Kodi Mukulinganiza Kudzatani m’Chilimwe?
1 Kodi si zoona kuti tingafikire zolinga zathu zopindulitsa ngati tikonzekera mmene tingagwiritsirire ntchito bwino kwambiri nthaŵi yathu? Miyezi ikudzayi ingatipatse mipata yosiyanasiyana yakufikira zolinga zateokrase. (Miy. 21:5) Kodi zina mwa zimenezo nziti?
2 Msonkhano wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu” uli chochitika chimodzi chimene tonsefe tiyenera kuchiphatikiza polinganiza zinthu zathu chilimwe chino. Pemphani nthaŵi kuntchito kapena kusukulu kuti tsiku lililonse la msonkhanowo mudzapezekepo.
3 Bwanji osalinganiza kudzaonjezera utumiki wanu wakumunda m’miyezi ikudzayi, poti tsopano nyengo yadzinja yatha, mungakhale ndi nthaŵi yambiri yowonongera pantchito yolalikira. Maholide a sukulu adzapatsa achinyamata mpata wakuchita upainiya wothandiza m’mwezi umodzi kapena ingapo ikudzayo. Enanso angalinganiziretu kudzachita upainiya wothandiza m’August, poti padzakhala milungu isanu yathunthu ndi maholide aŵiri. Mmene tizitsiriza chaka chautumiki August uno, tidzayesetsa ndithu kuti aliyense agwire nawo ntchito kwambiri mu utumiki.
4 Kodi mukulinganiza kudzathandiza mpingo wina wapafupi womwe ukufuna chithandizo pofola gawo lake? Woyang’anira dera angauze akulu zimene zikufunikira m’dera lanu. Kapena, ngati mungayenerere, ndipo mwina mungakonde kufunsira ku Sosaite kuti mukafole gawo losafoledwafoledwa kapena lopanda munthu, pemphani fomu kwa akulu anu. Ngati mudzakhala paholide kutali ndi kwanu, linganizani kudzamapezeka pamisonkhano ndi kuloŵa nawo mu utumiki wakumunda ndi mpingo wakomweko. Ngati mudzakachezera achibale omwe sali Mboni za Yehova, linganizani pasadakhale njira zimene mungakawauzire choonadi.
5 Kodi mukulinganiza kudzatani m’miyezi ikudzayi? Mosakayikira, mungakonde kuti mupume. Komabe musanyalanyaze mipata yambiri yomwe ilipo imene ingakulimbikitseni mwauzimu mwa kufunafunabe Ufumu choyamba.—Mat. 6:33; Aef. 5:15, 16.