Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?
Sungani chidziŵitso chimenechi kumene mukhoza kuchipeza msanga pamene chifunika
1 Palibe aliyense amene amaganiza kwambiri kuti angakhale m’chipatala lero kapena maŵa. Chikhalirechobe, ‘nthaŵi ndi zochitika zosayembekezereka zimatigwera tonsefe.’ (Mlal. 9:11, NW) Ngakhale ngati simungakonde kulandira chisamaliro cha mankhwala kuchipatala kaamba ka thanzi lanu, kodi mungadzitetezere bwanji pa kuthiridwa mwazi kumene simufuna ngati mungakomoke pangozi ndi kutengeredwa kuchipatala mwamsanga? Inde, ngozi kapena kukula kwa mwadzidzidzi kwa matenda kungakuchititseni kuyang’anizana mosayembekezera ndi chiyeso cha chikhulupiriro chanu.
2 Ngati mwapezeka m’chipatala pachifukwa chilichonse, kodi mudzachitanji kuti musunge umphumphu ngati munthu wina kumeneko akuuzani kuti mudzafa ngati simuthiridwa mwazi? Kodi mudzavomereza mofulumira kuti zonenazo zikusonyezadi mmene matenda anu akulira? Kodi ndinu wotsimikiziradi kuti simufuna mwazi? Kodi muli wokonzekera kuyang’anizana ndi chiyeso chimenechi cha chikhulupiriro chanu ndi ‘kusala mwazi’?—Mac. 15:28, 29.
3 Kukana mwachipambano kuthiridwa mwazi kosafunika ndi koipitsa mwauzimu kumasonkhezeredwa ndi chitsimikizo cholimba. Chitsimikizo chotero chiyenera kuzikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha zimene Baibulo limanena pa mwazi. Apo phuluzi, mungathe, chifukwa cha kutekeseka maganizo, kuwopsezedwa mosavuta ndi munthu amene akunena kuti akudziŵa zambiri ponena za vutolo kuposa inu. Kodi mudzasokeretsedwa ndi kuyamba kuganiza kuti mwina madokotala akudziŵa zambiri ponena za mwazi kuposa Mulungu? Ndithudi, m’mikhalidwe imeneyi mudzafunikira ‘kulimbika’ pakuchita “zoyenera” pamaso pa Yehova, mosasamala kanthu za zimene anthu wamba anganene. (Deut. 12:23-25) Koma kodi mufunikira kuyang’anizana ndi chiyeso chimenechi muli nokhanokha?—Mlal. 4:9-12.
DIPATIMENTI YOPEREKA CHIDZIŴITSO CHA ZACHIPATALA NDI MAKOMITI OLANKHULANA NDI CHIPATALA
4 Kuti ithandize awo amene afunikira thandizo pamene ayang’anizana ndi vuto la kuthiridwa mwazi, Sosaite yakhazikitsa Ofesi ya Chidziŵitso cha Zachipatala kubeteli. Yakhazikitsanso Makomiti Olankhulana ndi Chipatala 100 m’mizinda yaikulu ya United States. Makomiti ameneŵa ali opangidwa ndi akulu oposa 600 amene anaphunzitsidwa bwino za ntchito imeneyi.
5 Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala ikhoza kufufuza m’magazini a zamankhwala oposa 3,600 padziko lonse kuti ipeze chidziŵitso chonena za kukhalapo ndi kugwira ntchito kwa maopaleshoni ndi chisamaliro chopanda mwazi. Ndiyeno imapereka chidziŵitso chatsopanocho m’zamankhwala ku Makomiti Olankhulana ndi Chipatala, zipatala, ndi kwa madokotala ena. (Nthaŵi zina Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala yatumiza nkhani zamankhwala zosonyeza zimene zingachitidwe popanda mwazi ndi kuthetsa mwachipambano nkhondo yochitika kuchipatala.) Imadziŵitsa makomiti za zigamulo zabwino za makhoti zimene zidzathandiza oweruza kupenda milandu yathu ndi chidziŵitso chowonjezereka. Imasunganso zolembedwa za madokotala ogwirizanika oposa 40,000 kotero kuti makomiti azikhala ndi mafaelo achidziŵitso chatsopano ogwiritsira ntchito pamene mavuto a kuthiridwa mwazi abuka.
6 Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala imayang’aniranso maphunziro ndi ntchito za Makomiti Olankhulana ndi Chipatala. M’mizinda mmene ali, Makomiti Olankhulana ndi Chipatala nthaŵi zonse amapereka malipoti opatsa chidziŵitso kwa ogwira ntchito m’zipatala kuti alimbitse maunansi awo ndi iwo. Ndiponso amafunsa antchito ameneŵa kuti adziŵe ngati kungapezeke madokotala ena owonjezereka alionse amene angatisamalire popanda kugwiritsira ntchito mwazi. Abale ameneŵa ali okonzekera kukuthandizani, koma pali masitepe ofunika oyenera kutengedwa pasadakhale amene muyenera kutsatira kuti muyale maziko akuti iwo achite zimenezo bwino lomwe.
MASITEPE OFUNIKA OYENERA KUTENGEDWA PASADAKHALE—KODI MWAWATSATIRA KALE?
7 Choyamba, tsimikizirani kuti onse m’banja ali ndi khadi lawo la medical directive lodzazidwa mokwanira—lokhala ndi deti, siginecha, ndi mboni. Makadi opanda deti ndi/kapena mboni a abale ena amene anapita kuchipatala anakayikiridwa. Ndipo kodi ana athu onse osabatizidwa ali ndi ma identity card awo odzazidwa? Ngati alibe, kodi ogwira ntchito m’chipatala angadziŵe motani kaimidwe kanu ponena za mwazi ndi amene ayenera kuitanidwa litabuka vuto lamwadzidzidzi lokhudza mwana wanu?
8 Pamenepo tsimikizirani kuti onse ali ndi makadi ameneŵa NTHAŴI ZONSE. Onani ngati ana anu ali nawo asanapite kusukulu tsiku lililonse, inde, ngakhale asanapite kukaseŵera kapena kumalo osangulukira. Tonsefe tiyenera kutsimikizira kuti tili ndi makadi ameneŵa kuntchito, pamene tili patchuthi, kapena pamsonkhano Wachikristu. Musakhale mulibe iwo!
9 Talingalirani zimene zingachitike kwa inu ngati mungafike m’chipinda cha za mwadzidzidzi m’chipatala muli mumkhalidwe wowopsa, mwakomoka ndipo/kapena simutha kulankhula. Ngati mulibe khadilo, ndipo wachibale kapena mkulu sanafikebe kuchipatala kudzakulankhulirani, ndipo kupezeka kuti ‘mufunikira mwazi,’ inu mosakayikira mudzathiridwa mwazi. Mwatsoka, zimenezi zachitika kwa ena. Koma pamene tili ndi khadilo, limatilankhulira, likumasonyeza chosankha chathu.
10 Nchifukwa chake medical document ili yabwino kuposa khoza kapena unyolo wa m’khosi wofotokoza za mankhwala. Ziŵirizi sizimafotokoza zifukwa zathu zozikidwa m’Baibulo za kaimidwe kathu ndipo zilibe masiginecha okhalira umboni zonenedwazo. Chigamulo cha khoti la ku Canada chinati ponena za khadi la mlongo wina: “[Wodwalayu] wasankha mwanjira yokha yothekera kudziŵitsa madokotala ndi opereka chisamaliro cha mankhwala ena, kuti ngati angakomoke kapena mwanjira ina kulephera kulongosola zofuna zake, safuna kuthiridwa mwazi.” Chotero musakhale mulibe ilo!
11 Popeza kuti medical directive yathu yakonzedwa makamaka kaamba ka mikhalidwe yamwadzidzidzi, ndiye kuti ponena za opaleshoni yochita kukonzekera kudzakhala kwanzeru kuti mulembe malangizo anuanu pasadakhale, okhala ndi zochuluka (ozikidwa pa medical directive yathu) kotero kuti mungaphatikizepo malongosoledwe ena, onga mtundu wa opaleshoni ndi maina a madokotala ndi chipatala. Nkoyenera kwa inu kuchita zimenezi ndipo motero mukumadziŵikitsa chisamaliro chimene mukufuna. Ngakhale kuti inu ndi dokotala simungayembekezere mavuto aakulu, fotokozani kuti malangizo ameneŵa ayenera kutsatiridwa patachitika zilizonse zosayembekezereka.—Miy. 22:3.
12 Sitepe lotsatira lofunika ndilo kulankhula ndi madokotala oyenerera amene mudzafunikira kuonana nawo kaya kaamba ka chisamaliro wamba kapena cha mwadzidzidzi. Kodi ndani makamaka amene muyenera kulankhula naye?
LANKHULANI NDI MADOKOTALA
13 GULU LA MADOKOTALA: Iyi ndi nthaŵi imene sipafunikira kuwopa munthu. (Miy. 29:25) Ngati muli wosatsimikizira, wina angaganize kuti muli wosaona mtima. Pamene opaleshoni ikufunikira, yochita kukonzekera kapena yamwadzidzidzi, inu kapena wachibale wapafupi ayenera kufunsa mafunso olunjika molimba mtima kwa mkulu wa gulu la madokotala ochita opaleshoni. Limodzi la mafunso ofunika nlakuti, Kodi gululo lidzalemekeza zofuna za wodwalayo ndi kumchiritsa popanda mwazi m’mikhalidwe iliyonse? Popanda chitsimikizo chimenechi simudzakhala wotetezereka kwenikweni.
14 Fotokozani momvekera bwino ndi kulimba mtima kwaulemu zofuna zanu. Mveketsani bwino lomwe kuti mukufuna kuti chisamaliro cha mankhwala chiperekedwe pa vuto lanu mwa njira ina popanda mwazi. Modekha ndi mwachidaliro kambitsiranani ponse paŵiri za advance medical directive yanu ndi fomu yochotsera mlandu ya chipatala. Ngati dokotala wochita opaleshoni safuna kuchita zimene mukufuna, mudzawombola nthaŵi ngati mungapemphe woyang’anira chipatala kukupezerani dokotala wina. Imeneyo ndi ntchito yake.
15 DOKOTALA WOCHITITSA DZANZI: Pa madokotala onse amene mufunikira kulankhula nawo musanapite ku opaleshoni, MUSALEPHERE KULANKHULA NDI DOKOTALA AMENEYU. Pokhala ndi thayo la kukusungani muli wamoyo pamene dokotala akuchita opaleshoni, dokotala wochititsa dzanzi ndiye amene amapanga zosankha pa nkhani zonga za kugwiritsira ntchito mwazi. Chotero simumakhala wotetezereka kwenikweni mwa kungolankhula ndi dokotala wa opaleshoni. Chifukwa chake, muyenera kulankhula ndi dokotala wochititsa dzanzi ndi kumkhutiritsa ponena za kaimidwe kanu, pofuna kudziŵa ngati kadzalemekezedwa kapena ayi.—Yerekezerani ndi Luka 18:3-5.
16 Kukuoneka ngati kuti, nthaŵi zambiri zimene zimachitika nzakuti, dokotala wochititsa dzanzi amachezera wodwala kwanthaŵi yaifupi mochedwerapo usiku isanayambe opaleshoni—mochedwa kwambiri ngati akutsutsa kaimidwe kanu ponena za mwazi. Umirirani kuti dokotala wochita opaleshoni asankhiretu dokotala wochititsa dzanzi wogwirizanika amene mungalankhule naye opaleshoni yochita kukonzekera ikali patali. Pamenepo padzakhala nthaŵi ya kufuna wina ngati woyambayo sakufuna kutsatira zofuna zanu. Musalole aliyense kukukakamizani kusagwiritsira ntchito kuyenera kumeneku kuti mukhutiritsidwe ndi dokotala wochititsa dzanzi pa opaleshoni yanu.
17 Kwa onsewa, muyenera kumveketsa bwino lomwe kaimidwe kanu kosasintha: MWAZI AYI. Pemphani kuti chisamaliro cha mankhwala chiperekedwe kwa inu mwa njira ina popanda mwazi. Tchulani njira zina zilizonse zodziŵika zimene zingagwiritsidwe ntchito pa inu mmalo mwa mwazi. Ngati gulu la madokotala liganiza kuti zimenezo zili zosathandiza kwa inu, apempheni kufufuza njira zina zothekera m’mabuku a zamankhwala. Auzeni kuti mungawapezere chidziŵitso china ngati angafune mwa kupempha akulu akwanu kukaonana ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala yapafupi.
KUGWIRITSIRA NTCHITO ZOYENERA ZANU
18 Pendani mosamalitsa fomu yochotsera mlandu ndi fomu ya kuvomereza kwanu imene chipatala chikupemphani kusaina poloŵamo. Nthaŵi zina pambuyo ponena kuti iwo adzalemekeza zofuna zanu, ndime yotsatira imanena kuti wosainayo wavomereza kuti achipatala angagwiritsire ntchito chisamaliro “chopulumutsa moyo” atakumana ndi mavuto. Zimenezo zingaphatikizepo mwazi. Muli ndi kuyenera kwa kusintha mawu alionse otero kuti muchotsepo mwazi kapena kuwafafaniza onse. Manesi angayese kukuuzani kuti simuyenera kuchita zimenezo, koma mungatero! Fotokozani kuti fomu imeneyo ili pangano lanu ndi iwo ndi kuti simungasaine pangano limene simukuvomereza. Ngati aliyense ayesa kukukakamizani kusaina mosemphana ndi chifuno chanu, pemphani kulankhula ndi woyang’anira ndi/kapena woimira odwala wa chipatala chimenecho.
19 Kodi mungachite zimenezo? Inde, mungatero. Chotero dziŵani zoyenera zanu monga wodwala. Zoyenera zaumunthu zimenezi sizimasiyidwa pakhomo pamene muloŵa m’chipatala. Simufunikira kuzitaya kuti musamaliridwe. Musalole aliyense kukuuzani zinthu zina.
20 Chimodzi cha zoyenera zimenezo chimatchedwa kuyenera kwa informed consent, chimene chimatanthauza kuti palibe chisamaliro cha mtundu uliwonse chimene chingaperekedwe kwa inu popanda chilolezo chanu. Mukhozadi kukana chisamaliro chilichonse ngati mufuna. Muyenera kuvomereza chisamalirocho gulu la madokotalalo litakufotokozerani bwino lomwe zimene lifuna kuchita, kuphatikizapo ngozi zake zonse. Kenako, ayenera kukuuzani za njira zina zilizonse zimene zilipo. Ndiyeno, mutauzidwa, inu mungasankhe chisamaliro chimene mukufuna.
21 Kuti mutsimikizire zimene mukuvomerezazo, MUYENERA kufunsa mafunso omveka ponena za chilichonse chimene simukumvetsetsa, makamaka pamene mawu ovuta kumva kapena a zamankhwala agwiritsiridwa ntchito ndi antchito ya zachipatala. Mwachitsanzo, ngati dokotala anena kuti akufuna kugwiritsira ntchito “plasma,” inuyo mosadziŵa mungaganize kuti akunena za “plasma volume expander,” pamene sakutero. Musanavomereze, funsani kuti: “Kodi imeneyo ili mbali ya mwazi?” Ponena za njira yake iliyonse yochitira zinthu, funsani kuti: “Kodi chisamaliro chimenecho chikuphatikizapo kugwiritsira ntchito zinthu zamwazi?” Ngati alongosola chipangizo china chimene akufuna kugwiritsira ntchito, funsani kuti: “Kodi pali nthaŵi iliyonse pamene mwazi wanga udzasungidwa pogwiritsira ntchito chipangizocho?”
22 Koma kodi muyenera kuchitanji ngati mwachita zonse zimene zili pamwambazo ndipo sakugwirizanabe nanu kapena akutsutsabe kaimidwe kanu? Musazengereze kupempha thandizo. Ena ayembekezera kwanthaŵi yaitali kupempha thandizo naika miyoyo yawo pangozi.
THANDIZO LOFUNIKA M’NTHAŴI YA KUSOŴA
23 Onani njira yotsatirayi yopezera thandizo lofunikira: (1) Pamene inu kapena wokondedwa wanu afunikira opaleshoni yochita kukonzekera kapena yamwadzidzidzi ndipo pali mkangano chifukwa chakuti chipatala chikufuna kugwiritsira ntchito mwazi; kapena (2) ngati matenda anu kapena a wokondedwa wanu akula kwambiri; kapena (3) ngati ponena za mwana (kapena wachikulire), dokotala, nesi, kapena woyang’anira anena kuti adzapempha chilolezo cha khoti, pamenepo:
24 ITANANI AKULU AKWANUKO ngati simunachite zimenezo kale. (Ndithudi, chifukwa cha kaimidwe kathu ponena za mwazi, kuli kwanzeru kudziŵitsa akulu nthaŵi iliyonse imene tipita kuchipatala.) Kenako, ngati kuli kofunika, AKULU ADZAFIKIRA KOMITI YOLANKHULANA NDI CHIPATALA YAPAFUPI. Ngati mufuna, ziŵalo zina za Komiti Yolankhulana ndi Chipatala zingafike kuchipatala panthaŵiyi kudzakuthandizani.—Yes. 32:1, 2.
25 Akulu ameneŵa a m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala amadziŵa madokotala ogwirizanika amene ali m’dera lanu ndipo angakuchititseni kulankhula nawo ndipo amapereka maina a madokotala ena kapena zipatala zina zimene zingathandize. Ngati kulibe aliyense kumaloko, akuluwo adzafunsa komiti ina yapafupi. Ndipo ngati zimenezo zilephereka, adzafunsira ku Ofesi ya Chidziŵitso cha Zachipatala kunthambi. Iwo angakhozenso kulinganiza kuti dokotala wogwirizanikayo akambitsirane ndi madokotala amene akukusamalirani kuwafotokozera zimene zingachitidwe popanda mwazi. Abale a m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala aphunzitsidwa kusamalira nkhani zotero.
26 Ziŵalo za Makomiti Olankhulana ndi Chipatala zilinso zofunitsitsa kuthandiza inuyo kapena wachibale wanu kulankhula ndi dokotala kapena woyang’anira, koma muyenera kupempha thandizo limenelo. Ndithudi, abale ameneŵa sangakupangireni zosankha, koma kaŵirikaŵiri angakuthandizeni kulingalira za kaonedwe ka Sosaite ka nkhani zotero ndi kukudziŵitsani za zosankha zanu m’zamankhwala ndi mwalamulo.
27 Ngati gulu la madokotala silikufunabe kugwirizana nanu, kambitsiranani ndi woyang’anira chipatala za kuwasintha ndi kuika ena mwa antchito ake amene adzalemekeza zofuna zanu. Ngati woyang’anirayo azengereza kuchita zimenezo ndipo KOKHA ngati mulidi ndi dokotala wa opaleshoni wa kwinakwake ndipo mukhoza kusamutsidwa, mpamene mungasankhe kupatsa woyang’anirayo chikalata chokhala ndi deti ndi siginecha chikumasonyeza maina a madokotala osagwirizanika ndi kunena kuti sayenera kukusamalirani.
28 Kodi mungachite zimenezo? Inde, muli ndi kuyenera kumeneko. Ndipo ngati nkhaniyo ifika kwa woweruza, chikalata chanu chingamthandize kwambiri kuzindikira zofuna zanu. Mwina chingatsegulenso njira mogwirizana ndi makhalidwe abwino yakuti madokotala ena a opaleshoni tsopano agwepo ndi kukutumikirani. Ndipo, chofunika koposa, chingakuchititseni kupeza chisamaliro cha mankhwala chofunikira matenda anu asanakule kowopsa. Musayembekezere kwanthaŵi yaitali!
29 Pamene kuli kwakuti sitingauze aliyense kukhala ndi inshuwalansi ya umoyo, tiyenera kukudziŵitsani kuti kaŵirikaŵiri timakhala ndi mavuto aakulu kupeza dokotala wina amene kaŵirikaŵiri ali wogwirizanika kuti asamalire awo amene alibe inshuwalansi yokwanira kapena ya mankhwala iliyonse.
MAFUNSO OKHALA NZAMBIRI OFUNA KUKHALA NAWO MASO
30 Muyenera kudziŵa kuti pali mafunso ena amene madokotala ndi ena amafunsa amene si nthaŵi zonse pamene amafunsidwa ndi cholinga chabwino. Lomwe limafunsidwa nthaŵi zambiri ndi madokotala (ndi oweruza ena) nlakuti:
• “Kodi mungasankhe kufa (kulola mwana wanu kufa) mmalo mwa ‘kuthiridwa mwazi wopulumutsa moyo’?”
31 Ngati muyankha kuti inde, zimenezo zili zolondola m’lingaliro lachipembedzo. Koma yankho limenelo kaŵirikaŵiri limamvedwa molakwa ndipo nthaŵi zina limachititsadi khoti kugamula moipa. Muyenera kukumbukira kuti pamene muli mumkhalidwewu simuli mu utumiki. Mmalomwake, mukulankhula za chisamaliro cha mankhwala chofunikira. Chifukwa chake, muyenera kusinthira kwa omvetsera anu, kaya akhale madokotala kapena oweruza.—Sal. 39:1; Akol. 4:5, 6.
32 Kwa dokotala, woweruza, kapena woyang’anira chipatala, “inde” angatanthauze kuti mukufuna kukhala wofera chikhulupiriro kapena kuti mukufuna kupereka nsembe mwana wanu kaamba ka chikhulupiriro chanu. Kuwauza za chikhulupiriro chanu cholimba m’chiukiriro pamkhalidwewu sikudzathandiza kaŵirikaŵiri. Adzakuonani monga munthu wachipembedzo wotengeka maganizo, wosakhoza kupanga zosankha zanzeru pamene moyo uli pangozi. Ponena za ana, adzakuonani monga kholo losasamala losafuna chimene amatcha chisamaliro cha mankhwala “chopulumutsa moyo.”
33 Koma kwenikweni SIMUKUKANA chisamaliro cha mankhwala. Mwangosemphana ndi dokotala ponena za MTUNDU wa chisamalirocho. Kaŵirikaŵiri kaimidwe kameneka kadzasintha mkhalidwe wonsewo kwa iwo ndi kwa inu. Ndiponso, nkosokeretsa kwa iwo kupereka chithunzi chakuti mwazi uli wosungika ndi kuti ndiwo chisamaliro CHOKHA “chopulumutsa moyo.” (Onani Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?, masamba 7-22.) Chotero muyenera kumveketsa bwino mfundo imeneyo. Kodi mungachite motani zimenezo? Mungayankhe kuti:
• “Sindifuna (kuti mwana wanga afe) kufa. Ngati ndikanafuna (kuti mwana wanga afe) kufa, ndikanangokhala kunyumba. Koma ndadza kuno kudzafuna chisamaliro cha mankhwala kuti ndikhale (mwana wanga akhale) ndi moyo. Chimene ndifuna nchakuti chisamaliro cha mankhwala chiperekedwe kwa (mwana wanga) ine mwanjira ina popanda mwazi. Njira zina zilipodi.”
34 Mafunso ena angapo ofunsidwa kaŵirikaŵiri ndi madokotala ndi oweruza ngakuti:
• “Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa inu ngati muthiridwa mwazi mokakamizidwa ndi chilolezo cha khoti? Kodi mudzakhala ndi mlandu?”
• “Kodi kulandira kapena kukakamizidwa kuthiridwa mwazi kudzachititsa kuti muchotsedwe m’chipembedzo chanu kapena kumanidwa moyo wamuyaya? Kodi mpingo wanu udzakuonani motani?”
35 Mlongo wina anayankha woweruza wina kuti zimenezo zitachitika iye sangakhale ndi mlandu pa zimene woweruzayo wagamula. Ngakhale kuti kumbali ina zimenezo zinali zolondola, woweruzayo anaona zimenezo kukhala zikutanthauza kuti popeza kuti mlongoyo sangakhale ndi mlandu, ndiye kuti iye adzatenga mlanduwo kukhala wake mmalo mwa mlongoyo. Iye analamula kuti athiridwe mwazi.
36 Muyenera kudziŵa kuti pofunsa mafunso ameneŵa, ena kaŵirikaŵiri amafunafuna njira yokupatsirani mwazi umene mwakana. Musawapatse njirayo mosadziŵa! Chotero kodi ndimotani mmene tingapeŵere kumvedwa molakwa? Muyenera kuyankha kuti:
• “Ngati mwazi ukakamizidwa pa ine mwanjira iliyonse, kwa ine zidzafanana ndi kugwiriridwa chigololo. Ndidzavutika mumtima ndi mwauzimu kwa moyo wanga wonse chifukwa cha kuukiridwa kosafunika kumeneko. Ndidzakana ndi mphamvu zanga zonse kutchipitsa thupi langa kotero popanda ineyo kuvomereza. Ndidzachita zonse zothekera kuti ondiukirawo alangidwe monga momwe ndingachitire nditagwiriridwa chigololo.”
37 Chithunzi champhamvu, choonekera chakuti ife timaona kuthiridwa mwazi kokakamiza monga kutchipitsa matupi athu konyansa chiyenera kuperekedwa. Siili nkhani yopepuka. Chotero chirimikani. Mveketsani bwino lomwe kuti mukufuna kuti chisamaliro cha mankhwala chiperekedwe mwanjira ina popanda mwazi.
KODI MUDZACHITANJI KUTI MUKHALE WOKONZEKERA?
38 Tapenda zinthu zina zimene mufunikira kuchita kuti mudzitetezere inu ndi banja lanu ku kuthiridwa mwazi kosafunika. (M’kupita kwa nthaŵi, tikuyembekezera kukupatsani malangizo ena osamalirira mavuto amene amabuka pamene makanda ndi ana ayang’anizana ndi kuthiridwa mwazi.) Taonanso zimene Sosaite yachita mwachikondi kupereka thandizo m’nthaŵi ya kusoŵa. Kodi muyenera kuchitanji ndi chidziŵitso chimenechi kutsimikizira kuti muli wokonzekera kuyang’anizana ndi vuto la kuchipatala loyesa chikhulupiriro?
Choyamba: Khalani ndi makambitsirano a banja kuyeseza nkhani zimenezi ndi kupeza zimene mudzanena ndi kuchita, makamaka pa zakugwa za mwadzidzidzi.
Chotsatira: Tsimikizirani kuti muli ndi mapepala onse ofunikira.
Ndiyeno: Ipangeni kukhala nkhani ya pemphero laphamphu kwa Yehova kuti akuchirikizeni m’chosankha chanu cholimba cha ‘kusala mwazi.’ Kumvera lamulo lake ponena za mwazi kumatidzetsera chiyanjo chake kaamba ka moyo wosatha.—Mac. 15:29; Miy. 27:11, 12.
[Bokosi patsamba 5]
Ngati vuto lililonse la kuchipatala lifika powopsa kwakuti nkhani ya kuthiridwa mwazi ikhoza kubuka, pendani bokosi ili kuti muone zimene muyenera kuchita:
1. Itanani akulu a mpingo wanu kuti akuthandizeni.
2. Pemphani akulu kufikira Komiti Yolankhulana ndi Chipatala yapafupi ngati kufunikira.
3. Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ingakuthandizeni kulankhula ndi madokotala ndi ena.
4. Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ingakuthandizeni kupempha madokotala ena kuti akambitsirane ndi madokotala anu a opaleshoni za njira zina.
5. Komiti Yolankhulana ndi Chipatala ingakuthandizeninso kusamutsidwira kuchipatala chaulemu kwambiri kaamba ka chisamaliro chofunikira.