Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
‘Sankhani moyo . . . [mwa] kumvera mawu [a Mulungu] . . . , pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.’—DEUTERONOMO 30:19, 20.
1. Kodi Akristu owona ngapadera motani m’kulemekeza kwawo moyo?
ANTHU ambiri amanena kuti amaulemekeza moyo, akumapereka lingaliro lawo pa chilango chaimfa, kuchotsa mimba, kapena kusaka nyama kukhala umboni wawo. Komabe, pali njira yapadera imene Akristu owona amalemekezera moyo. Salmo 36:9 limati: ‘Pakuti chitsime cha moyo chiri ndi inu [Mulungu].’ Popeza kuti moyo ndimphatso yochokera kwa Mulungu, Akristu amatenga lingaliro lake la mwazi wa moyo.
2, 3. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kumlingalira Mulungu ponena za mwazi? (Machitidwe 17:25, 28)
2 Moyo wathu umadalira pa mwazi, umene umapereka mpweya wotchedwa oxygen ku mbali zonse za thupi lathu, kuchotsa mpweya wotchedwa carbon dioxide, kulola matupi athu kulabadira masinthidwe a kutentha ndi kuzizira, ndi kutithandiza kulimbana ndi matenda. Uyo amene anatipatsa moyo wathu analinganizanso ndi kugaŵira madzi amthupi ochirikiza moyo otchedwa mwazi. Ichi chimasonyeza chikondwerero chake chopitirizabe chakusunga moyo wa anthu.—Genesis 45:5; Deuteronomo 28:66; 30:15, 16.
3 Ponse paŵiri Akristu ndi anthu mwachisawawa ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi mwazi ungapulumutse moyo wanga kokha mwa ntchito zake zachibadwa, kapena kodi mwazi ungapulumutse moyo mwa njira ina yofunika koposapo?’ Pamene kuli kwakuti anthu ambiri amazindikira kugwirizana kwa pakati pa moyo ndi ntchito zamasiku onse za mwazi, kwenikweni pali zambiri zoloŵetsedwamo. Miyezo yamakhalidwe ya Akristu, Asilamu, ndi Ayuda yonse imasumika pa Mpatsi wa Moyo yemwe analongosola malingaliro ake ponena za moyo ndi mwazi. Inde, Mlengi wathu ali nzambiri zonena pa mwazi.
Kaimidwe Kolimba ka Mulungu pa Mwazi
4. Kalekale m’mbiri ya anthu, kodi nchiyani chimene Mulungu ananena pa mwazi?
4 Mwazi umatchulidwa nthaŵi zoposa pa 400 m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Pakati pa kutchulidwa koyambirira pali lamulo la Yehova iri: “Chirichonse chokhala ndi moyo ndi kuyenda chidzakhala chakudya chanu. . . . Koma simuyenera kudya nyama yake yokhala ndi mwazi wake wa moyo.” Iye anawonjezera kuti: “Popeza kuti Ine ndidzafunsira mlandu wa mwazi wa moyo wanu.” (Genesis 9:3-5, New International Version) Yehova ananena zimenezo kwa Nowa, kholo la banja la anthu. Chotero, anthu onse anadziŵitsidwa kuti Mlengi amawona mwazi kukhala woimira moyo. Motero aliyense amene amati amamzindikira Mulungu monga Mpatsi wa Moyo ayenera kuzindikira kuti Iye akutenga kaimidwe kolimba ponena za kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi wa moyo.
5. Kodi nchifukwa chachikulu chiti chimene Aisrayeli sankadyera mwazi?
5 Mulungu anatchulanso mwazi popatsa Israyeli mpambo wa Chilamulo. Levitiko 17:10, 11, mogwirizana ndi matembenuzidwe Achiyuda a Tanakh, amati: “Ngati aliyense wa m’nyumba ya Israyeli kapena ya alendo okhala pakati pawo adya mwazi uliwonse, ndidzasonyeza mkwiyo wanga Ine motsutsana ndi munthu wodya mwaziyo, ndipo ndidzamdula pakati pa banja lake. Popeza kuti moyo wa nyama uli m’mwazi.” Lamulo limenelo lingakhale linali ndi mapindu athanzi, koma zambiri zinaloŵetsedwamo. Mwakuwona mwazi kukhala wapadera, Aisrayeli akasonyeza kudalira kwawo pa Mulungu kaamba ka moyo. (Deuteronomo 30:19, 20) Inde, chifukwa chachikulu chopeŵera kudya mwazi chinali, osati kuti ukakhala waupandu ku thanzi, koma kuti mwazi unali ndi tanthauzo lapadera kwa Mulungu.
6. Kodi tingakhalirenji otsimikiza kuti Yesu analemekeza kaimidwe ka Mulungu pa mwazi?
6 Kodi Chikristu chimaima pati ponena za kupulumutsa moyo wa anthu ndi mwazi? Yesu anadziŵa zimene Atate wake ananena ponena za kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi. Yesu ‘sanachita tchimo, ndipo m’kamwa mwake zichinapezedwa chinyengo.’ Izi zikutanthauza kuti iye anasunga Chilamulo mwangwiro, kuphatikizapo lamulo lonena za mwazi. (1 Petro 2:22) Chotero iye anakhazikitsira otsatira ake chitsanzo, kuphatikizapo chitsanzo chakulemekeza moyo ndi mwazi.
7, 8. Kodi ndimotani mmene kunakhalira kowonekera poyera kuti lamulo la Mulungu la mwazi limagwira ntchito kwa Akristu?
7 Mbiri imatiuza zimene zinachitika pambuyo pake pamene bungwe lolamulira Lachikristu linakhala upo ndi kupereka chigamulo chakuti kaya Akristu anayenera kusunga malamulo onse a Israyeli. Pansi pa chitsogozo chaumulungu, iwo anati Akristu sali ndi thayo lakusunga chilamulo cha Mose koma kuti “nkoyenera kupitirizabe kupeŵa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi mwazi ndi zinthu zopotoledwa [nyama zosakhetsedwa mwazi] ndi dama.” (Machitidwe 15:22-29, NW) Chotero iwo anachimveketsa bwino lomwe kuti kupeŵa mwazi ndimkhalidwe wofunika kwambiri mofanana ndi kupeŵa kupembedza mafano ndi chisembwere chowopsa.a
8 Akristu oyambirira anasunga chiletso chaumulungu chimenecho. Katswiri wa ku Briteni Joseph Benson anathirira ndemanga ponena za zimenezi kuti: “Chiletso cha kudya mwazi chimenechi, choperekedwa kwa Nowa ndi mbadwa zake zonse, ndi chobwezeredwa kwa Aisrayeli . . . sichinafafanizidwepo konse, koma, mosiyana, chatsimikiziridwa pansi pa Chipangano Chatsopano, Machitidwe xv.; ndipo motero chinakhalitsidwa thayo lopitirizabe.” Komabe, kodi zimene Baibulo limanena pa mwazi zimachotsapo kuugwiritsira ntchito m’zamankhwala kwamakono, monga ngati kuthiridwa mwazi, kumene mwachiwonekere kunalibeko m’tsiku la Nowa kapena m’nthaŵi ya atumwi?
Mwazi m’Mankhwala Kapena Monga Mankhwala
9. Kodi ndimotani mmene mwazi unagwiritsiridwa ntchito monga mankhwala m’nthaŵi zakale, mosiyana ndi kaimidwe Kachikristu kotani?
9 Kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi monga mankhwala sikwamakono konse. Bukhu lakuti Flesh and Blood, lolembedwa ndi Reay Tannahill, limanena kuti kwa zaka pafupifupi 2,000, mu Igupto ndi kwina kulikonse, “mwazi unalingaliridwa kukhala mankhwala amphamvu koposa a khate.” Aroma anakhulupirira kuti khunyu inakhoza kuchiritsidwa mwakumwa mwazi wa anthu. Tertullian analemba ponena za kugwiritsiridwa ntchito kwa mwazi monga “mankhwala” kumeneku kuti: “Talingalirani awo amene pokhala ndi ludzu laumbombo, pachisonyezero cha m’bwalo lazirombo, amatenga mwazi wauŵisi wa apandu . . . kukachiritsira akhunyu awo.” Ichi chinali chosiyana kotheratu ndi zimene Akristu ankachita: “Sitimakhala ngakhale ndi mwazi wanyama pa chakudya chathu . . . Pa ziyeso za Akristu muwapatsa masoseji odzala ndi mwazi. Ndithudi, ndinu okhutiritsidwa kuti [iko] ndikuswa lamulo kwa iwo.” Lingalirani tanthauzo lake: Mmalo mwakudya mwazi, umene umaimira moyo, Akristu oyambirira anali ofunitsitsa kuika moyo wawo pachiswe.—Yerekezerani ndi 2 Samueli 23:15-17.
10, 11. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti muyezo wa Mulungu wa mwazi umaletsa kulandira kuthiridwa mwazi?
10 Ndithudi, kalelo mwazi sunathiridwe m’thupi, popeza kuti kuchiritsa koyesa kwa kuthiridwa mwazi kunangoyamba pafupi ndi zaka za zana la 16. Komabe, m’zaka za zana la 17, profesa wa ziŵalo za thupi wa pa Yunivesiti ya Copenhagen anatsutsa kuti: ‘Anthu amene amadziloŵetsa m’kugwiritsira ntchito mwazi wa anthu kaamba ka kuchiritsa matenda a m’thupi amaoneka kukhala akuugwiritsira ntchito mwazi molakwa ndi kuchita tchimo lowopsa. Anthu odya nyama ya anthu anzawo ngosaloledwa. Kodi nchifukwa ninji sitimanyansidwa ndi anthu amene amaipitsa m’mero wawo ndi mwazi wa anthu? Chofanana ndicho kulandira mwazi wa munthu wina wotulukira pa mtsempha wobooledwa, kaya kupyolera m’kamwa kapena zipangizo zothirira mwazi. Amene anayambitsa kachitidwe kameneka akuchita mantha ndi lamulo laumulungu.’
11 Inde, ngakhale m’zaka mazana akale, anthu anawona kuti lamulo la Mulungu linaletsa kudya mwazi ponse paŵiri kupyolera m’mitsempha ndi kupyolera mkamwa. Kuzindikira zimenezi kungathandize anthu lerolino kumvetsetsa kaimidwe kamene Mboni za Yehova zakatenga, kamene kamagwirizana ndi kaimidwe ka Mulungu. Pamene kuli kwakuti amawona moyo kukhala wa mtengo wapatali ndi kuyamikira chisamaliro cha zamankhwala, Akristu owona amalemekeza moyo monga mphatso yochokera kwa Mlengi, chotero samayesa kuchirikiza moyo wawo mwakudya mwazi.—1 Samueli 25:29.
Kodi Ndiwo Mankhwala Opulumutsa Moyo?
12. Kodi nchiyani chimene anthu anzeru adzalingalira ponena za kuthiridwa mwazi?
12 Kwa zaka zambiri akatswiri anena kuti mwazi umapulumutsa miyoyo. Adokotala angasimbe kuti winawake yemwe anataya mwazi mowopsa anathiridwa mwazi ndipo anakhala bwino. Chotero anthu angazizwe kuti, ‘Kodi kaimidwe Kachikristu nkanzeru motani kapena nkopusa motani ponena za mankhwala?’ Asanalingalire machiritsidwe a zamankhwala owopsa aliwonse, munthu wolingalira adzapenda ponse paŵiri mapindu othekera ndi maupandu othekera. Bwanji ponena za kuthiridwa mwazi? Chenicheni nchakuti kuthiridwa mwazi nkodzaza ndi maupandu ambiri. Iko kungakhaledi kwakupha.
13, 14. (a) Kodi ndinjira zina ziti zimene zatsimikizira kuti kuthiridwa mwazi nkwaupandu? (b) Kodi ndimotani mmene chokumana nacho cha papa chinasonyezera maupandu a mwazi ku thanzi?
13 Posachedwapa, adokotala L. T. Goodnough ndi J. M. Shuck ananena kuti: “Anthu a ntchito zamankhwala akhala odziŵa kwa nthaŵi yaitali kuti pamene kuli kwakuti mwazi wosungidwa ngotetezereka monga momwe timadziŵira kuusunga, kuthiridwa mwazi nthaŵi zonse kwakhala ndi upandu. Vuto lobwerezabwereza la kuthiridwa mwazi lapitirizabe kukhala matenda a kutupa kwa chiŵindi otchedwa non-A, non-B hepatitis (NANBH); mavuto ena othekera amaphatikizapo matenda a kutupa kwa chiŵindi otchedwa hepatitis B, alloimmunization, ziyambukiro za kuthiridwa mwazi, kutsenderezeka kwa dongosolo lathupi lochinjiriza matenda, ndi kuchulukitsitsa kwa nsanganizo ya iron.” Kuyerekezera ‘mosamalitsa’ umodzi wokha wa maupandu owopsa ameneŵa, lipotilo linawonjezera kuti: “Kukuyembekezeredwa kuti pafupifupi anthu 40,000 [mu United States mokha] adzakhala ndi NANBH chaka chirichonse ndikuti ofika ku 10% a ameneŵa adzakhala ndi cirrhosis ndi/kapena hepatoma [kansa ya chiŵindi].”—The American Journal of Surgery, June 1990.
14 Pamene upandu wakutenga matenda ku mwazi wothiridwa wadziŵika mofala, anthu akupendanso lingaliro lawo la kuthiridwa mwazi. Mwachitsanzo, pamene papa anawomberedwa mfuti mu 1981, anakathandizidwa ku chipatala ndi kutulutsidwa. Pambuyo pake anafunikira kubwererakonso kwa miyezi iŵiri, ndipo mkhalidwe wake unawoneka kukhala wowopsa kwakuti anawoneka monga woyenera kuleka ntchito yake. Chifukwa ninji? Iye anatenga nthenda yoyambukira ziŵalo zonse yotchedwa cytomegalovirus ku mwazi umene anapatsidwa. Anthu ena angazizwe kuti, ‘Ngati mwazi wopatsidwa kwa papa ngwopanda chisungiko, bwanji ponena za mwazi wothiridwa kwa anthu wambafe?’
15, 16. Kodi nchifukwa ninji kuthiridwa mwazi nkopanda chisungiko ngakhale kuti mwaziwo wapimidwa kuwonamo matenda?
15 ‘Koma kodi sangakhoze kupima mwazi kuwonamo matenda?’ wina angafunse motero. Eya, talingalirani monga chitsanzo kupimidwa kwa mwazi kuti apeze matenda a kutupa kwa chiŵindi otchedwa hepatitis B. Patient Care (February 28, 1990) inanena kuti: “Nthenda yakutupa chiŵindi kwa pambuyo pakuthiridwa mwazi inacheperapo pamene mwazi unapimidwa kuwona [matendawo], koma 5-10% ya matenda akutupa chiŵindi kwa pambuyo pa kuthiridwa mwazi amachititsidwabe ndi hepatitis B.”
16 Kulephera kwa kuyesa koteroko kumawonekanso ndi upandu wina woyambukira kupyolera m’mwazi—AIDS. Mliri wa AIDS, wagalamutsa anthu mwamphamvu ku upandu wa mwazi wokhala ndi matenda. Mosakaikira, tsopano pali zoyesera zopimira mwazi kuwona zizindikiro za kachirombo kopereka nthendayi. Komabe, mwazi sumapimidwa m’malo onse, ndipo zikuwoneka kuti anthu akhoza kunyamula kachirombo ka AIDS m’mwazi wawo kwa zaka zambiri popanda kupezedwa ndi njira zoyesera zatsopano. Chotero odwala akhoza kutenga AIDS—ndipo atenga AIDS—ku mwazi umene unapimidwa ndi kupezedwa kukhala wabwino!
17. Kodi ndimotani mmene kuthiridwa mwazi kungachitire chivulazo chimene sichingawoneke mwamsanga?
17 Adokotala Goodnough ndi Shuck anatchulanso “kutsenderezeka kwa dongosolo lathupi lochinjiriza matenda.” Inde, maumboni akuchuluka kuti ngakhale mwazi woyenderana bwino ungawononge dongosolo la thupi lochinjiriza matenda la wodwala, kuchititsa kansa ndi imfa. Chotero, kupenda kwa ku Canada kwa “odwala okhala ndi kansa ya m’mutu ndi m’khosi kunasonyeza kuti amene anathiridwa mwazi mkati mwa kuchotsedwa chotupa anakhala ndi kuchepekera kwa dongosolo la thupi lochinjiriza matenda pambuyo pake.” (The Medical Post, July 10, 1990) Adokotala pa Yunivesiti ya Southern California anapereka lipoti lakuti: “Kubukabukanso kwa makansa onse a pa m’mero kunali 14% kwa amene sanalandire mwazi ndipo 65% kwa amene anatero. Ponena za kansa ya m’kamwa, pakhosi, ndi m’mphuno kapena m’njira yam’mphuno, kubukabukanso kunali 31% popanda kuthiridwa mwazi ndipo 71% kwa kuthiridwa mwazi.” (Annals of Otology, Rhinology & Laryngology, March 1989) Dongosolo lathupi lochinjiriza matenda lotsenderezedwa likuwoneka kukhala likusonyezanso chenicheni chakuti amene amapatsidwa mwazi mkati mwa kutumbulidwa amayambukiridwa ndi matenda mosavuta.—Onani bokosi, tsamba 10.
Kodi Ziripo Njira Zina Mmalo Mwa Mwazi?
18. (a) Kodi maupandu okhala m’kuthiridwa mwazi apangitsa asing’anga a m’chipatala kutembenukira ku chiyani? (b) Kodi ndichidziŵitso chotani cha njira zina m’malo mwa kuthiridwa mwazi chimene mungakambitsirane ndi sing’anga wanu wa m’chipatala?
18 Ena angalingalire kuti, ‘Kuthiridwa mwazi nkwangozi, koma kodi pali njira zina zirizonse?’ Mosakaikira timafuna chisamaliro cha zamankhwala chothandiza ndi chamtengo wapatali, chotero kodi ziripo njira zoyenerera ndi zothandiza zochiritsira matenda aakulu popanda kugwiritsira ntchito mwazi? Mokondweretsa, inde ziripodi. Magazini otchedwa The New England Journal of Medicine (June 7, 1990) anapereka lipoti iri: “Popeza kuti asing’anga mowonjezerekawonjezereka akudziŵa maupandu a [AIDS], ndi matenda ena oyambukira mwakuthiridwa mwazi, akulingaliranso maupandu ndi mapindu a kuthiridwa mwazi ndipo akutembenukira ku njira zina, kuphatikizapo zija zopeŵeratu kuthira mwazi.”b
19. Kodi nchifukwa ninji mungakhale achidaliro kuti mukhoza kukana mwazi komabe nkuchiritsidwa ndi mankhwala mwachipambano?
19 Kwanthaŵi yaitali Mboni za Yehova zakhala zikukana kuthiridwa mwazi, osati kwenikweni chifukwa cha maupandu a thanzi, koma chifukwa cha kumvera lamulo la Mulungu la mwazi. (Machitidwe 15:28, 29) Komabe, adokotala aluso atha kusamalira mwachipambano Mboni zodwala popanda kugwiritsira ntchito mwazi, ndi maupandu ake otulukapo. Monga chimodzi chokha cha zitsanzo zambiri zosimbidwa m’mabuku onena za mankhwala, Archives of Surgery (November 1990) inafotokoza kusintha mtima kochitidwa kwa Mboni zodwala zimene chikumbumtima chawo chinalola kachitidwe koteroko popanda kuikidwa mwazi. Lipotilo linati: “Kwazaka zoposa 25 zakuchita kutumbula kwa mtima pa Mboni za Yehova kwatulukira m’kusintha mtima kwachipambano popanda kugwiritsira ntchito nsanganizo za m’mwazi . . . Palibe imfa zinachitika pamene wodwala akali m’chipatala asanatumbulidwe kapena pambuyo pake, ndipo kupenda kotsatirapo mwamsanga kwasonyeza kuti sikwenikweni kuti matupi a odwala ameneŵa amakana ziŵalo zachilendo zoikidwa mwa iwo.”
Mwazi Wamtengo Wapatali Koposa
20, 21. Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala ochenjera kuti asakhale ndi maganizo akuti “Mwazi ndiwo mankhwala oipa”?
20 Komabe, pali funso lopenda moyo limene aliyense wa ife afunikira kudzifunsa. ‘Ngati ndasankha kusalandira kuthiridwa mwazi, nchifukwa ninji? Kunena mowona mtima, kodi chifukwa changa choyambirira, chachikulu nchotani?’
21 Tatchula kale kuti pali njira zina zothandiza m’malo mwa mwazi zimene sizimaika munthu pa ngozi zambiri zogwirizanitsidwa ndi kuthiridwa mwazi. Ngozi zonga ngati kutupa chiŵindi kapena AIDS zasonkhezeradi ambiri kukana mwazi pazifukwa zosakhala zachipembedzo. Ena amalankhula motsutsa zimenezi mwamphamvu, monga ngati kuti anali kuguba pansi pa mbendera yomati, “Mwazi Ndiwo Mankhwala Oipa.” Nkotheka kuti Mkristu angakokedwere m’kuguba kwa kutsutsa koteroko. Koma iko ndiko kuguba panjira yogoma. Kodi ziri choncho motani?
22. Kodi ndilingaliro lenileni lotani la moyo ndi imfa limene tiyenera kukhala nalo? (Mlaliki 7:2)
22 Akristu owona amazindikira kuti ngakhale ndi chisamaliro chamankhwala m’zipatala zabwino koposa, panthaŵi ina yake anthu amafa. Ndi kuthiridwa mwazi kapena popanda kuthiridwa mwazi, anthu amafabe. Kunena motero sikukhala oitana tsoka. Kuli kuyang’anizana ndi zenizeni. Imfa ndichenicheni cha moyo lerolino. Anthu amene amanyalanyaza lamulo la Mulungu la mwazi kaŵirikaŵiri amakumana ndi chivulazo chamwamsanga kapena chochedwetsedwa cha mwazi. Ena amafa ngakhale ndi mwazi wothiridwa. Chikhalirechobe, monga momwe tonsefe tiyenera kudziŵira, awo amene amachira pambuyo pothiridwa mwazi samapezabe moyo wosatha, motero mwazi sunatsimikizire kukhala wopulumutsa miyoyo yawo kwanthaŵi yonse. Kumbali ina, anthu ambiri amene amakana mwazi, pazifukwa zachipembedzo ndi/kapena zifukwa zamankhwala, koma namalola njira zina zochiritsira m’malo mwa mwazi amachira bwino lomwe. Iwo motero angatalikitse moyo wawo kwa zaka zambiri—koma osati kosatha.
23. Kodi ndimotani mmene malamulo a Mulungu pa mwazi amasonyezera kuti ndife ochimwa ndi ofunikira dipo?
23 Chenicheni chakuti anthu onse okhala ndi moyo lerolino ali opanda ungwiro ndikuti m’kupita kwanthaŵi amafa chimatitsogolera ku mfundo yaikulu ya chimene Baibulo limanena pa mwazi. Mulungu anauza anthu onse kusadya mwazi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti umaimira moyo. (Genesis 9:3-6) Mu mpambo Wachilamulo, iye anaika malamulo onena za mfundo yakuti anthu onse ngochimwa. Mulungu anauza Aisrayeli kuti mwakupereka nsembe za nyama, iwo akasonyeza kuti machimo awo anafunikira kukwiriridwa. (Levitiko 4:4-7, 13-18, 22-30) Ngakhale kuti ichi sichimene akuchifuna kwa ife lerolino, icho chiri ndi tanthauzo tsopano. Mulungu anafuna kupereka nsembe imene ikakwirira kotheratu machimo a okhulupirira onse—dipo. (Mateyu 20:28) Ichi ndicho chifukwa chake tifunikira kukhala ndi lingaliro la Mulungu la mwazi.
24. (a) Kodi nchifukwa ninji kukakhala kulakwa kutenga maupandu a thanzi kukhala mfundo yaikulu ponena za mwazi? (b) Kodi nchiyani kwenikweni chimene chiyenera kukhala chifukwa chachikulu cha lingaliro lathu pa kugwiritsira ntchito mwazi?
24 Kukakhala kulakwa kusumika maganizo kwakukulu pa maupandu a thanzi a mwazi, popeza kuti sindicho chinali chifukwa cha Mulungu. Aisrayeli angakhale anapeza mapindu a thanzi mwakusadya mwazi, monga momwe angakhale anapindulira mwakusadya nyama ya nkhumba kapena nyama zimene zimadya zonyansa. (Deuteronomo 12:15, 16; 14:7, 8, 11, 12) Komabe, kumbukirani kuti, pamene Mulungu anapatsa Nowa chiyeneretso chakudya nyama, iye sanaletse kudya mnofu wa nyamazo. Koma anapereka lamulo lakuti anthu sayenera kudya mwazi. Mulungu sanasumike maganizo kwakukulukulu pa maupandu a thanzi othekera. Imeneyo sindiyo inali mfundo yaikulu ya lamulo lake la mwazi. Olambira ake anayenera kukana kugwiritsira ntchito mwazi kuti achirikize moyo wawo, osati kwakukulukulu chifukwa chakuti kuteroko kunali kwaupandu ku thanzi, koma chifukwa chakuti kunali kupanda chiyero. Iwo anakana mwazi, sichifukwa chakuti unali woipitsidwa, koma chifukwa chakuti unali wamtengo wapatali. Iwo akapeza chikhululukiro kokha mwa mwazi woperekedwa nsembe.
25. Kodi ndimotani mmene mwazi ungapulumutsire moyo kosatha?
25 Zirinso chimodzimodzi kwa ife. Pa Aefeso 1:7, mtumwi Paulo analongosola kuti: ‘Tiri ndi mawomboledwe mwa mwazi [wa Kristu], chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.’ Ngati Mulungu amakhululukira machimo a munthu ndi kuwona munthuyo kukhala wolungama, munthuyo amakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Chotero dipo la mwazi wa Yesu likhoza kupulumutsa moyo—kwanthaŵi yonse, kwenikweni, kwamuyaya.
[Mawu a M’munsi]
a Lamulo linamaliza motere: “Ngati musunga zinthu zimenezi mosamalitsa, mudzalemerera. Thanzi labwino kwa inu!” (Machitidwe 15:29, NW) Ndemanga yakuti “Thanzi labwino kwa inu” silinali lonjezo lakuti, ‘Ngati mupeŵa mwazi kapena dama, mudzakhala ndi thanzi labwinopo.’ Iyo inali chabe ndemanga yomalizira kalata, monga ngati, ‘Tsalani bwino.’
b Njira zina zothandiza m’malo mwa kuthiridwa mwazi zafotokozedwa m’brosha yakuti How Can Blood Save Your Life?, yofalitsidwa mu 1990 ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova zimakanira kuthiridwa mwazi nchotani?
◻ Kodi ndiumboni wotani umene umatsimikizira kuti lingaliro la Baibulo la mwazi siliri lopanda nzeru ponena za mankhwala?
◻ Kodi dipo limagwirizanitsidwa motani ndi lamulo la Baibulo la mwazi?
◻ Kodi ndinjira yokha yotani imene mwazi ungapulumutsire miyoyo kwanthaŵi yonse?
[Bokosi patsamba 10]
KUTHIRIDWA MWAZI NDI KUYAMBUKIRIDWA NDI MATENDA
Pambuyo pakukambitsirana kwakukulu kwakuti kaya kuthiridwa mwazi kungapangitse thupi la wodwala kuyambukiridwa ndi matenda mosavuta, Dr. Neil Blumberg anagamula kuti: “Mwa kupenda 12 kwa zamankhwala [pa nkhaniyo], 10 kunapeza kuti kuthira mwazi kunali kwenikweni ndipo mwapadera kogwirizanitsidwa ndi kuwonjezereka kwa upandu wakuyambukiridwa ndi kachirombo ka bacteria . . . Kuwonjezerapo, kuthiridwa mwazi kwakale kungachititse kutumbula kukhala ndi chiyambukiro pa mphamvu ya wodwala yoletsa kuyambukiridwa ngati ziyambukiro za dongosolo la thupi lochinjiriza matenda zakhala kwa nthaŵi yaitali yomwe yasonyezedwa ndi kupenda kwina . . . Ngati mapendedwe ameneŵa angafutukulidwe ndi kutsimikiziridwa, kukuwoneka kuti ziyambukiro zoipitsitsa zamatenda zapambuyo pa kutumbulidwa zingakhale vuto limodzi lofala logwirizanitsidwa ndi kuthiridwa mwazi wa munthu wina.”—Transfusion Medicine Reviews, October 1990.
[Chithunzi patsamba 8]
Maselo ofiira a mwazi okulitsidwa. “‘Microliter’ iriyonse ya mwazi imakhala ndi maselo ofiira a mwazi ochokera pa 4 miliyoni kufika ku 6 miliyoni.”—“The World Book Encyclopedia”
[Mawu a Chithunzi]
Kunkel-CNRI/PHOTOTAKE NYC