Kutseka Mpata Pakati pa Madokotala ndi Mboni Zodwala
MADOKOTALA kuzungulira padziko lonse kwakukulukulu amadziŵa chinthu chimodzi ponena za Mboni za Yehova: Kuti iwo amakana kuthiridwa mwazi. Komabe, madokotala ambiri amangodziŵa zina zochepa ponena za Mboni. Chotero pamene amafuna kuthira mwazi Mboni yodwala, kukanako kungawoneke kwa iwo kukhala kopanda nzeru kotheratu. Motero, mpata wochititsa chisoni ungalekanitse sing’anga ndi wodwala.
Ndimadokotala oŵerengeka kwambiri omwe amazindikira kuti Mboni za Yehova sizitsutsa kuchiritsa kwamankhwala ndikuti kaimidwe kawo pa mwazi kali ponse paŵiri kosakambitsirana ndi kozikidwa zolimba m’lamulo Lamalemba. Pakali pano, nzeru ya kaimidwe Kamalemba kameneka yakhala ikulemekezedwa pang’ono m’pang’ono ndi unyinji wa zopezedwa zasayansi zatsopano ponse paŵiri zamaupandu a kuthiridwa mwazi wa munthu wina ndi zakutetezereka kwa njira zina m’malo mwa kuthiridwa mwazi. Koma kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zingaperekere chidziŵitsochi ku chitaganya cha ogwira ntchito zamankhwala?
Makomiti Otigwirizanitsa Ndichipatala
Pachifukwa chimenecho, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linalinganiza kukhazikitsidwa kwa makomiti otigwirizanitsa ndichipatala m’mizinda yaikulu ndi zipatala zazikulu. Mu United States, makomiti okwanira zana limodzi, ndi avareji ya aminisitala asanu mu iliyonse, ayamba kale kutseka mpata pakati pa achigawo cha zamankhwala ndi Mboni. Kuchiyambi kwa chaka chino makonzedwewo anafutukulidwira ku maiko ena. Kuchokera February 19 mpaka March 27, ziŵalo zitatu za Hospital Information Services m’Brooklyn zinachezera maofesi anthambi asanu ndi atatu a Mboni za Yehova m’dera la Pacific.
Cholinga chinali chambali zitatu: kutsogoza masemina ophunzitsira aminisitala a Mboni zosankhidwira ntchito ya makomiti otigwirizanitsa ndichipatala, kuphunzitsa ogwira ntchito panthambi kusamalira desiki la Hospital Information Services m’nthambi iriyonse, ndikuchezera zipatala ndi madokotala kotero kuti alimbikitse kupitiriza kukulitsa njira zochiritsira Mboni za Yehova popanda kugwiritsira ntchito mwazi. Masemina anayi anachitidwa: imodzi m’Sydney kaamba ka Australia ndi New Zealand; imodzi m’Manila kaamba ka Philippines, Hong Kong, ndi Taiwan; imodzi mu Mzinda wa Ebina kaamba ka Japan ndi Korea; ndiyomalizira m’Honolulu kaamba ka Hawaii.
Programuyo inagwiritsira ntchito zonse ziŵiri zithunzithunzi za maslide ndi video kulongosola mmene mwazi umagwirira ntchito ndi zamkati mwake ndi njira zina zochiritsira zomawonjezereka mmalo mwa kuthiridwa mwazi wa munthu wina. Makambitsiranowo anasumika pa njira zothandizira Mboni za Yehova pamene ziyang’anizana ndi mavuto ochita ndi mwazi. Semina inagogomezeranso phindu lakugwirizana ndi madokotala ndi zipatala, mwakutero kukupangitsa kukhala kosavuta kwa iwo kulemekeza kaimidwe ka Mboni. Chiŵalo china cha komiti ya ku Japan chinati: “Programuyo inatikonzekeretsadi kuyamba ntchito yopititsa patsogolo kumvana.” Mboni zoposa 350 zamagulu onse a moyo zinaphunzitsidwa pa masemina anayiwo.
Kuchezako kusanayambe, maofesi anthambi anapanga mapangano okakumana ndi madokotala otumbula otchuka ndi akuluakulu azipatala zazikulu kuti akakambitsirane zakuchiritsa kosagwiritsira ntchito mwazi kaamba ka Mboni za Yehova. Magulu atatu panthambi iriyonse anagaŵiridwa kupanga maulendowo, lirilonse likutsogoleredwa ndi mmodzi wa oimira atatu ochokera ku Brooklyn. Izi sizinangopereka maphunziro apanthaŵi yomweyo kwa awo ogaŵiridwa kukhala ziŵalo za komiti yachipatala komanso zinawatheketsa kukhala omasuka polankhula ndi madokotala ndi akatswiri a zaumoyo. Maulendo oposa 55 oterowo anapangidwa m’nyengo ya milungu isanu ndi umodziyi.
Maulalo a Chigwirizano
Zotulukapo zinali zosangalatsa. Mu Australia gulu limodzi lochezera linakumana ndi wachiŵiri kwa nduna yaboma ya zaumoyo ya ku New South Wales. Iwo anakambitsirana naye zakupanga maopareshoni mosagwiritsira ntchito mwazi m’zipatala za zaumoyo zambiri, akumapereka lingaliro lakuti Australia ikakhala likulu la kutumbula koteroko kaamba ka Mboni za Yehova m’South Pacific. Iye sanawone chifukwa chimene magulu a madokotala sangakhazikitsidwire kumachita kutumbula koteroko. Maulendo ochezera 22 anapangidwa mu Australia. Dailekitala wina wachipatala anati: “Mumadziŵa zochuluka m’nkhani yamwazi ndi njira zosiyanasiyana zochiritsira kutiposa.” Mkulu wa akuluakulu a zipatala zisanu ndi ziŵiri anapereka chitsimikizo chakuti akasankha profesa wakutumbula kuti asamalire nkhani yakukhazikitsa gulu la madokotala otumbula pa chimodzi cha zipatala zawo kuti pakhale kuchiritsa kosagwiritsira ntchito mwazi kaamba ka Mboni za Yehova.
Pa chipatala cha odwala mtima cha ku Manila—cholingaliridwa ndi ena kukhala chabwino kwambiri Kummawa—chinatchulidwa kwa dailekitala wazamankhwala kuti Mboni za Yehova pafupifupi zana limodzi zoyembekezera kutumbulidwa mtima zinaiikidwa kumapeto kwa ondandalitsidwa chifukwa chokana mwazi. Iye anati akaleketsa kachitidweko. Dailekitala wazamankhwala wa chipatala chotchuka koposa cha ku Philippines, St. Luke’s, anasonyezedwa zimene mabuku a zamankhwala tsopano akunena ponena za kutumbula kosagwiritsira ntchito mwazi, ndipo anavomereza kuti nkotetezereka. “Ndichinthu chimene chikubwera,” iye anavomereza motero. “Ndiyo njira yokha imene tingapeŵere AIDS ndi kutupa chiŵindi.” Iye ananena kuti anali wokonzekera kupatsa Mboni mwaŵi wakulandira kuchiritsa kosagwiritsira ntchito mwazi pa chipatala chake; iye alinso pulezidenti wa malo osungira mwazi achipatalacho.
Pa semina yamasiku atatu ya ku Japan, Korea inaimiridwanso, ndi nthumwi 44 za Mboni za Yehova, 5 mwa izo anali madokotala. Ku Japan kunachokera aminisitala a Mboni 255, kuphatikizapo madokotala 41, mwa iwo ena anali adokotala otumbula mitsempha ndi akatswiri azakupha ululu potumbula, kudzanso maloya 2. Makomiti makumi aŵiri anakhazikitsidwa m’Japan, ndi asanu ndi aŵiri m’Korea.
Pambuyo pa seminayo, alangiziwo anapita ndi ziŵalo za komiti yachipatala yakumaloko kukachezera madokotala ndi zipatala m’dera la Tokyo kuchirikiza unansi wogwirizana. “Tinachezera profesa wothandizira kubadwa kwa makanda pa chipatala cha pa yunivesiti,” akusimba motero minisitala wa ku Japan. “Iye anathandiza kubadwa kwa makanda kwa a akazi osachepera pa khumi omwe ndi Mboni za Yehova. Mmodzi wa iwo anataikiridwa mwazi wokwanira makyubiki sentimita 2,800, ndipo mlingo wake wa hemoglobin unatsika kufika pa magiramu 3.5 pa desilita imodzi. (Avareji ya akazi ndi magiramu 14 pa desilita imodzi.) Koma dokotalayo anapeza chipambano m’kuthandiza kubalako mosagwiritsira ntchito mwazi. Chinkana kuti ndi m’Budda, lamulo lake nlakulemekeza zikhulupiriro za odwala ake. Iye analola kupitirizabe kulandira Mboni za Yehova zodwala.”
Dailekitala wazamankhwala m’Yokohama anavomereza kulembetsa chipatala chake pandandanda ya zipatala zofunitsitsa kugwirizana nafe ndipo anati iwo adzakhala achimwemwe kulandira Mboni zodwala zokanidwa ndi zipatala zina. “Kuchiritsa Mboni za Yehova mosagwiritsira ntchito mwazi,” anatero dokotalayo, “kulidi chitokoso, koma ndimayamikira Mboni chifukwa chakuti izo zandipatsa mwaŵi wakukulitsa maluso anga monga dokotala.” Munalinso m’Yokohama mmene katswiri wamatenda a akazi anati: “Ndingaumenyere ufulu woyenerera odwala m’khoti ngati ndidati ndiimbidwe mlandu wa kulemekeza zosankha za wodwalayo ndikusathira mwazi.”
Makomiti amene anakhazikitsidwa kaamba ka Korea akuchitira lipoti chipambano chabwino. Pa May 26 ulendo wochezera Yonsei University Hospital unapangidwa. Icho nchotchuka m’Korea monse ndipo chiri ndi nthambi zitatu. Ziŵalo zochokera ku malo atatu onsewo zinapezekapo, zikupanga chionkhetso cha 62. Profesa wa zakupha ululu potumbula analakhula za mbali “Yosamalira Zakupha Ululu Potumbula Mboni za Yehova Zodwala.” Chidziŵitso chimene anapereka chidzalembedwa m’magazini a m’Korea ophunzitsa ponena za kupha ululu potumbula. Popeza kuti n’chimodzi cha zipatala zotchuka m’Korea, ichi chiyenera kukhala ndi chisonkhezero chabwino pa zipatala zina ndi madokotala. Palibe funso limene linafunsidwa lomwe silinayankhidwe mokwanira pa semina ya ku Japan.
Makomiti otigwirizanitsa asanu anakhazikitsidwa kaamba ka Hawaii, ndipo onsewo anabwera ku Honolulu ku semina. Ambiri a iwo anatengedwa pamaulendo ochezera zipatala. Pa Hawaii Healthcare Center, dailekitala anati akalemba nkhani yonena za ife m’magazini awo ndikumiza ku zipatala zonse m’Hawaii.
Pa chipatala cha zaumoyo chachikulu koposa, cha Queen m’Honolulu, komiti inatchula kuti fomu yachimvano yogwiritsidwa ntchito ndi chipatalacho inalembedwa ndi mawu olakwika amene anaimira molakwa Mboni za Yehova. Iwo anatanthauza kuti Mboni zikasankha kufa mmalo molandira kuthiridwa mwazi “kopulumutsa moyo.” Kunawongoleredwa kuti kameneka sindiko kanalidi kaimidwe kathu, kuti timapita kuchipatala kukatetezera thanzi ndi moyo wathu. Mawu awo anakupangitsa kuwoneka ngati kuti mwazi ndiwo unali wabwino wokha ndikuti kusathiridwa mwazi kumafanana ndikukhala munthu wakufa. Mawu awo olembedwawo analephera kuvomereza kuthekera kwa imfa yochititsidwa ndi kuthiridwa mwazi, kuteroko kunali kummana wodwalayo chosankha chodziŵidwa bwino lomwe cha ngozi zimene angakhale wokonzekera kuyang’anizana nazo. Loya wachipatalacho anati: “Tandipatsani ndiwonepo!” Pamene anaiŵerenga, anati: “Sinde ndinalemba zimenezi!” Pamene loyayo ndi mkuluyo anachoka, mkuluyo anati kwa loyayo: ‘Ndikulingalira kuti tiyenera kuchipendanso pamodzi chikalatachi.’
Komiti Yatsopano Ikwaniritsa Chifuno Chake
M’masiku oŵerengeka pambuyo pa gawo lophunzira m’Hawaii, Mboni ina inafulumiziridwa kuchipatala yopereŵera mwazi moopsa, mwazi wake udapunguka mochititsa mantha. Komwe mwaziwo unkakhera sikunapezedwe; panafunikira kutumbula kofufuza. Dokotala sakatumbula popanda kugwiritsira ntchito mwazi. Mlongoyu anasamutsidwira ku chipatala china kumene dokotala winanso anakana kuchita opareshoniyo. Komiti yotigwirizanitsa yopangidwa chatsopanoyo inabwera, inakambitsirana ndi dailekitala wa zamankhwala ndi sing’anga yemwe analipoyo, nalongosola kuti, kwenikweni, wodwalayo adasiidwa. Dokotalayo anakanabe kupanga opareshoni ndipo anachotsedwa m’nkhaniyo. Madokotala otumbula aŵiri anabweretsedwa. Iwo anapanga opareshoniyo, napeza pomwe mwazi unkakhera, nakonza vutolo. Mlongo wathu anapulumuka. Popanda kuloŵamo kwa komiti yotigwirizanitsa, iye akanamwalira, ndipo ofalitsa nkhani akanakulongosola kukhala chochitika chinanso cha Mboni cha ‘kumwalira chifukwa chokana mwazi wofunikira.’ M’chenicheni, m’zochitika zoterozo Mboni zamwalira chifukwa chosoŵa kutumbula kofunikira pamene madokotala otumbula oyeneretsedwa akanazipulumutsa.
Pamenepa, pamlingo wadziko lonse, makomiti otigwirizanitsa ndichipatala akugwira ntchito kutseka mpata pakati pa ogwira ntchito zamankhwala ndi Mboni za Yehova kupyolera m’makambitsirano ophulapo kanthu ndi omvetsetsana. Zotulukapo zakhala zosangalatsa. Madokotala ambirimbiri akuyamba kuwona kuti kachitidwe kabwino kazamankhwala ndi kutumbula kwaluso zingamvane ndi zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Mu United States, madokotala oposa 6,500 ngofunitsitsa kuchita motero.
Kwa izo, Mboni ziyenera kupitirizabe kupanga kuyesayesa kulikonse kukhala odwala ogwirizanika ndi olingalira. Mwakutero, madokotala ena amalemekezadi Mboni kaamba ka kumamatira kwawo ku malamulo amakhalidwe abwino apamwamba. Monga momwe profesa wa mitsempha yankodzo pa koleji ina m’Tokyo ananenera kuti: “Ndimalemekeza odwala omwe ali Mboni za Yehova. Iwo ali ndi mikhalidwe yabwino yawoyawo m’dziko limene kulibe wina amene alinayo.”
Chonulirapo chachikulu cha masemina ndi maulendo ocheza ameneŵa chinali kuchirikiza chigwirizano cholemekezeka kwambiri ndipo mwakutero kupeŵa kukangana. Onse amene anaphatikizidwa m’kuyesayesa kumeneku analingalira kuti chonulirapo chimenechi chinafikiridwa ndi chipambano chosangalatsa. Tikukhulupirira kuti Yehova adzapitiriza kudalitsa zoyesayesa zimenezi ndikuchirikiza omvera chilangizo cha Yehova cha kusala mwazi, monga momwe Mawu ake akuwalamulira kutero.
[Bokosi patsamba 31]
‘Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.’
‘Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake. Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo aliyense wakugonera mwa inu asamadya mwazi.’
‘Pakuti chinakomera mzimu woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.’