Kodi Magaziniwo Mumawaŵerenga?
1 Amishonale ena okwatirana mu Afirika anati ponena za magazini athu: “Nsanja ya Olonda imatithandiza kukhala atcheru mwauzimu m’gawo lathu. Timapeza chilimbikitso ndi nyonga m’magazini iliyonse.” Kodi mumayamikira kwambiri magazini athu mofananamo? Kodi inunso muli ofunitsitsa kuwaŵerenga?
2 Kumatenga nthaŵi yaitali kukonza nkhani za m’magazini zimene zingaŵerengedwe mu mphindi zochepa chabe. Poti mwadziŵa zimenezi, kodi mudzangoona nkhani zimene zilimo, kuonamo zithunzi, kapena nthaŵi zina kungoŵerengako nkhani imene yakuchititsani chidwi? Nkwanzeru kuchita zoposa pamenepo. Tiyenera kukhala ndi nthaŵi ya kuŵerenga ndi kupenda nkhani zonse za m’kope lililonse la magazini athu. Nsanja ya Olonda ndi magazini yathu yaikulu imene imakhala ndi chakudya chauzimu cha panthaŵi yake. Galamukani! imakhala ndi nkhani zokondweretsa ndi zophunzitsa pankhani zosiyanasiyana. Zimene timaphunzira mwa kuŵerenga magazini ameneŵa si kuti zimangotilimbikitsa ife mwauzimu komanso zimatikonzekeretsa kuchita utumiki mogwira mtima. Pokhala oŵerenga okhulupirika ife enife, tidzakhala ofunitsitsa kugaŵira ena magaziniwo.
3 Mmene Tingapititsire Patsogolo Zizoloŵezi za Kuŵerenga: Kodi mungathe kumaŵerenga magazini iliyonse? Nawa malingaliro aŵiri amene amathandiza anthu ochuluka. (1) Pangani ndandanda yoŵerengera yokhazikika. Mwa kungopatula mphindi 10 kapena 15 tsiku lililonse kuti muŵerenge, mudzadabwa ndi kuchuluka kwa zimene mungaŵerenge pa mlungu umodzi. (2) Khalani ndi njira yoti muzidziŵira zimene mwaŵerenga. Mwina mukhoza kuchonga poyambira pa nkhani iliyonse imene mwaŵerenga. Popanda kuchita zimenezi mukhoza kudumpha nkhani zina kapenanso magazini yathunthu osaiŵerenga. Nkofunika kupanga njira yoŵerengera imene ingakhale yabwino kwa inu ndi kuimamatira.—Yerekezerani ndi Afilipi 3:16.
4 Mwanzeru “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wachita mogwirizana ndi kusintha kwa nthaŵi mwa kufalitsa nkhani zimene zimagwirizana ndi zosoŵa zenizeni za anthu. (Mat. 24:45) Zoonadi, magaziniwa akhudza miyoyo yathu. Mmene timapitira patsogolo mwauzimu kwakukulukulu kumadalira pa zizoloŵezi zathu za kuŵerenga zinthu za teokrase. Madalitso auzimu ochuluka akuyembekezera amene amapeza nthaŵi ya kuŵerenga magazini onse.