Mmene Tingapezere Chimwemwe Chochuluka mwa Kupezeka Pamisonkhano
1 Misonkhano ndi yofunika kwambiri pamoyo wathu wauzimu. Chimwemwe chimene timapeza pamisonkhano chimadalira zimene timachita tisanapite ku misonkhano, tili pamisonkhano ndi pamapeto pa misonkhano. Kodi tingadzithandize bwanji komanso ena kukhalabe achimwemwe kwambiri popezeka pamisonkhano?
2 Tisanapite ku Misonkhano: Chimwemwe chimene timapeza pamisonkhano chimadalira kwambiri kukonzekera. Tikakonzekera bwino, timakhala ofunitsitsa kumvetsera ndi kutengamo mbali. Komanso, nkhani iliyonse ya pamsonkhano imene tapatsidwa iyenera kukonzedwa bwino, kuti tipereke nkhaniyo molondola mogwirizana ndi malangizo ake komanso mopatsa chidwi omvetsera. Tiyenera kuikonzekera bwino. Pamene tichirikiza misonkhano kuti ikhale yosangalatsa ndi yomangirira komanso yopindulitsa aliyense, kupita kwathu patsogolo kumaonekera ndipo timakhala ndi chimwemwe chochuluka.—1 Tim. 4:15, 16.
3 Pamisonkhano: Kuyankha pamisonkhano kungatithandize kuti tisangalale nayo kwambiri. Nkhani zimene zimafuna omvetsera kutengamo mbali ziyenera kuonedwa monga nkhani imene aliyense mumpingo wapatsidwa. Kaŵirikaŵiri ndemanga zachidule ndi zosapita m’mbali ndizo zimakhala zogwira mtima kwambiri. Kuwonjezerapo mwachidule zokumana nazo zomangirira kungakhale kolimbikitsa, koma tiyenera kuonetsetsa kuti tikuzinena pamene nkhaniyo ikufuna zimenezo. (Miy. 15:23; Mac. 15:3) Pokamba nkhani pamsonkhano, tiyenera kulankhula mwamphamvu ndi mwachidaliro, kuchitira kuti nkhaniyo ikhale yosangalatsa, yosakokomeza ndi yothandiza.
4 Pamapeto pa Misonkhano: Kulankhulana mokoma mtima, kupatsana moni mwaubwenzi, ndi kukambirana mfundo zazikulu zimene zinakambidwa pamisonkhano kudzatipindulitsa. Kusonyeza chimwemwe chathu poona achinyamata, achikulire ndi achatsopano akutengamo mbali kumakulitsa chikondi chapaubale. M’malo monena zoipa za anthu amene alephera kufika pamisonkhano, tiyenera kugaŵana nawo chimwemwe chathu chimene tapeza mwa kupezekapo, tikumawalimbikitsa kupezekapo.—Aheb. 10:24, 25.
5 Tiyeni tisadzimane makonzedwe apadera ameneŵa ogaŵana chilimbikitso. (Aroma 1:11, 12) Mwa kuchita khama ndithu, tonse tingakhalebe achimwemwe popezeka pamisonkhano yachikristu.