Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/00 tsamba 8
  • Misonkhano Imapindulitsa Achinyamata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Imapindulitsa Achinyamata
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakuthandizeni Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Mmene Tingapezere Chimwemwe Chochuluka mwa Kupezeka Pamisonkhano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Mmene Yehova Akutitsogolera
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 8/00 tsamba 8

Misonkhano Imapindulitsa Achinyamata

1 Mtsikana wina anati: “Nthaŵi zina ndimaganiza kuti achinyamata ndi amene amavutika kwambiri m’moyo. Timakhala pamodzi ndi anthu amene amachita chisembwere, amamwa mankhwala osokoneza bongo, ndiponso kumwa moŵa.” Kodi ndi mmene inu mumaganizira? Ngati ndi choncho, kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimene chingakuthandizeni kugonjetsa zisonkhezero zoipazi? Mufunika chikhulupiriro, kukhulupirira kwambiri kuti njira za Yehova n’zolondola, popeza popanda kutero “sikutheka kum’kondweretsa.” (Aheb. 11:6) Kupezeka pamisonkhano ya mpingo kudzakuthandizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu chachikristu ndi kutsimikiza mtima kwanu kupeŵa zoipa.

2 Misonkhano Imakupatsani Zambiri: Kodi n’chiyani chimapangitsa chakudya chokoma chodyera pamodzi ndi mabwenzi a pamtima kukhala chokoma kwambiri? Kodi si chifukwa chophatikiza chakudya chabwinocho ndi mayanjano abwino pamalo oduka mphepo? Ndithudi, misonkhano yathu imakhala ndi zabwino ngati zimenezi, kungoti izo zimakhala mwauzimu.

3 Zinthu zimene zimakambidwa pamisonkhano n’zolimbikitsa, kuyambira nkhani zokhudza mmene tingachitire ndi mavuto a tsiku ndi tsiku mpakana maphunziro abwino a maulosi a m’Baibulo. Amakambako malangizo abwino okuthandizani mmene mungakhalire ndi moyo wabwino ndi mmene mungagonjetsere mavuto amene mungakumane nawo. Mabwenzi opezeka kumisonkhano ndi abwino kwambiri, ndipo mkhalidwe wauzimu ndi wokondweretsa ndi wotetezeka. (Sal. 133:1) N’chifukwa chake mtsikana wina anati: “Ndimapita kusukulu nthaŵi zonse, ndipo imanditopetsa kwabasi. Koma misonkhano ili ngati chitsime chopezeka m’chipululu, kumene ndimakatsitsimulidwa kuti ndithe kupitanso kusukulu tsiku linalo.” Wina anati: “Ndaona kuti kucheza kwambiri ndi anthu amene amakonda Yehova kwandithandiza kuyandikana naye kwambiri.”

4 Mwa kulembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase, mumaphunzira kusonkhanitsa chidziŵitso cha m’Baibulo, kuchilemba kukhala nkhani, ndi kuikamba mokambirana kutsogolo kwa anthu mu Nyumba ya Ufumu. Tangolingalirani phindu lophunzitsidwa kuti tiphunzitse mwaluso choonadi chopulumutsa moyo cha m’Mawu a Mulungu! N’kutinso kumene achinyamata angapeze maphunziro apamwamba ngati ameneŵa?

5 Mmene Mungapindulire Kwambiri ndi Misonkhano: Kuti mupindule kwambiri ndi misonkhano, pali zinthu zitatu zofunika kuchita. Zinthu zimenezi ndizo kukonzekera, kutengamo mbali, ndi kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzira.

6 Ikonzekereni: Nthaŵi zonse khalani ndi nthaŵi yokonzekera misonkhano. Musalole homuweki, ganyu, kapena maseŵera kukudyerani nthaŵi imene mukufunika kukonzekera nkhani zimene zikakambidwe pamsonkhano uliwonse. Kukhala ndi chizoloŵezi chabwino kumathandiza. Chachikulu kwambiri ndicho kuyendera limodzi ndi ndandanda yoŵerenga Baibulo ya mlungu ndi mlungu ya m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Zimatenga mphindi zochepa chabe tsiku lililonse kuti muŵerenge ndi kusinkhasinkha pa machaputala operekedwawo. Patulani nthaŵi yoti mukonzekere Phunziro la Buku la Mpingo ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ena amachita zimenezi kutatsala tsiku limodzi kapena aŵiri kuti misonkhano ichitike. Mlungu uliwonse chitani zomwezi ndi nkhani za mu Msonkhano wa Utumiki, kumlingo umene mungathe.

7 Tenganimo Mbali: Baibulo limanena kuti Yesu ali ndi zaka 12 anapezeka m’kachisi, akumvetsera, kufunsa mafunso ndi kuyankha. (Luka 2:46, 47) Mwachidule, analoŵetsedwamo kwambiri. Mudzapindula kwambiri ndi misonkhano ngati muyesetsa kutengamo mbali.—Miy. 15:23.

8 Muyenera kuika mtima kwambiri pa zimene zikukambidwa pamisonkhano. Nthaŵi zina, kumvetsera nkhani kumakhala kovuta kulekana n’kukamba. Chifukwa? Maganizo anu atha kupita kwina pamene wina akulankhula. Kodi mungathetse bwanji zimenezi? Mwakulemba notsi. Lembani mfundo zofunika zimene mukufuna kukagwiritsa ntchito nthaŵi ina. Kulemba notsi kudzakuthandizani kuika maganizo anu papulogalamu. Komanso, santhulani malemba, ndipo ŵerengani malembawo pamene wokamba nkhani akuŵerenga.

9 Komanso, chikhale cholinga chanu kutengamo mbali m’kukambirana kwa mafunso ndi mayankho pamisonkhano. Mudzapindula kwambirinso ngati muganiziratu zimene mukufuna kunena. Miyambo 15:28 imati: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.”

10 Gwiritsani Ntchito Zimene Mukuphunzira: Chinthu chomaliza ndicho kuonetsetsa kuti zimene mukuphunzira “[zi]kugwira ntchito mwa inu.” (1 Ates. 2:13, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Pogwiritsa ntchito mfundo zabwino zimene mumaphunzira pamsonkhano uliwonse, mudzam’yandikira kwambiri Yehova Mulungu. Adzakhala pafupi nanu, ndipo mudzapeza chimwemwe chochuluka ndi chikhutiro popitiriza ‘kuyenda m’choonadi,’ ndi kuchipanga kukhala chanuchanu.—3 Yoh. 4.

11 Abale ndi alongo achinyamata, pamene mukonzekera misonkhano nthaŵi zonse, kutengamo mbali, ndi kugwiritsa ntchito zimene mukuphunzira, mudzasangalala kwambiri ndi misonkhano. Komanso, mudzapeza mapindu onse amene mungathe m’misonkhano. Chikhulupiriro chanu chidzalimba, monga mmene kutsimikiza mtima kwanu kukhalabe oona kwa Atate wanu wakumwamba, Yehova kudzachitira.—Sal. 145:18.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena