“Wokonzeka Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino”
1 Anthu a Yehova lerolino adalitsidwa ndi chakudya chauzimu chambiri ndiponso chonona. (Yes. 25:6) Pali nkhani zambiri za m’Malemba zimene tingasangalale nazo mwa phunziro laumwini ndi labanja, ndiponso pamisonkhano yampingo, yadera, ndi yachigawo. Koma kodi timazigwiritsira ntchito zonsezo ndi cholinga chakukhala “woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino”?—2 Tim. 3:17.
2 Tangoganizani za mitundumitundu ya chakudya chauzimu cha chaka cha 1998, chomwenso changotsala pang’ono kutha! Mwa misonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu, tikuphunzira mfundo zina zazikulu za m’mabuku 23 a Malemba Achikristu Achigiriki, kupendanso mfundo zosiyanasiyana za ziphunzitso za Baibulo. Tikubwerezanso chigawo chimodzi mwa zigawo zitatu za buku la Chidziŵitso, ndi buku la Chimwemwe cha Banja. Kuwonjezerapo, timadyetsedwa ndi makope 12 a Utumiki Wathu Waufumu, nkhani 52 zophunzira mu Nsanja ya Olonda, ndiponso nkhani zapoyera pafupifupi 52, zamitu yosiyanasiyana ya m’Baibulo. Maprogramu abwino kwambiri a msonkhano wachigawo ndi wadera amawonjezeredwa pa zonsezo. Komatu ndiye tikupatsidwa zinthu zabwino zauzimu zochulukitsitsa zedi!
3 Yamikirani Zimene Yehova Amapereka: Kuti tipindule kwambiri, tifunikira kumvetsetsa chifukwa chake Yehova akupereka chakudya chauzimu chochuluka chonchi. Kudya zinthu zabwino zimenezi kumamangirira chikhulupiriro chathu ndi kulimbikitsa unansi wathu ndi iye. (1 Tim. 4:6) Komabe, chakudya chauzimucho samangotipatsa kuti azilangiza ife tokha. Chimatisonkhezera kuuza ena choonadi ndipo chimatithandiza kukhala ogwira mtima pochita zimenezo monga atumiki a uthenga wabwino.—2 Tim. 4:5.
4 Tiyeni tisamanyalanyaze zosoŵa zathu zauzimu, komatu nthaŵi zonse tizikulitsa chikhumbo cha chakudya chauzimu chokhutiritsa chochokera pathebulo ya Yehova. (Mat. 5:3; 1 Pet. 2:2) Kuti tipindule kwambiri timafunikira kupatula nthaŵi yokwanira ya zinthu zofunikazo, zonga phunziro la Baibulo laumwini ndi labanja lanthaŵi zonse ndi kupezekanso pamisonkhano nthaŵi zonse. (Aef. 5:15, 16) Mapindu osangalatsa amene timapeza tikamachita zimenezo amakhala ogwirizana ndi mawu olimbikitsa ouziridwa amene Paulo analembera Akristu achihebri okhulupirika, amene ali pa Ahebri 13:20, 21.