Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 3/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 3/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi Mboni za Yehova zimalola kugwiritsira ntchito mwazi wa autologous (kudzithira mwazi), monga ngati kulola mwazi wawo kusungidwa ndipo pambuyo pake kubwezeredwa mwa iwo?

Ogwira ntchito a za mankhwala kaŵirikaŵiri amasiyanitsa pakati pa mwazi wa homologous (wochokera kwa munthu wina) ndi mwazi wa autologous (mwazi wotulutsidwa mwa munthu wodwala mwiniyo). Chiri chodziŵika bwino lomwe kuti Mboni za Yehova sizimalandira mwazi wochokera kwa anthu ena. Koma bwanji ponena za kugwiritsira ntchito mwazi wa autologous, liwu logwiritsiridwa ntchito ponena za njira zosiyanasiyana?

Zina za njira zimenezo ziri zosalandirika kwa Akristu chifukwa cha kukhala mowonekera bwino zowombana ndi Baibulo, koma zina zimatsogolera ku mafunso. Ndithudi, pa nthaŵi imene Baibulo linalembedwa, kuthiridwa mwazi ndi kugwiritsira ntchito kwina kwa mankhwala kwa mwazi koteroko kunali kosadziŵika. Komabe, Mulungu anapereka zitsogozo zimene zinatheketsa atumiki ake kusankha kaya ngati njira zina za mankhawala zoloŵetsamo mwazi sizingamkondweretse iye.

Kugamulapo kwa Mulungu kuli kwakuti mwazi umaimira moyo ndipo chotero uli wopatulika. Iye analamula kuti palibe munthu amene akayenera kuchirikiza moyo wake mwa kudya mwazi. Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; . . . Koma nyama,mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.” (Genesis 9:3, 4; Levitiko 7:26, 27) Mogwirizana ndi Mpatsi wa Moyo, kugwiritsira ntchito mwazi kololedwa kokha kunali popereka nsembe: “Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa lansembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.”​—Levitiko 17:11, 12.

Ngakhale kuti Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose, Baibulo limanena kuti chiri “chofunikira” kaamba ka ife ‘kusala mwazi,’ kuwona iwo monga wopatulika. (Machitidwe 15:28, 29) Ichi chiri chomveka, popeza kuti nsembe pansi pa Chilamulo zinachitira chithunzi mwazi wa Kristu, njira ya Mulungu mwa imene tingapezere moyo wosatha.​—Ahebri 9:11-15, 22.

Kodi mwazi unayenera kuchitidwa motani pansi pa Chilamulo ngati unayenera kugwiritsiridwa ntchito m’nsembe? Timaŵerenga kuti ngati wosaka nyama anapha nyama kaamba ka chakudya, “azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi.” (Levitiko 17:13, 14; Deuteronomo 12:22-24) Chotero mwazi sunayenere kugwiritsiridwa ntchito monga chakudya kapena njira inayake. Ngati unatengedwa kuchokera m’cholengedwa ndipo sunagwiritsiridwe ntchito m’nsembe, unayenera kutayidwa pansi, chopondapo mapazi cha Mulungu.​—Yesaya 66:1; yerekezani ndi Ezekieli 24:7, 8.

Ichi mowonekera chimachotsapo kugwiritsira ntchito kwa mwazi kumodzi kofala kwa mwazi wa autologous​—kutengedwa kwa mwazi kutumbula kusadakhale, kusungidwa, ndipo pambuyo pake kuthiridwa mwazi wa wodwala iyemwiniyo. M’njira yotereyo, chomwe chimachitidwa ndi ichi: Kutumbulidwa kosankhidwa kusanachitike, mbale zina za mwazi wonse wa munthu zimasungidwa kapena ma red cells (maselo ofiira) amapatulidwa, kuziziritsidwa, ndi kusungidwa. Keneka ngati chiwoneka kuti wodwalayo afunikira mwazi mkati mwa kapena kutsatira kutumbulidwako, mwazi wa iyemwini wosungidwa ungabwezeretsedwe mwa iye. Nkhaŵa za nthaŵi ino ponena za matenda a mwazi wa m’mafupa zachititsa kugwiritsira ntchito kwa mwazi wa autologous kumeneku kukhala kofala. Mboni za Yehova, ngakhale ndi tero, SIZIMALANDIRA njirayi. Tazindikira kwa nthaŵi yaitali kuti mwazi wosungidwa woterowo sulinso mbale ya munthuyo. Iwo wachotsedwa kotheratu kuchoka kwa iye, chotero uyenera kutayidwa m’chiyang’aniro ndi Lamulo la Mulungu lakuti: “Muuthire pansi ngati madzi.”​—Deuteronomo 12:24.

M’njira yosiyanako, mwazi wa autologous ungapatutsidwe kwa wodwalayo kuloŵa m’chiwiya cha hemodialysis (imso wamba yopangidwa) kapena pompi ya mtima ndi mapapo. Mwazi umatuluka kupyola mu kachubu kupita ku chiwalo chopangidwa chimene chimapompa ndi kusunza (kapena kuika mpweya womwe timaloŵetsa mkati popuma) mu iwo, ndipo kenaka umabwerera ku dongosolo la kuyenda kwa mwazi la wodwalayo. Akristu ena alola ichi ngati chiwiyacho sichikutsogozedwa ndi mwazi wosungidwa. Iwo awona kuika chubu kwakunjako kukhala kutalikitsa dongosolo lawo la kuyenda kwa mwazi kotero kuti mwazi ungapite kupyola mu chiwalo chopangidwa. Iwo alingalira kuti mwazi m’njira yotsekeredwa imeneyi udakalibe mbali ya iwo ndipo sunafunikire ‘kuthiridwa pansi.’a

Bwanji, ngakhale ndi tero, ngati kuyenda koteroko kwa mwazi wa autologous kunaleka mwachidule, monga ngati makina a mtima ndi mapapo atsekeka pamene sing’angayo akufufuza umphumphu wa coronary-by-pass grafts (dongosolo lopatutsira mwazi)?

M’chenicheni, chigogomezero cha Baibulo sichiri pa nkhani ya kuyenda kwa mwazi kosalekeza. Ngakhale kusiyapo nkhani ya kutumbula, mtima wa munthu ungaleke mwachidule ndipo kenaka kuyambanso.b Dongosolo lake la kuyenda kwa mwazi silingafunikire kuchotsedwa mwazi ndi kutayidwa kokha chifukwa chakuti kutenda kwa mwazi kunali kutalekeka mkati mwa kumangika kwa mtima. Chotero, Mkristu wofunikira kusankhapo kaya akalola mwazi wake kupatutsidwa kupyola m’chiwiya cha kunja kwa thupi ayenera kusumika, osati kwakukulukulu pa kaya kulekeka kwachidule kukachitika m’kuyenda kwa mwazi, koma kaya ngati iye mwa chikumbumtima anadzimva kuti mwazi wopatutsidwawo ukakhalabe mbali ya dongosolo lake la kuyenda kwa mwazi.​—Agalatiya 6:5.

Bwanji ponena za kusungunula mwazi kochititsidwa? Asing’anga ena otumbula amakhulupirira kuti chiri cha phindu kaamba ka mwazi wa wodwala kusungunulidwa mkati mwa kutumbula. Chotero, kumayambiriro kwa kutumbula, amatsogoza mwazi wina ku matumba osungiramo kunja kwa thupi la wodwala ndi kuwuloŵa m’malo ndi mtundu wina wa madzi opanda mwazi; pambuyo kape, mwaziwo umaloledwa kuyenda kuchokera m’matumba osungiramowo kubwereranso m’thupi la wodwalayo. Popeza kuti Akristu samalola mwazi wawo kusungidwa, asing’anga ena atenga njirayi, akumakonza ziwiya mtsatanetsatane amene ali wolumikizidwa mosalekeza ku dongosolo la kuyenda kwa mwazi la wodwalayo. Akristu ena alandira chimenechi, ena akana. Kachiŵirinso, aliyense payekha ayenera kugamulapo kaya ngati akalingalira mwazi wopatutsidwa mtsatanetsantane wosungunula mwazi woterowo kukhala wofanana ndi uja woyenda kupyola mu makina a mtima/​mapapo, kapena akalingalira iwo kukhala mwazi umene unamusiya ndipo motero uyenera kutayidwa.

Chitsanzo chomalizira cha kugwiritsira ntchito mwazi wa autologous chimalowetsamo kutenga ndi kugwiritsiranso ntchito mwazi mkati mwa kutumbula. Ziwiya zimagwiritsiridwa ntchito kutulutsa mwazi kuchokera pa chironda, kuwupompa iwo kupyola m’chosunzira (kuchotsa mwazi wowumirira kapena zidutswa) kapena chiwiya cha centrifuge (kuchotsa madzi), ndipo kenaka kuwubweza kuloŵanso mwa wodwalayo. Akristu ambiri akhala odera nkhaŵa kwambiri kuti kaya m’njira yoteroyo mungakhale kulekeka kwachidule kulikonse m’kuyenda kwa mwazi. Komabe, monga momwe kwatchulidwira, nkhaŵa yowonjezereka ya Baibulo iri kaya mwazi wolowa pa chironda chotumbulidwacho udakali mbale ya munthuyo. Kodi chenicheni chakuti mwaziwo wayenda kuchokera m’dongosolo lake la kuyenda kwa mwazi kuloŵa m’chironda chimatanthauza kuti uyenera ‘kutayidwa,’ monga mwazi wotchulidwa pa Levitiko 17:13? Ngati munthu akhulupirira tero, iye mothekera angakane kulola thandizo la mwazi loterolo. Komabe, Mkristu wina (yemwe sakalola mwazi wake kutuluka kuchoka mwa iye, kusungidwa kwa kanthaŵi, ndipo pambuyo pake kuikidwanso mwa iye) Angamalize kuti tsatanetsatane wokhala ndi mwazi wochiritsira kuchokera ku malo otumbulira ndi kuloŵetsanso kwa mwazi kochitidwa sikungalakwire chikumbumtima chake chophunzitsidwa.

Monga mmene tikuwonera, pali kusiyanasiyana komakula kwa ziwiya zogwiritsira ntchito kapena maluso olowetsamo mwazi wa autologous. Sitingathe ndipo sitiyenera kuyesa kupereka ndemanga pa kusiyana kulikonse. Pamene tiyang’anizana ndi funso m’mbaliyi, Mkristu aliyense ali ndi thayo kupeza tsatanetsatane kochokera kwa ogwira ntchito a za mankhwala ndipo kenaka kupanga chosankha chaumwini.

Ngakhale kuti zambiri zanenedwa ponena za mbali za zamankhwala, chimene chiri chofunika mokulira koposa chiri nkhani za chipembedzo. Pamene Mkristu akuthetsa zikaikiro zirizonse kapena mafunso ponena za njira zamankhwala zoloŵetsamo mwazi, chimene chiyenera kukhala cholamulira chiri chakuti ayenera kusonyeza chikhulupiriro, kuti amalemekeza lamulo la Mulungu la ‘kusala mwazi,’ ndipo kuti amasungirira chikumbumtima chabwino. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti njira yaikulu koposa mu imene miyoyo ingapulumutsidwe mdi mwazi siiri m’zopangapanga za mankhwala koma kupyolera mwa mphamvu yopulumutsa ya mwazi wa Kristu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiri ndi mawomboledwe mwa mwazi wake.” (Aefeso 1:7; Chibvumbulutso 7:14, 17) Pamene kuli kwakuti mankhwala amakono angatithandize kutalikitsa miyoyo yathu kwa kanthaŵi, mosakaikira sitikafuna kutalikitsa moyo wathu wa nthaŵi ino mwa kuchita chirichonse chimene chikalakwira chikumbumtima chathu Chachikristu kapena kusakondweretsa Mpatsi wathu wa Moyo.​—Mateyu 16:25; 1 Timoteo 1:18, 19.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda, June 15, 1978, tsamba 30, (Chingelezi).

b Ichi chingatulukepo kuchokera ku nthenda ya mtima, kukanthidwa ndi magetsi, kapena kuzizira kopambanitsa kwa thupi, konga ngati kumizidwa m’madzi ozizira kwambiri.

[Chithunzi patsamba 31]

Ndi chiwiya cha mtima ndi mapapo, dongosololo limaphatikizapo: (1) kuyika chubu kuchokera ku dongosolo la mitsempha ya mwazi; (2) mapompi okoka mwazi ochiritsira; (3) chiwiya chopereka mpweya womwe timaloŵetsa popuma; (4) chiwiya cha mphako chosunzira mwazi; (5) pompi yaikulu yobweza mwazi; (6) njira yobwerera ku dongosolo la kuyenda kwa mwazi la wodwala

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena