Sankhani Nkhani Zokopa Chidwi cha Anthu
1 Monga amachitira akatswiri a uta, omwe amalunjikitsa mivi yawo mosamala, ofalitsa ampingo ndi apainiya ambiri zikuwayendera bwino kwambiri chifukwa amasankha nkhani za Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zomwe zingasangalatse kwenikweni anthu a m’dera lawo. Iwo amadziŵiratu kuti ndi ayani omwe angakondedi kuŵerenga nkhani zakutizakuti za magaziniwo. Kodi amachita bwanji zimenezo?
2 Choyamba, amaŵerenga kope lililonse kuyambira kuchikuto mpaka kuchikuto. Ndiyeno amadzifunsa kuti, Kodi ndi munthu wotani yemwe nkhani iliyonse ingamsangalatse? Kenako amayesetsa kukachezera anthu omwe angakondedi kuŵerenga nkhani yomweyo. Ngati akuganiza kuti kope lina lidzalandiridwa ndi anthu ambiri a m’dera lawo, amaoda makope ambirinso.
3 Magazini Athu Amalemekezedwa Kwambiri: Mmodzi mwa olembetsa sabusikripishoni ya magazini athu yemwe amagwira ntchito ku kampani ina ya ku Nigeria yotchuka kwambiri yofalitsa magazini padziko lonse, ponena za Galamukani! anati: “Ndikukuyamikirani chifukwa cha magazini ya anthu onse padziko lapansi.” Winanso yemwe ali ndi khama loŵerenga magazini athu anati: “Ndi ngale zamtengo wapatali zedi za nzeru! M’magazini ameneŵa simumasoŵeka nkhani ina imene ndimakonda.”
4 Magaziniwo amafotokoza nkhani zambirimbiri, kuphatikizapo Baibulo, zochitika zadziko, zokhudza banja, mavuto a anthu, mbiri yakale, sayansi, moyo wa nyama ndi wa zomera, kungotchula zoŵerengeka chabe. Nzoonadi kuti munthu angakonde kwambiri kuŵerenga kanthu kena ngati kamakhudzana ndi zosoŵa zake, mikhalidwe yake, kapena ntchito yake. Popeza timalankhula ndi anthu ambiri, aliyense wokhala ndi zokonda zake ndi mavuto ake, kusankha nkhani zomwe zingasangalatse kwenikweni anthu amene timakumana nawo nkothandiza.
5 Taonani zimene zinachitika pamene Mboni ziŵiri zinagaŵira wina wolemba nkhani za m’nyuzipepala kope la Galamukani! ya September 8, 1996. Iye analemba kuti: “Ndisanakane, winayo anatinso: ‘Muli nkhani yonena za Aindiya a ku America. Tikudziŵa kuti mwakhala mukulemba zambiri pankhani imeneyi,’” Iye anatenga magaziniyo, ndipo pachakudya cha mmaŵa, anaiŵerenga nkhani yonena za Aindiya, kenako nkudzavomereza kuti “inali yabwino kopambana” ndipo “njoonadi.”
6 Kodi Nchiyani Chimasangalatsa Anthu m’Dera Lanu? Kodi mwaona chiyani m’magazini a miyezi yaposachedwapa chimene chingasangalatse eni masitolo ndi anthu a bizinesi m’dera lanu kapena anansi anu, anzanu a kuntchito, ndi anzanu a kusukulu? Kodi nchiyani makamaka chingakondweretse maloya, aphunzitsi, aphungu abanja ndi a kusukulu, alangizi a achinyamata, antchito zothandiza anthu ndi madokotala? Kuganizira za anthu amene mumawalalikira mmene mukupenda kope lililonse kudzakuthandizani kupeza njira zabwino kopambana zofalitsira mawu a choonadi.
7 Mukapeza munthu yemwe wakondwa kwambiri ndi nkhani ina ya Nsanja ya Olonda kapena ya Galamukani!, yemwenso walandira magaziniyo, munganene kuti: “M’magazini yamtsogolo ngati mudzakhala nkhani ina imene ndidzaganiza kuti ingakusangalatseninso, ndidzakubweretserani kope.” Panjira zanu zamagazini mungathe kumamfikiranso munthuyo, mukumabwererako ndi magazini atsopano. Zimenezo zikufanana ndi zimene takhala tikuchita popempha anthu kubwereranso kukawachezera omwe anakondwa kwambiri ndi nkhani za m’magazini athu.
8 Khalani ndi Cholinga Chauzimu: Zaka zingapo zapitazo, munthu wina wofunitsitsa kupambana pazantchito anapeza magazini ya Galamukani! yomwe inali ndi nkhani yomsangalatsa. Komabe, munthu wokonda chipembedzo ameneyu anaŵerenganso kope la Nsanja ya Olonda yomwe inali ndi nkhani imene inamsonkhezera kupendetsetsa chiphunzitso cha Utatu chomwe anakhulupirira kwa moyo wake wonse. Patapita miyezi isanu ndi umodzi anabatizidwa! Choncho, musamazengereze kuwalankhula anthu oŵerenga magazini athu pankhani zauzimu. Mungawasonyeze brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndi kuwapempha mphindi zoŵerengeka chabe kuti mukambitsirane nawo phunziro limodzi nthaŵi iliyonse pamene mwabwererako muli ndi magazini atsopano.
9 Onetsetsani kuti mwa anthu amene mudzawachezeranso ndiponso mwa anthu a bizinesi ndi ayani amene angakonde makope atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndiyeno yesetsani kukawapeza. Fikirani anthu ambiri ndi magazini ofunika ameneŵa. Ndipo musadzaiŵale kuti pamene mukuthandiza anthu ambiri kuŵerenga magazini athu, ‘mukuponya zakudya zanu pamadzi.’ Pakupita kwa nthaŵi, mudzapezadi ophunzira anzanu mtsogolomu.—Mlal. 11:1, 6.