Tower Society, kufotokoza kunyansidwa kwake ndi mkhalidwe wampikisano wa akavalo. Anati anali atangoŵerenga Galamukani! wa March 8 wakuti “Kugwirira Chigololo—Nkhaŵa ya Mkazi” ndipo sanathe kukhulupirira kuti kungakhale magazini amtengo wapatali otero. Anafunsa mafunso kwamphindi pafupifupi 30 ndipo anali wokondwa kumva mayankho operekedwa.
16. Kodi ndimwanjira zotani zimene mungasonyezere chiyamikiro chanu cha magazini athu?
16 Bwanji ponena za inu? Kodi moyo wanu wayambukiridwa ndi nkhani yakutiyakuti yofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!? Ngati zili choncho, mosakayikira muli ndi chiyamikiro chachikulu kaamba ka magazini athu. Kodi ndimotani mmene mungasonyezere chiyamikiro chanu? Ndithudi mwa kuŵerenga kope lililonse inu mwininu. Mungakhalenso ndi phande m’kuchititsa magazini amtengo wapatali ameneŵa kugaŵiridwa kwambiri. Kodi zimenezo zingachitidwe motani?
Agaŵireni kwa Ena!
17. Kodi nchiyani chimene mipingo ingachite kuwonjezera kugaŵira magazini?
17 Choyamba, pali kanthu kena kamene mpingo uliwonse ungachite. Kope la October 1952 la Informant (tsopano yotchedwa Utumiki Wathu Waufumu) linati: “Njira yabwino koposa yogaŵira magazini ili ya kunyumba ndi nyumba ndi kusitolo ndi sitolo. Chotero Sosaite ikupereka lingaliro lakuti njira zimenezi zogaŵira magazini zikhale chizoloŵezi cha zochitika za pa Tsiku Lamagazini.” Uphungu umenewo ukugwirabe ntchito lerolino. Mipingo ingalinganize Tsiku Lamagazini loikika, tsiku losankhidwa kwakukulukulu kaamba ka umboni wamagazini. Kwa mipingo yambiri, masiku a Loŵeruka osankhidwa mosakayikira angakhale nthaŵi yabwino. Inde, mpingo uliwonse usankhetu masiku kapena madzulo apadera a kuchitira umboni wamagazini—kunyumba ndi nyumba, kusitolo ndi sitolo, m’ntchito ya m’khwalala, ndi kwa amene timapititsira magazini. Ndiponso, kodi nchiyani chimene inuyo, wofalitsa Waufumu, mungachite kuwonjezera kugaŵira magazini?
18, 19. (a) Kodi ndimotani mmene kukhala wozindikira kufunika kwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kungakuthandizireni kugaŵira magazini? (b) Kodi ubwino wa ulaliki waufupi, wolunjika pogaŵira magazini ngwotani? (c) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza phindu la kupereka magazini kunyumba za anthu?
18 Kuzindikira kufunika kwa “Nsanja ya Olonda” ndi “Galamukani!” ndiko njira yoyamba. Ŵerengani magaziniwo pasadakhale. Pamene muŵerenga nkhani iliyonse, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndani amene angakondweretsedwe ndi nkhaniyi?’ Ganizani mawu angapo amene munganene kuti mudzutse chikondwerero m’nkhaniyo. Kuwonjezera pa kuchirikiza Tsiku Lamagazini loikika, bwanji osanyamula makopewo kuti mugwiritsire ntchito mpata uliwonse kuwagaŵira kwa ena—pamene muli paulendo kapena pokagula zinthu ndi pamene mukukambitsirana ndi antchito anzanu, anansi, anzanu a pasukulu, kapena aphunzitsi?
19 Lingaliro lachiŵiri nlakuti perekani ulaliki wosavuta. The Watchtower ya December 1, 1956, inati: “Ulaliki waufupi, wolunjika ngwabwino koposa pogaŵira magazini. Cholinga ndicho kugaŵira makope ambiri. Iwo ‘adzalankhula’ okha.” Ofalitsa ena akuona kukhala kogwira mtima kupeza lingaliro limodzi m’nkhaniyo, kuliumba m’mawu angapo, ndi kugaŵira magaziniwo. Ataloŵa m’nyumba, magaziniwo “angalankhule” kwa ena kuwonjezera pa munthu amene anawatenga kwa inu. Ku Ireland wophunzira wa payunivesite wachichepere anaŵerenga kope la Nsanja ya Olonda ya September 1, 1991, limene atate wake anatenga kwa Mboni ina. Nkhani zonena za kulankhulana ndi nkhani zina zinadzutsa chikondwerero chake. Mwamsanga atangoŵerenga magaziniyo, anaimbira foni Mboni, akumagwiritsira ntchito nambala yosonyezedwa m’buku la manambala a foni. Posapita nthaŵi phunziro Labaibulo linayambika, ndipo msungwanayo anabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wa “Chiphunzitso Chaumulungu” m’July 1993. Ndithudi, tiyeni tipereke magazini kunyumba za ena, kumene “angalankhule” kwa anthu! Woyang’anira woyendayenda wina anapereka lingaliro lina losavuta: “Tulutsani magazini m’chikwama chanu chamabuku.” Ndithudi, ngati zimene munena sizikopa mwininyumba, pamenepo mwinamwake zithunzithunzi zokongola za pachikuto zingakugaŵirireni magaziniwo.
20, 21. (a) Kodi ndimotani mmene mungakhalire wokhoza kusintha pochita ntchito yamagazini? (b) Kodi nchiyani chimene mungachite kuti mugaŵire magazini ochuluka mwezi uliwonse?
20 Lingaliro lachitatu nlakuti khalani wokhoza kusintha. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:19-23.) Konzekerani maulaliki achidule angapo. Khalani ndi nkhani imodzi m’maganizo imene idzakopa amuna, ndi ina imene idzakopa akazi. Kwa achichepere, mungagwiritsire ntchito nkhani ya “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” Khalaninso wokhoza kusintha panthaŵi imene mumachitira ntchito yamagazini. Kuwonjezera pa Tsiku Lamagazini, mungapeze kuti umboni wa madzulo umapereka mpata wabwino wa kugaŵira magazini kunyumba ndi nyumba.
21 Lingaliro lachinayi nlakuti khazikitsani chonulirapo chaumwini. Mphatika yakuti “Magazini Amatsogolera ku Njira ya ku Moyo,” imene inali mu Utumiki Wathu Waufumu wa May 1984, inati: “Monga mwa lingaliro, ofalitsa akhoza kukhala ndi chonulirapo, tinene kuti, magazini 10 pamwezi, zikumadalira pa mikhalidwe yawo; apainiya akhoza kumenyera chiŵerengero cha 90. Ndithudi, ofalitsa ena angakhoze kugaŵira magazini ochuluka pamwezi ndipo motero angakhazikitse chonulirapo chapamwamba chaumwini. Komabe, chifukwa cha kusakhala ndi thanzi labwino, mtundu wa gawo, kapena pazifukwa zina zabwino, zonulirapo za ena zingakhale zochepa. Chikhalirechobe utumiki wawo kwa Yehova uli wokulira mofananamo. (Mat. 13:23; Luka 21:3, 4) Chinthu chomwe chili chofunika ndicho kukhala ndi chonulirapo chaumwini.”
22. Kodi ndimwanjira yotani imene tingasonyezere kuti tikuyamikira Yehova kaamba ka magazini athu apanthaŵi yake a chowonadi?
22 Ndife oyamikira chotani nanga kuti Yehova, “Mulungu wa chowonadi,” wagwiritsira ntchito kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi Bungwe lake Lolamulira kutigaŵira magazini a panthaŵi yake ameneŵa! (Salmo 31:5) Malinga ngati Yehova alola, magazini ameneŵa adzapitirizabe kuchita ndi zosoŵa zenizeni za anthu. Adzapitirizabe kuchirikiza miyezo yapamwamba ya Yehova ya makhalidwe. Sadzasiya kuchirikiza chiphunzitso chowona. Ndipo adzapitirizabe kupereka chisamaliro pa kukwaniritsidwa kwa ulosi umene umasonyeza kuti masiku athu ndiwo nthaŵi pamene Ufumu wa Mulungu ukulamulira ndi pamene chifuniro cha Mulungu chikuchitidwa padziko lapansi kuposa ndi kale lonse ndi chiŵerengero chomawonjezereka cha olambira owona a Yehova. (Mateyu 6:10; Chivumbulutso 11:15) tili ndi chuma chamtengo wapatali chotani nanga mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tiyeni tigwiritsire ntchito bwino mpata uliwonse kugaŵira kwa ofatsa magazini ofunika ameneŵa amene amayambukira miyoyo ya anthu ndi kuchirikiza chowonadi Chaufumu.
[Mawu a M’munsi]
b Kwa zaka zambiri Nsanja ya Olonda inalingaliridwa kukhala magazini a Akristu odzozedwa okha. Komabe, kuyambira mu 1935, chigogomezero chowonjezereka chinaperekedwa pa kulimbikitsa a “khamu lalikulu,” amene chiyembekezo chawo ndicho moyo wosatha padziko lapansi, kutenga ndi kuŵerenga Nsanja ya Olonda. (Chivumbulutso 7:9) Patapita zaka zingapo, mu 1940, Nsanja ya Olonda inali kugaŵiridwa nthaŵi zonse kwa anthu m’makwalala. Zaka zingapo pambuyo pake, chiŵerengero cha makope ofalitsidwa chinawonjezereka mofulumira.
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ali magazini a chowonadi?
◻ Kodi ndimotani mmene Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zayambukirira miyoyo ya anthu?
◻ Kodi nchiyani chimene mipingo ingachite kuti iwonjezere kugaŵira magazini?
◻ Kodi ndimalingaliro otani amene angakuthandizeni kugaŵira magazini ochuluka?
[Bokosi patsamba 22]
Nkhani Zina Zimene Zayambukira Miyoyo ya Anthu
Mkati mwa zaka zambiri oŵerenga ambiri alemba makalata kusonyeza chiyamikiro kaamba ka nkhani zakutizakuti zofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pansipa pandandalikidwa zingapo chabe mwa nkhani zambiri zimene zinayambukira oŵerenga athu. Kodi nkhani zimenezi kapena zina zasintha moyo wanu?
Nsanja ya Olonda
“Landirani Chithandizo cha Mulungu m’Kugonjetsa Machimo Amtseri” (October 15, 1985)
“Kuphunzira Kupembedza Mulungu Kulinga kwa Okalamba” (June 1, 1987)
“Maphunziro Okhala ndi Cholinga” (November 1, 1992)
Galamukani!
“Mungathe Kulimbana ndi Kuchita Tondovi!” (Awake!, September 8, 1981)
“Pamene Munthu Amene Mukonda Amwalira . . . ” (Awake!, April 22, 1985)
“Tetezerani Ana Anu!” (October 8, 1993)
[Chithunzi patsamba 23]
Ku Canada—kulalikira kunyumba ndi nyumba ndi magazini
[Chithunzi patsamba 24]
Ku Myanmar—kugaŵira magazini amene amasonyeza njira ya ku moyo