Misonkhano ya Utumiki ya October
Mlungu Woyambira October 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 17: “Mawu Onse Aulosi a Mulungu Adzakwaniritsidwa!” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndipo kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani mfundo zingapo za m’buku latsopanoli zimene zimagogomeza kufunika kwa nthaŵi yathu.
Mph. 18: Khalani Ofunitsitsa Kugaŵira Magazini! Tchulani chiŵerengero chonse cha magazini amene mpingo unagaŵira mwezi watha. Kodi chiŵerengero chimenechi chikusiyana bwanji ndi chimene Sosaite inatumiza? Ngati pali kusiyana kwambiri, kodi pakufunika kuchitanji? Pemphani omvetsera kuthirira ndemanga pa mfundo zotsatirazi: (1) Wofalitsa aliyense ayenera kuoda magazini okwanira. (2) Onani Loŵeruka lililonse kukhala Tsiku la Magazini. (3) Mwezi uliwonse pa ndandanda yanu ya utumiki phatikizanipo kufalitsa magazini. (4) Konzani zochita umboni wamwamwayi mwa kugwiritsa ntchito magazini kuyamba kukambirana. (5) Perekani kwa ogwira ntchito komanso akatswiri ena magazini okhala ndi nkhani zapadera zokhudzana ndi ntchito yawo zimene mosakayikira angasangalale nazo. (6) Sungani polemba magazini amene mwagaŵira ndipo yambitsani njira za magazini, mukumapitako nthaŵi zonse ndi magazini atsopano. (7) Gwiritsani ntchito magazini alionse akale kuti asakuunjikireni. Onetsani magazini atsopano, ndipo sonyezani nkhani zimene mosakayikira zingakope chidwi. Wachikulire ndi wachinyamata apange chitsanzo chake aliyense komanso chachidule cha ulaliki wa magazini.—Onani mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 1995.
Nyimbo Na. 105 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Mmene Tingapezere Chimwemwe Chochuluka mwa Kupezeka Pamisonkhano.” Mafunso ndi mayankho. Tchulani zitsanzo zenizeni za mmene tingasonyezere kulingalira ena ndi kukhala wolimbikitsa ena pamisonkhano. Pemphani omvetsera kunena zitsanzo mwa zokumana nazo zawo.
Nyimbo Na. 152 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 18
Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi zokumana nazo za mu utumiki wakumunda.
Mph. 13: “Kodi Mukusamuka?” Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi mlembi. Pamene wofalitsa aona kuti n’koyenera kusamukira mpingo wina, n’kofunika kuti akhazikike bwinobwino kumalo achilendowo kupeŵa kufooka mwauzimu. Gogomezani kufunika kouza akulu za malingaliro ameneŵa komanso kuwapempha kutithandiza kudziŵitsa mpingo watsopano.
Mph. 22: “Kodi Mukanena Chiyani kwa Munthu Wachiyuda?” Mafunso ndi mayankho. Onetsani ulaliki wokonzekeredwa bwino. Ngati mungafune zowonjezereka za Chiyuda, onani buku la Kukambitsirana masamba 22-3.
Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 25
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Thandizani onse kukonzekera kugaŵira bolosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso m’November. Fotokozani mmene tingachitire ulaliki wokhudza funso lakuti, “Kodi Mulungu amayankha mapemphero?” Gwiritsani ntchito mfundo zopezeka m’phunziro 7 m’boloshalo kapena pamutu 16 ndime 12-14 m’bukulo. Chitani chitsanzo cha ulaliki wosavuta wokhala ndi lemba limodzi.
Mph. 15: Kupeza Mayankho a Mafunso a Baibulo. Mtumiki wotumikira wafikiridwa ndi wofalitsa amene wakumana ndi munthu wokondwerera yemwe wam’funsa funso la Baibulo. M’malo mongoyankha, mtumiki wotumikirayo akufotokoza mmene angapezere yankho. Choyamba, akupenda malingaliro opezeka m’Bukhu Lolangiza la Sukulu, phunziro 7, ndime 8-9. Ndiyeno, onse pamodzi akufufuza funso limene anthu m’gawo lawolo amakonda kufunsa. Akuyang’ana malifalensi amene amakamba za nkhaniyi ndi kupeza mfundo zokhutiritsa zimene zikumveketsa chifukwa chake yankho la Baibulolo lili choncho. Limbikitsani omvetsera kuchita phunziro lopindulitsa limeneli lofufuza mafunso a Baibulo.
Mph. 15: Zolinga Zimene Tingakhale Nazo. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Pendani zolinga zotheka zolembedwa m’bokosi la patsamba 11 mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1997. Limbikitsani kuchita nawo utumiki waupainiya wothandiza kapena wokhazikika. Fotokozani mmene kukwaniritsa zolinga zimenezi kungatipindulitsire. Pemphani omvetsera kusimba chimwemwe chimene anali nacho pamene anakwaniritsa zolinga zina zateokalase.
Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.