Kodi Mukanena Chiyani kwa Mhindu?
1 Monga mukudziŵa, Ahindu ambiri akukhala m’mayiko osiyanasiyana, kuphatikizapo lino. Izi zikutanthauza kuti posachedwa mu utumiki wanu mudzakumana ndi Mhindu. Ngati zatero, kodi mungalalikire bwanji?
2 Kumbukirani Mfundo Izi: Amishonale amene akhoza kulalikira kwa Ahindu akuti simufunikira kuphunzira mozama za Chihindu kuti mupereke umboni wogwira mtima. Ulaliki wosavuta kumva wa choonadi kaŵirikaŵiri umachititsa anthu kumvetsera kwambiri. Choyamba pemphani kulankhula ndi bambo wa nyumbayo. Ngati iye akufuna, kukakhala kosavuta kuchitira umboni anthu ena a m’banjamo. Poyamba penipeni, peŵani kupereka lingaliro lakuti mwabweretsa uthenga woposa zimene mwininyumbayo amakhulupirira kapena kuti mukufuna kukambirana za Mulungu yekha woona kapenanso za malemba opatulika akale kwambiri. Popeza Ahindu ambiri amaona Baibulo kukhala buku la Azungu, mungathetse malingaliro ameneŵa mwa kufotokoza kuti silimachirikiza utsamunda kapena kukweza mtundu wina pamwamba pa wina.
3 Gwiritsani Ntchito Zida Zoyenera: Mabolosha aŵiri akonzedwera makamaka Ahindu. Why Should We Worship God in Love and Truth? lili m’Chigujarati ndi m’Chipunjabi. Our Problems—Who Will Help Us Solve Them? lili m’zinenero zina 11 zachiindiya. Mabolosha aŵiriŵa alinso m’Chingelezi. Bolosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano” ndi Kodi Mulungu Amatisamaliradi? alinso oyenera kwambiri pochitira umboni kwa Ahindu. Bolosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso zingagwiritsidwe ntchito bwino kwambiri pochititsa maphunziro a Baibulo.
4 Kambani Zimene Mungagwirizane: Si kovuta kupeza zimene mungagwirizane ndi Ahindu. Amakhulupirira kuti tikukhala m’masiku amene kuipa kwafika poipa kwambiri ndi kuti Mulungu adzachotsa mavuto a dziko lonse kupyolera m’chiwonongeko choopsa chimene chidzadzetsa nthaŵi ya choonadi. Mutha kuona mmene mungagwirizanitsire zikhulupiriro zimenezi ndi ziphunzitso za Baibulo zonena za masiku otsiriza, chisautso chachikulu, ndi dziko latsopano limene likudzalo. Popeza Ahindu ambiri amaona moyo kukhala wamavuto opanda zothetsera, amachita chidwi ndi nkhani za moyo wa banja, upandu ndi chisungiko, komanso zimene zimachitika pa imfa. Nazi zitsanzo ziŵiri za ulaliki zimene mungayese.
5 Izi zingasangalatse mwamuna wapabanja:
◼ “Ndikuchezera anthu amene akuda nkhaŵa ndi mmene moyo wa banja ulili m’mayiko ambiri lerolino. Kodi muganiza kuti ndi chiyani chimene chingathandize mabanja kugwirizana? [Yembekezani yankho.] Anthu ena amadziŵa zimene malemba achihindu amanena pa zabanja, koma sanakhaleko ndi nthaŵi yoziyerekezera ndi zomwe Baibulo limanena pankhaniyi. Ndikufuna kukusonyezani mfundo imene ili pa Akolose 3:12-14.” Mukatha kuŵerenga lembali, muonetseni mwininyumba mutu 15 wa m’buku la Chidziŵitso ndipo nenani kuti: “Ndikufuna kuŵerenga nanu mutu uwu kwa nthaŵi yochepa chabe.”
6 Wachinyamata angamvetsere izi:
◼ “Mosakayikira umakhulupirira Mulungu. Ulingalira kuti chifuno cha Mulungu kwa ife n’chiyani?” Yembekezani yankho. Ndiyeno ŵerengani Genesis 1:28, ndipo nenani kuti: “Madera ambiri padziko lapansi ali ndi anthu ambiri komanso ali ndi mavuto ochuluka. Kodi muganiza kuti Mlengi angafune kutithandiza kuthetsa mavuto athu?” Mukamva yankho, muonetseni buku loyenera.
7 Sangalalani ndi Zotsatira Zabwino: Mwamuna wina wachihindu wazaka 22 anafikira mlongo amene anali kuchitira umboni pamsika nam’pempha kuphunzira naye Baibulo. Mwamunayo anafotokozera mlongoyo kuti kwa zaka zisanu ndi zitatu zapitazo ankamva mobera makambirano a Baibulo a mlongoyo ndi mayi ake a mwamunayu. Ngakhale kuti anachita chidwi ndi mayankho omveka bwino a Baibulo a mavuto a mtundu wa anthu, mayi ake sanasangalale ndipo mnyamatayo ankaganiza kuti anali wamng’ono kuyamba chipembedzo chakechake. Tsopano popeza ndi wamkulu, anafuna kuti aphunzire zambiri. Mnyamatayu sanataye nthaŵi. M’masiku 23 okha, anamaliza kuphunzira buku la Chidziŵitso, ndipo patangopita miyezi inayi chikumanireni ndi mlongo uja kumtsika anapempha kuti abatizidwe!
8 Mbale wina anayamba phunziro ndi mwamuna wina wachihindu amene anakumana naye m’sitima ya pamtunda. Mwamunayu anali ndi mavuto m’banja. Analinso ndi vuto la uchidakwa. Iye anavomereza kuti Mboniyo idzamuyendere ndi kumuuza malangizo a Baibulo a moyo wa banja. Ziphunzitso za Baibulo za makhalidwe abwino zinam’sangalatsa kwambiri, ndipo anavomereza phunziro la Baibulo. Iye ndi banja lake onse anayamba kupezeka pamisonkhano. Kenako, iwo anauza choonadi mabwenzi ndi achibale. Panopo, asanu ndi mmodzi mwa anthu ameneŵa alandira choonadi!
9 Chifuno cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Tim. 2:4) Izi zikuphatikizapo amuna ndi akazi amene ali m’zipembedzo zimene si zachikristu, monga Chihindu. Ngati kuli Ahindu m’gawo lanu, bwanji osawafikira mwamsanga ndi kugwiritsa ntchito ena mwa malingaliro operekedwa m’nkhani inowa?