Mwazi—Wofunika Koposa Kaamba ka Moyo
Kodi mwazi ungapulumutse motani moyo wanu? Mosakayikira zimenezi nzokukondweretsani chifukwa chakuti mwazi ngogwirizanitsidwa ndi moyo wanu. Mwazi umatengera okosijeni m’thupi lanu lonse, umachotsa kalaboni dayokosaidi, umathandizana ndi masinthidwe a kunja, ndipo umathandiza m’kumenyana kwanu ndi nthenda.
Mgwirizano wa moyo ndi mwazi unapangidwa kalekale William Harvey asanafotokoze dongosolo lozungulira la mwazi mu 1628. Malamulo aakulu akhalidwe a zipembedzo zazikulu amasonyeza Wopatsa Moyo, amene anafotokoza ponena za moyo ndi ponena za mwazi. Loyala wina Mkristu Wachiyuda anati ponena za iye: “Iye mwini amapatsa anthu onse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse. Pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda ndi kukhalako.”a
Anthu amene amakhulupilira Wopatsa Moyo woteroyo amadalira kuti zitsogozo zake ziri kaamba ka ubwino wathu wosatha. Mneneri wina Wachihebri anamfotokoza kukhala “Iye wokuphunzitsa kuti upindule, Iye wokuchititsa kuyenda mmene uyenera kuyendamo.”
Chitsimikiziro chimenecho, pa Yesaya 48:17, (NW) chiri mbali ya Baibulo, bukhu lolemekezedwa chifukwa cha miyezo ya makhalidwe imene ingapindulitse tonsefe. kodi limanenanji ponena za kugwiritsidwa ntchito kwa anthu mwazi? Kodi limasonyeza mmene miyoyo ingapulumutsidwire ndi mwazi? Kwenikweni, Baibulo limasonyeza momvekera bwino kuti mwazi uli woposa madzi a moyo okhala ndi zambiri. Limatchula mwazi nthaŵi zoposa 400, ndipo zisonyezero zina za zimenezi zimaphatikizapo kupulumutsidwa kwa moyo.
M’chisonyezero china choyambilira, Mlengi analengeza kuti: “Chirichonse chimene chiri ndi moyo ndi kuyendayenda chidzakhala chakudya chanu. . . . Koma simuyenera kudya nyama imene iri ndi mwazi wake wamoyo mkati mwake.” Iye anatinso: “Ponena za mwazi wanu wamoyo ndidzakufunsanidi kufotokoza,” ndipo iye kenako anatsutsa mbanda. (Genesis 9:3-6, New International Version) Iye ananena zimenezo kwa Nowa, kholo la onse lolemekezedwa kwambiri ndi Ayuda, Asilamu, ndi Akristu. Motero anthu onse anauzidwa kuti m’lingaliro la Mlengi, mwazi umaimira moyo. Zimenezi zinali zoposa lamulo la zakudya. Mwachiwonekere lamulo la khalidwe linaphatikizidwa. Mwazi wamunthu uli ndi tanthauzo lalikulu ndipo suyenera kuipsidwa. Pambuyo pake Mlengi anawonjezera zinthu zimene tingawone mosavuta nkhani zamakhalidwe amene iye amagwirizanitsa ndi mwazi wamoyo.
Iye kachiŵirinso anatchula mwazi pamene anapereka mpambo Wachilamulo kwa Israyeli wakale. Pamene kuli kwakuti anthu ambiri amalemekeza nzeru ndi makhalidwe mumpambo umenewo, ochepereka amazindikira malamulo ake aakulu onena za mwazi. Mwachitanzo: “Ngati aliyense wa nyumba ya Israyeli kapena wa alendo amene akukhala pakati pawo adya mwazi uliwonse, ndidzayang’aniza nkhope yanga pa munthu amene akudya mwazi ndipo ndidzamdula kumchotsa pakati pa anthu a kwake. Pakuti moyo wa nyama uli m’mwazi.” (Levitiko 17:10, 11, Tanakh) Pamenepo Mulungu anafotokoza zimene wosaka nyama anayenera kuchita ndi nyama yakufa: “Iye adzakhetsa mwazi wake ndi kuufotsera ndi dothi. . . . Simuyenera kudya mwzi wa nyama iriyonse, pakuti moyo wa nyama iriyonse ndiwo mwazi wake. Aliyense wa kuudya adzadulidwa.”—Levitiko 17:13, 14, Ta.
Asayansi tsopano amadziŵa kuti mpambo Wachilamulo Wachiyuda unapititsa patsogolo umoyo wabwino. Mwachitsanzo, unafunikiritsa kuti, tudzi tikumbiridwe kunja kwa msasa ndi kufotseredwa ndi kuti anthu asadye nyama imene inali ndi kuthekera kwakukulu kwa nthenda. (Levitiko 11:4-8, 13; 17:15; Deuteronomo 23:12, 13) Pamene kuli kwakuti lamulo lonena za mwazi linali ndi mbali ya zathanzi, zina zochuluka zinaphatikizidwapo. Mwazi unali ndi tanthauzo lophiphiritsira. Unaimira moyo woperekedwa ndi Mlengi. Mwakuwona mwazi kukhala wapadera, anthuwo anasonyeza chidaliro pa iye kaamba ka moyo. Inde, chifukwa chachikulu chifukwa chake iwo sanayenera kudya mwazi chinali chakuti, osati kuti unali woipa, koma kuti unali ndi tanthauzo lapadera kwa Mulungu.
Mobwerezabwereza Chilamulocho chinafotokoza chiletso cha Mlengi pakudya mwazi kuchirikiza moyo. “Musadya mwazi; utayireni pansi ngati madzi. Musaudye, kotero kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana apambuyo panu, chifukwa chakuti mudzakhala mukuchita chimene chiri chabwino.”—Deuteronomo 12:23-25, NIV; 15:23; Levitiko 7:26, 27; Ezekieli 33:25.b
Mosiyana ndi mmene ena amalingalilira lerolino, lamulo la Mulungu pamwazi siliyenera kunyalanyazidwa kokha chifukwa chakuti ngozi inabuka. Mkati mwa vuto la nthaŵi yankhondo, asilikali Achiisrayeli ena anapha nyama “nazidya ziri ndi mwazi wawo.” Polingalira ngoziyo, kodi kunali kololeka kwa iwo kuchirikiza miyoyo yawo ndi mwazi? Ayi. Mtsogoleri wawo anasonyeza kuti njira yawo inali ya cholakwa chachikulube. (1 Samueli 14:31-35) Chifukwa cha chimenecho, moyo monga momwe uliri wamtengo wapatali, Wopatsa Moyo wathu sananene kuti miyezo yake ikatha kunyalanyazidwa m’ngozi.
MWAZI NDI AKRISTU OWONA
Kodi Chikristu chimaima pati pankhani ya kupulumutsa moyo waumunthu ndi mwazi?
Yesu anali mwamuna waumphumphu, ndicho chifukwa chake iye akulemekezedwa kwambiri. Iye anadziŵa kuti Mlengi ananena kuti kudya mwazi kunali kolakwa ndi kuti lamulo limeneli linali logwira ntchito. Chifukwa cha chimenecho, pali chifukwa chabwino cha kukhulupilira kuti Yesu akachirikiza lamulo lonena za mwazi ngakhale ngati iye anali pansi pa chitsenderezo cha kuchita mwanjira ina. Yesu “sanachite cholakwa, [ndipo] palibe chinyengo chimene chinapezedwa pamilomo yake.” (1 Petro 2:22, Knox) Motero iye anakhazikitsira chitsanzo otsatira ake, kuphatikizapo chitsanzo cha kulemekeza moyo ndi mwazi. (Tidzalingalira pambuyo pake mmene mwazi wa Yesu mwini ukuphatikizidwira m’nkhani yofunika imeneyi yokhudza moyo wanu.)
Wonani chimene chinachitika pamene, zaka zingapo imfa ya Yesu itachitika, funso linabuka lakuti kaya munthu wokhala Mkristu anafunikira kusungu malamulo onse a Israyeli. Limeneli linakambitsiridwa paupo wa bungwe lolamulira Lachikristu, limene linaphatikizapo atumwi. Mbale wa atate wina wa Yesu Yakobo anasonyeza malembo okhala ndi malamulo onena za mwazi onenedwa kwa Nowa ndi kumtundu wa Israyeli. Kodi amenewo akakhala akugwira ntchito pa Akristu?—Machitidwe 15:1-21.
Upo umenewo unatumiza chosankha chawo kumipingo yonse: Akristu safunikira kusunga mpambo wa malamulo operekedwa kwa Mose, koma “nkofunikira” kwa iwo “kuleka kusala zinthu zoperekedwa nsembe kumafano ndi kusala mwazi ndi zinthu zopotoledwa [nyama yosakhetsedwa mwazi] ndi kusala chisembwere.” (Machitidwe 15:22-29, NW) Atumwiwo sanali kokha kupereka lamulo la mwambo kapena la zakudya. Lamulolo linakhazikitsa chitsanzo cha makhalidwe ofunika, chimene Akristu oyambilira anatsatira. Pafupifupi zaka khumi nsembe kumafano ndiponso kusala mwazi . . . ndi kusala chisembwere.”—Machitidwe 21:25.
Mukudziŵa kuti mamiliyoni a anthu amapita kumatchalitchi. Ambiri a iwo mwinamwake akavomereza kuti makhalidwe Achikristu amaphatikizapo kusalambira mofano ndi kusachita chigololo. Komabe, nkoyenerera kuti tizindikire kuti atumwiwo anaika kupeŵa mwazi pamlingo wapamwamba wofananawo ndi kupeŵa zolakwa zimenezo. Lamulo lawo linamaliza ndi kuti: “Ngati mudziletsa mosamalitsa kuzinthu zimenezi, mudzachita bwino. Thanzi labwino kwa inu!”—Machitidwe 15:29, NW.
Lamulo la atumwi linazindikiridwa kale kukhala lomanga. Eusebius amasinba za mkazi wina wachichepere pafupi ndi mapeto a zaka za zana lachiŵiri amene, asanafe ndi chizunzo, ananena mawu akuti Akristu “samaloledwa kudya mwazi ngakhale wa nyama zosalingalira.” Iye sanali kugwiritsira ntchito kuyenera kwa kufa. Iye anafuna kukhala ndi moyo, koma iye sakanaleka ziphunzitso zake. Kodi inu simukulemekeza awo amene amaika chiphunzitso pamwamba pa phindu lawo?
Wasayansi Joseph Priestley anati: “Chiletso cha kudya mwazi, choperekedwa kwa Nowa, chimawonekera kukhala chomanga pambadwa zake zonse . . . Ngati titanthauzira chiletso cha atumwi[cho] ndi kachitidwe ka Akristu oyambirira, amene sangalingaliridwe kukhala asakuzindikira moyenera mtundu ndi ukulu wake, ife sitingachitire mwina kusiyapo kunena kuti, chimenecho chinalinganizidwa kukhala chotheratu ndi chachikhalire; pakuti mwazi sunadyedwe ndi Akristu alionse kwa zaka mazana ambiri.”
BWANJI ZA KUGWIRITSIRA NTCHITO MWAZI MONGA MANKHWALA?
Kodi chiletso Chabaibulo pamwazi chikaphatikizapo kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala, monga ngati kuthiriridwa mwazi, kumene ndithudi kunali kosadziŵika m’nthaŵi ya Nowa, Mose, kapena atumwi?
Pamene kuli kwakuti kuchiritsa kwamakono kogwiritsira ntchito mwazi kunalibe kalero, kugwiritsiridwa ntchito kwamankhwala kwamwazi sikwamakono. Kwazaka zokwanira 2,000, mu Igupto ndi kwina kulikonse, “mwazi wamunthu unalingaliridwa kukhala mankhwala amphamvu a khate.” Sing’anga wina anavumbula mankhwala operekedwa kwa mwana wamwamuna wa Mfumu Esar-haddon pamene mtundu wa Asuri unali kutsogolera m’zopangapanga: “[Kalonga] akupeza bwino kwambiri; mbuyanga, mfumu, angakondwere. Kuyambira patsiku la 22 ndinampatsa (iye) mwazi kuti amwe, adzaumwa (uwo) kwa masiku 3. Kwamasiku ena 3 ndidzampatsa (iye mwazi) kaamba ka kugwiritsiridwa ntchito kwa mkati.” Esar-haddon anali kudyerana ndi Aisrayeli. Komabe, chifukwa chakuti Aisrayeli anali ndi Lamulo la Mulungu, iwo sakanamwa mwazi monga mankhwala.
Kodi mwazi ungwiritsiridwa ntchito monga mankhwala m’nthaŵi za Aroma? Wopenda zinyama Pliny (wokhala ndi moyo panthaŵi imodzimodziyo ndi atumwi) ndi sing’anga wa m’zaka za zana lachiŵiri Aretaeus akusimba kuti mwazi wa munthu unali mankhwala a khunyu. Pambuyo pake Tertullian analemba kuti: “Lingalirani awo amene ndi dyera la ludzu, pachiwonetsero m’bwalo la maseŵera, amatenga mwazi wongotuluka kumene wa apandu oipa . . . ndi kumka nawo kukachiritsira akhunyu awo.” Iye anawasiyanitsa ndi Akristu, amene “sakhaladi ndi mwazi wa zinyama pa zakudya [zawo] . . . Pamilandu ya Akristu inu mumawapatsa masoseji odzaza mwazi. Ndithudi, mukudziŵa, kuti puwo] ngosayenera kwa iwo.” Chotero, Akristu oyambilira ankalolera imfa koposa kudya mwazi.
“Mwazi mumpangidwe wake watsiku ndi tsiku sunasinthe . . . monga msanganizo m’mankhwala ndi matsenga,” likusimba motero bukhulo Flesh and Blood. “Mwachitsanzo, mu 1483, Louis XI wa Falansa anali kufa. ‘Tsiku lirilonse mkhalidwe wake unaipaipirabe, ndipo mankhwala sanampindulitse, ngakhale anali ndi mkhalidwe wachilendo; popeza kuti iye mwaphamphu anayembekezera kuchira ndi mwazi wamunthu umene anatenga kwa ana ena namwa.’”
Bwanji za kuthirira mwazi? Kuyeza kumeneku kunayambika pafupi ndi chiyambi cha zaka za zana la 16. Thomas Bartholin (1616-80), pulofesala wa kaumbidwe ka thupi pa Univesite ya Copenhagen, anatsutsa kuti: ‘Awo amene amadzetsa kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi wamunthu kuti ukhale mankhwala a mkati mwa thupi a nthenda akuwonekera kukhala akuugwiritsira ntchito molakwa ndi kuchimwa kwakukulu. Odya nyama ya anthu amatsutsidwa. Kodi nchifukwa ninji sitimanyansidwa ndi awo amene amaipitsa pammero pawo ndi mwazi wamunthu? Kofanana nako ndiko kulandiridwa kwa mwazi wachilendo wochokera pamtsempha wodulidwa, kaya mwa pakamwa kapena mwa zipangizo zothirira magazi. Oyambitsa kachitidwe kameneka amagwidwa ndi mantha ndi lamulo laumulungu, mwa limene kudyedwa kwa mwazi kukuletsedwa.’
Chifukwa cha chimenecho, anthu oganiza m’zaka mazana ambiri apitawo anazindikira kuti lamulo Labaibulo linagwira ntchito pakuloŵetsa kwa mwazi m’mitsempha monga momwe linagwirira ntchito pakuuloŵetsa mkamwa. Bartholin anamaliza kuti: “Mkhalidwe uliwonse wa kuloŵetsera [mwazi] umagwirizana ndi chifuno chimodzi cholingana, chakuti mwa mwazi umenewu thupi lodwala lidyetsedwe kapena kuchiritsidwa.”
Kupenda uku kungakuthandizeni kuzindikira kaimidwe kosasintha kachipembedzo kamene Mboni za Yehova zimatsatira. Izo zimaŵerengera kwambiri moyo, ndipo zimafunafuna chisamaliro cha mankhwala chawino. Koma izo nzotsimikiza kusaswa muyezo wa Mulungu, umene wakhala wosasinthika: Awo amene amalemekeza moyo monga mphatso yochokera kwa Mlengi samayesa kuchirikiza moyo mwa kudya mwazi.
Komabe, kwazaka zambiri mawu ambiri anenedwa kuti mwazi umapulumutsa moyo. Madokotala angasimbe zochitika m’zimene munthu wina anali ndi kutayika mwazi kwakukulu koma anathiriridwa mwazi ndiyeno anawongokera mwamsanga. Chotero mungadabwe kuti, ‘Kodi kumeneku nkwanzeru kapena kopanda nzeru motani mwamankhwala?’ Umboni wa zamankhwala umaperekedwa kuchirikizira kuchiritsa kwamwazi. Motero, ziri kwa inu kuti mupeze zenizeni kuti mupange chosankha chanzeru ponena za mwazi.
[Mawu a M’munsi]
a Paulo, pa Machitidwe 17:25, 28, New World Translation of the Holy Scriptures.
b Ziletso zofananazo zinalembedwa pambuyo pake m’Korani.
[Bokosi patsamba 4]
“Mwanjira imeneyi malamulo okhazikitsidwa m’mkhalidwe wachidule ndi wadongosolo [m’Machitidwe 15] akufotokozedwa kukhala ofunika, akumapereka umboni wamphamvu koposa wakuti m’maganizo mwa atumwi ameneŵa sanali makonzedwe akanthaŵi, kapena njira yakanthaŵi.”—Pulofesala Édouard Reuss, University of Strasbourg.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
Martin Luther anasonyeza matanthauzo a lamulo la atumwi: “Tsopano ngati tifuna kukhala ndi tchalitchi chimene chimagwirizana ndi upo umenewu, . . . tiyenera kuphunzitsa ndi kuumilira kuti kuyambira tsopano ndi kumkabe mtsogolo palibe kalonga, mbuye, mfulu, kapena mlimi amene ati adye atsekwe, kalulu, chinkhoma, kapena nyama yankhumba yophikidwa ndi mwazi . . . Ndipo mfulu ndi alimi ayenera kusala makamaka soseji yofiira ndi soseji ya mwazi.”
[Mawu a Chithunzi]
Woodcut by Lucas Cranach
[Bokosi patsamba 6]
“Mulungu ndi anthu amalingalira zinthu m’njira zosiyana kwambiri. Zimene zimawonekera kukhala zofunika m’maso mwathu kaŵirikaŵiri nzosanunkha kanthu m’kuyerekezera kwa nzeru yosatha; ndipo chimene chimawonekera kukhala chaching’ono kwa ife kwaŵirikaŵiri nchokhala ndi kufunika kwakukulu kwa Mulungu. Zinali choncho kuyambira pachiyambi.”—An Inquiry Into the Lawfulness of Eating Blood,” Alexander Pirie, 1787.
[Chithunzi patsamba 3]
Medicine and the Artist by Carl Zigrosser/Dover Publications
[Chithunzi patsamba 4]
Paupo wa mumbiri, bungwe lolamulira Lachikristu linatsimikizira kuti lamulo la Mulungu pamwazi nlomangabe
[Chithunzi patsamba 7]
Zirizonse zimene zingakhale zotulukapo, Akristu oyambilirawo anakana kuswa lamulo la Mulungu la mwazi
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzithunzi chojambulidwa ndi Gérôme, 1883, courtesy of Walters Art Gallery, Baltimore