Kodi Mukupindula?
1 Mamiliyoni a anthu lerolino amafuna kudziŵa mmene angagonjetsere mavuto ndi kukhala ndi moyo wachimwemwe. Amaŵerenga kwambiri mabuku onena za mmene munthu angadzithandizire kapena amafuna malangizo a mmene angasinthire miyoyo yawo ku magulu ndi mabungwe a anthu. Mwina ena anganene mapindu ochepa amene apeza. Komabe, kuona mmene moyo ulili lerolino, kodi anthu aphunzira kusangalala ndi moyo wamtendere, moyo wokhutiritsa zedi mwa mapulogalamu a anthu aulangizi? Ndithudi ayi!—1 Akor. 3:18-20.
2 Komano, Mlengi wathu amapereka kwaulere malangizo othandiza kwambiri kwa onse amene angamvetsere. Yehova amafuna kuti aliyense apindule ndi chiphunzitso chake. Mowoloŵa manja wapereka Mawu ake ouziridwa kuti atsogolere anthu mowongoka, ndipo wapangitsa uthenga wabwino wa Ufumu wake kulalikidwa padziko lonse. (Sal. 19:7, 8; Mat. 24:14; 2 Tim. 3:16) Moyo wachimwemwe chenicheni umadalira kwambiri pa kulabadira malamulo a Yehova.—Yes. 48:17, 18.
3 Chitsogozo cha Yehova n’chapamwamba kwambiri kuposa zimene zimapezeka m’mabuku onse onena za mmene munthu angadzithandizire kapena m’malangizo a dzikoli. Tingapeze thandizo lenileni ndi mapindu okhalitsa ngati tigwiritsa ntchito mokwanira zogaŵira za Yehova monga mmene zilili m’Mawu ake ndi zimene gulu lake limaphunzitsa.—1 Pet. 3:10-12.
4 Pindulani Pamisonkhano ya Mpingo: Lerolino, Yehova akusonyeza chidwi kwambiri potiphunzitsa njira zake, ndipo timapindula mwa kulabadira malangizo ake. Misonkhano yathu isanu mlungu uliwonse imapereka umboni wakuti Yehova amatikonda. Kupezeka pamisonkhano ya mpingo, kumawonjezera kum’dziŵa kwathu Mulungu. Timaphunzira mmene tingadzitetezere ku zoipa mwa kuyandikira kwambiri kwa Yehova. Mwa njira imeneyi timalimbikitsidwa.
5 Si zokhazi ayi. Pamisonkhano ya mpingo timatha ‘kufutukuka.’ (2 Akor. 6:13, NW) Izi zimaphatikizapo kudziŵana ndi anthu ena mumpingo. Timapindula mwa kulimbikitsana, mofanana ndi zimene mtumwi Paulo analemba m’kalata yake yopita kwa Aroma. (Aroma 1:11, 12) Pamene ankalembera Ahebri, analangiza zolimba awo amene anali ndi chizoloŵezi chophonya mayanjano achikristu.—Aheb. 10:24, 25.
6 Kukhala achimwemwe ndi okhutira m’moyo kumayenderana ndi kuchita chidwi ndi zochita za ena. Timalimbikitsidwa kupeza njira zoti tithandize ena kukhala osangalala. Chotero misonkhano yathu yachikristu, ilipo kuti tipindule nayo ndiponso kupindulitsa awo amene timacheza nawo bwino. Chimene chimafunika kuti tichite ndicho kutengamo mbali ndi mtima wonse.
7 Mtumwi Paulo mu uphungu wake kwa Timoteo anakamba mfundo yomweyo pamene analemba kuti: “Khala ukudziphunzitsa uli ndi kudzipereka kwaumulungu monga cholinga chako.” (1 Tim. 4:7, NW) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndikudziphunzitsa? Kodi ndikuphunzira kupindula ndi zimene ndimamva kumisonkhano yampingo?’ Mayankho athu adzakhala inde ngati tilabadira zimene timamva kumisonkhano ndi kuyesetsa kuzigwiritsa ntchito. Ndi maso achikhulupiriro, tiyenera kuona zambiri osati abale amene akuphunzitsa okhawo, tiyeneranso kuona Yehova monga Mlangizi Wamkulu wa anthu ake.—Yes. 30:20.
8 Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi Msonkhano wa Utumiki: Misonkhano iŵiri imeneyi inalinganizidwa kuti itithandize kukhala ogwira mtima mu utumiki wachikristu. Sukulu ya Utumiki Wateokalase kwenikweni ilipo kaamba ka chifukwa chimenecho—sukulu ya ophunzira amene amalandira malangizo ndi uphungu nthaŵi zonse. Muli ndi mwayi wosonyeza kupita kwanu patsogolo monga wokamba nkhani poyera ndiponso monga mphunzitsi wa Mawu a Mulungu. Koma kuti mupindule kwambiri ndi sukuluyi, muyenera kulembetsa, kupezekapo, kutengamo mbali nthaŵi zonse, ndi kuikirapo mtima pankhani imene mwapatsidwa. Kulandira uphungu umene mwapatsidwa ndi kuugwiritsa ntchito kudzakuthandizani kupita patsogolo.
9 Msonkhano wa Utumiki umatiphunzitsa kufunika kwa utumiki wachikristu ndipo umatisonyeza mmene tingachitire ntchito yopanga ophunzira. Kodi inu ndi banja lanu mukupindula kwambiri ndi zimene zimakambidwa pamisonkhano iŵiri imeneyi? Banja lina lachikristu linati: “Pamsonkhano wa Utumiki winawake, tinaphunzira kuti tiyenera kuchitira lemba latsiku pamodzi monga banja. Sitinkachita zimenezi, koma tsopano timachita.” Kodi apindula motani? Iwo akuti: “Timaona kuti nkhani zathu panthaŵi yachakudya n’zosangalatsa kwambiri. Palibenso kukangana panthaŵi yachakudya.” Kodi ngakhale ana aang’ono amapindula ndi misonkhano? Inde. Amayi akuti: “N’zodziŵikiratu kuti misonkhano imawakhudza mtima kwambiri ana athu. Mlungu winawake tinam’pezerera mwana wathu wamwamuna wazaka zisanu ndi chimodzi akunena nkhani zina zabodza. Koma mlungu umenewo pamsonkhano, nkhani yachilangizo inali yokhudza bodza. Ndi nkhope yamanyazi, mwana wathuyo anayang’ana atate ake ndipo anaŵeramira pansi. Anaphunzirapo kenakake, ndipo kuyambira pomwepo tinalibenso vuto.”
10 Mlongo wina amene ndi mpainiya akuti amasangalala kuti malingaliro a mmene tingapititsire patsogolo utumiki wathu amaperekedwa pa Msonkhano wa Utumiki. Chifukwa chiyani? Iye akuti: “Ndimazoloŵera. Nthaŵi zina ndimaganiza kuti malingaliro amene ali mu Utumiki Wathu wa Ufumu sangagwire ntchito. Koma pa Msonkhano wa Utumiki, ndikamva kuti tiyenera kuyesera, ndimalimbikitsidwa kugwiritsa ntchito malingalirowo. Zimapangitsa utumiki kukhala wosangalatsa!” Atagwiritsa ntchito malingaliro a mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba kwa milungu ingapo, pa ulendo woyamba anayamba phunziro ndi mtsikana amene anali kupempherera thandizo.
11 Mukamva nkhani imene ili ndi uphungu wa Baibulo pa zosankha zanu, kodi mumazindikira kuti Yehova ndiye akulankhula nanu mwachindunji? Mbale wina anamva motero. Iye anati: “Posachedwapa pamsonkhano wina, panali nkhani imene mbale wokamba nkhaniyo anafotokoza mitundu ya zosangalatsa zimene zili zoyenera Akristu ndi zimene zili zosayenera. Ndinkakonda kuonera nkhonya pa wailesi yakanema. Koma utangotha msonkhano umenewo, ndinaona kuti maseŵera ameneŵa anali m’gulu la maseŵera amene si oyenera kwa Akristu. Choncho sindioneranso.” Inde, ngakhale kuti mbale ameneyu ankakonda chinthu chimene chinali chachiwawa, modzichepetsa analabadira chitsogozo cha Yehova.—Sal. 11:5.
12 Msonkhano Wapoyera, Phunziro la Nsanja ya Olonda, ndi Phunziro la Buku la Mpingo: Nkhani zapoyera zimene timaphunzira mlungu uliwonse zimakhala ndi nkhani zosiyanasiyana za Baibulo. Kodi mumaphunziramo chiyani m’nkhani zimenezi? Mwamuna wina wachikristu anatchula mapindu amene anapeza. Iye anati: “Nkhani ina yapoyera inagogomezera zipatso zonse za mzimu. Ponena za iyemwini wokamba nkhaniyo anati, kuti athe kuwongolera kukulitsa zipatso zimenezi, ankasankha mkhalidwe umodzi n’kuugwiritsa ntchito kwa mlungu wonse. Pamapeto a mlungu, ankaona zimene wachita posonyeza chipatso chimenecho m’zochita zake za tsiku ndi tsiku. Kenako mlungu wina ankagwiritsa ntchito mkhalidwe wina. Malingaliro ameneŵa anandisangalatsa ndipo ndinayamba kuchita zomwezo.” Anagwiritsatu ntchito bwino zimene anaphunzira!
13 Phunziro la Nsanja ya Olonda limatiphunzitsa kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo m’mikhalidwe yosiyanasiyana m’moyo. Izi zimatithandiza kukhala odekha m’maganizo ndi mu mtima ngakhale pamavuto. Phunziro la Nsanja ya Olonda limatithandizanso kuyendera limodzi ndi choonadi chimene chikuwonjezereka. Mwachitsanzo, kodi sitinapindule kuphunzira Nsanja ya Olonda ya May 1, 1999, pankhani za mitu iyi: “Kuyenera kuti Izi Zioneke,” “Iye Amene Aŵerenga M’kalata Azindikire,” ndi “Khalani Atcheru Ndipo Chitani Khama!” Kodi maphunziro ameneŵa anakukhudzani motani inuyo panokha? Kodi mumasonyeza mwa zochita zanu kuti mumalabadira chenjezo la Yesu lonena za m’tsogolo? Kodi mukukonzekera ziyeso zili patsogolopa pamene ‘chonyansa cha kupululutsa, chidzaima m’malo oyera’? (Mat. 24:15-22) Kodi zolinga zanu ndi moyo wanu umasonyeza kuti si zinthu za kuthupi, koma kuyeretsa dzina la Yehova kumene kuli chinthu chofunika kwambiri kwa inu? Pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, kodi sitikuphunzira kupindula pakalipano?
14 Tangoganizani kuchuluka kwa zinthu zimene timaphunzira mlungu uliwonse pa Phunziro la Buku la Mpingo. Pakali pano tikuphunzira buku la m’Baibulo la Danieli. M’miyezi iŵiri imene taphunzira buku la m’Baibulo limeneli, kodi sitikuona chikhulupiriro chathu chikukula mlungu uliwonse? Monga Danieli, mneneri wokondedwa wa Yehova, timalimbitsa chikhulupiro chathu kuti tipirire.
15 Yehova Amatiphunzitsa kuti Tizikhala Mosangalala: Sitithedwa nzeru kwenikweni ngati tilabadira malamulo a Mulungu. Komanso, timakhala mosangalala monga mmene kusangalala ndi moyo kumafunikira. Potsatira chitsogozo cha Yehova, timachita nawo ntchito yake, osati kungoonerera. Ndipo amene akuchita ntchito ya Mulungu ndi anthu osangalala.—1 Akor. 3:9; Yak. 1:25.
16 Ganizani kwambiri za mmene mugwiritsire ntchito zinthu zimene mukuphunzira pamisonkhano ya mpingo. (Yoh. 13:17) Ndi mtima wanu wonse tumikirani Mulungu mwachangu. Chimwemwe chanu chidzasefukira. Moyo wanu udzasintha, udzakhala watanthauzo kwambiri. Inde, mudzapindula.