Mawu Onse Aulosi a Mulungu Adzakwaniritsidwa!
1 Nthaŵi zonse Mboni za Yehova zimachita chidwi ndi ulosi wa Baibulo. Chotero tinasangalala kuona kuti mutu wa msonkhano wachigawo wa chaka chino unali wakuti “Mawu Aulosi a Mulungu.” Tinali ofunitsitsa kudziŵa zimene Yehova watikonzera monga “zakudya panthaŵi yake.” (Mat. 24:45) Ndipo sanatikhumudwitse.
2 Mfundo Zazikulu za Msonkhano: Lachisanu nkhani yaikulu yakuti, “Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu,” inanenanso nkhani yopatsa chidziŵitso ya kusandulika. (Mat. 17:1-9) Inagogomeza kuti tsopano lino tili kuchiyambi kwa nthaŵi yabwino kwambiri popeza kuti tili mkati ndithu, mkati mwenimweni mwa nthaŵi ya mapeto, ndipo dongosolo latsopano lili pafupi pompa! Njira yabwino yolabadirira Mawu a Mulungu ndi mwa kuwaŵerenga nthaŵi zonse. Nkhani yosiyirana yakuti “Sangalalani ndi Kuŵerenga Mawu a Mulungu” inapereka malingaliro othandiza a mmene tingapangire kuŵerenga kwathu Baibulo kukhala kwa phindu ndi kosangalatsa.
3 Loŵeruka masana tinapenda zifukwa zake tiyenera kukhulupirira kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Kodi zonsezi mungazikumbukire? Lamlungu mmaŵa, ulosi wa Habakuku unali wosangalatsa kwambiri popeza tinaphunzira kuti masiku athu akufanana kwambiri ndi masiku ake ndi kuti zochitika zofunika zimenezo zili pafupi, pamene Yehova adzawononga oipa ndi kupulumutsa olungama. Kodi paseŵero la m’Baibulo la Yakobo ndi Esau munatolapo mfundo? Tiyenera kufuna madalitso kwa Yehova, ndi kukaniza mzimu wosasamala ndi wopanda chidwi.
4 Buku Latsopano Losangalatsa Kwambiri: Si mmene tinasangalalira kulandira buku latsopano lakuti, Pay Attention to Daniel’s Prophecy! Mosakayika inu amene mumaŵerenga ndi kumva Chingelezi mwayamba kale kuŵerenga buku losangalatsali. M’lankhuli amene analengeza kutulutsidwa kwa bukuli anati: “Kungopatula mbali zochepa zokha, maulosi onse a m’buku la Danieli akwaniritsidwa.” Kodi zimenezi sizikutsimikizira kuti nthaŵi ikufulumira masiku athu ano?
5 Pologalamu ya msonkhano yalimbitsa kwambiri chidaliro chathu chakuti malonjezo onse a Mulungu amene pakalipano sanakwaniritsidwe adzakwaniritsidwa. Tikulimbikitsidwa kupitirizabe kulengeza mawu aulosi a Mulungu kwa ena!