Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndinu wokonzekera matenda aakulu?
M’dziko lamakonoli, “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zimayendera limodzi kaŵirikaŵiri kuyambitsa matenda aakulu, kuphatikizapo chikakamizo choti atiike magazi. (Mlal. 9:11, NW) Kuti tikhale okonzekera tsoka ngati limenelo, Yehova wapereka thandizo m’njira zambiri kupyolera m’gulu lake, koma amafuna kuti ife tichite mbali yathu. Pansipa pali mpambo wokuthandizani kuchita zimenezo.
• Nthaŵi zonse nyamulani khadi latsopano la Chidziŵitso kwa Dokotala/Chommasula ku Mlandu.
• Onetsetsani kuti ana anu anyamula Khadi la Ana latsopano.
• Bwereranimo m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 1995, mukumayesera mmene mungakambirane ndi madokotala ndi oweruza ponena za mankhwala amene mukufuna kaamba ka mwana wanu.
• Bwereranimo m’nkhani zofotokoza mbali za magazi ndi mankhwala ena m’malo mwa magazi. (Makamaka: Nsanja ya Olonda ya October 1, 1994, tsamba 31; June 1, 1990, masamba 30-1; March 1, 1989, masamba 30-1; Galamukani! yachingelezi ya December 8, 1994, masamba 23-7; August 8, 1993, masamba 22-5; ya December 8, 1991 yachicheŵa, tsamba 28; ndi m’mphatika za Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 1995 ndi September 1994. Zisungeni m’faelo kuti zisamavute kupeza.)
• Gamulani ndi chikumbumtima chabwino ngati mudzalola kugwiritsa ntchito makina amene amayendetsa magazi kunja kwa thupi kapena ngati mungalandire mankhwala ophatikizapo mbali zina za magazi.
• Musanapite ku chipatala, ngati n’kotheka, dziŵitsani akulu kuti akuchirikizeni komanso kuti athe kulankhulana ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala (HLC) patakhala kufunikira kotero. Ponena za mwana wamng’ono, pemphani akulu kudziŵitsa HLC mwamsanga.
Nenetsani Kuti Simukufuna Magazi: Malipoti akusonyeza kuti abale ndi alongo ena amayembekezera kufikira zinthu zitaipa kuti auze madokotala kuti sakufuna magazi. Zimenezi si chilungamo kwa madokotalawo ndipo zimakuikani pangozi yakuti akhoza kukuikani magazi. Madokotala akadziŵa za zikhulupiriro zanu ndi kuti muli ndi mapepala osainidwa ochirikiza zofuna zanu amenenso ali ndi malangizo omveka, zimawathandiza kupitiriza ndi ntchito yawo popanda kuzengereza ndipo nthaŵi zambiri amakhala ndi mpata waukulu wogwiritsa ntchito mankhwala ena osaphatikizapo magazi.
Popeza kuti matenda aakulu angabuke nthaŵi iliyonse, kaŵirikaŵiri pamene simukuyembekezera, chitanipo kanthu tsopano kudziteteza inuyo ndi ana anu kuti musaikidwe magazi.—Miy. 16:20; 22:3.