Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 3/8 tsamba 12-13
  • Kulankhulana kwa Dokotala ndi Wodwala—Mfungulo Yonkira Kuchipambano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhulana kwa Dokotala ndi Wodwala—Mfungulo Yonkira Kuchipambano
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero Okhalapo Athandizo
  • Chitsimikizo Chakuti Amagwira Ntchito
  • Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kutseka Mpata Pakati pa Madokotala ndi Mboni Zodwala
    Galamukani!—1990
  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kupititsa Patsogolo Maopareshoni Opanda Mwazi pa Mboni za Yehova
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 3/8 tsamba 12-13

Kulankhulana kwa Dokotala ndi Wodwala—Mfungulo Yonkira Kuchipambano

KUCHIYAMBIYAMBI kwa ma 1980, kunali kwachiwonekere kuti njira zodziyambira zikayenera kutengedwa kukhazikitsa kulankhulana kwabwinopo pakati pa Mboni za Yehova ndi opatsa mankhwala. Chotero Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linalola programu yoyambitsa unansi wopindulitsa ndi adokotala ndi zipatala.

Oimira kuchokera pamalikulu a dziko lonse a Mbonizo mu Mzinda wa New York anachezera zipatala zambiri zazikulu mumzindawo. Ichi chinayamikiridwa kwambiri ndi antchito am’chipatala, ndipo chinayala maziko a kugwirizana, mmalo mwa kukangana. Oimiraŵa pambuyo pake anachititsa masemina m’mizinda yaikulu kuzungulira dzikolo. Monga mbali ya maseminaŵa, iwo ananka ndi aminisitala akumaloko a Mboni za Yehova ku misonkhano ya pamalikulu a zamankhwala m’deralo, mwakutero akumalangiza aminisitalawa kupitiriza ndi programuyi. Pamene anali m’Chicago, Illinois, U.S.A., iwo anakumana ndi mkonzi wa Journal of the American Medical Association. Ichi chinatulukapo kuitanidwa kukalemba nkhani yonena za mmene adokotala angagwirire ntchito ndi Mboni za Yehova.a

M’kupita kwanthaŵi, kuphunzitsa ndi zitsogozo zolembedwa zinaperekedwa pamaziko ofutukulidwa kotero kuti Mboni zokhala m’maiko ena ziyambe maprogramu ofananawo.b Mwachitsanzo, pambuyo pakutsogozedwa kwa semina mu Canada, Makomiti Otigwirizanitsa ndi Chipatala (omwe pambuyo pake komweko anadzatchedwa Makomiti Otigwirizanitsa ndi Zamankhwala) anapangidwa ndikuphunzitsidwa. Komiti iriyonse inali yopangidwa ndi akulu Achikristu ofunitsitsa ndi okhoza kulankhula kwa adokotala, antchito zamayanjano, ndi antchito za m’chipatala.

Mapangano anapangidwa ndi nduna zaboma m’zaumoyo m’zigawo zakutizakuti, atsogoleri a zigwirizano zamankhwala ndi zipatala, ndi ena otchuka m’chigawo chosamalira umoyo. Misonkhanoyi inathandizira kupangitsa ziungwe za zamankhwala kukhala zozindikira kwambiri chomwe Mboni za Yehova zimadera nkhaŵa. Chotero maziko olimba anayalidwa kaamba ka kukambitsirana kwamtsogolo.

Magwero Okhalapo Athandizo

Kwayamikiridwa kwanthaŵi yaitali kuti chidziŵitso cholongosoka ndithandizo lalikulu lopeputsira kuyang’anizana koyembekezeredwa pakati pa Akristu owona mtima ndi asing’anga omwe amadalira pakuchiritsa ndi mwazi. Kuchiyambi kwa ma 1960 pamalikulu a Mboni za Yehova, ndandanda ya adokotala amankhwala ogwirizanika inayamba kulembedwa. Awa anali asing’anga omwe anakhala ozoloŵerana ndi mankhwala oloŵa m’malo kuthira mwazi. Pambuyo pake, ngati dokotala wapamalopo kapena chipatala sichinali chomasuka kusamalira matendawo, komiti ikatenga maina a asing’anga ena. Wodwalayo pambuyo pake akasamutsidwira kwa asing’anga amankhwala ena.

Lingaliro lina linali lakuti Makomiti Otigwirizanitsa ndi Chipatala apange makonzedwe a kufunsa kwa pafoni pakati pa dokotala wotumbula wa kumaloko ndi anzake ozoloŵera. Nthaŵi zina mtundu wa kulankhulana kwa pomwepo umenewu unatheketsa adokotala kusintha thandizo lawo la mankhwala, popanda kuika moyo wa wodwalayo pachiswe. Chotero, potumikira monga wogwirizanitsa pakati pa wodwala ndi dokotala, makomitiwa akhala akatswiri akuchepetsa kuda nkhaŵa kwa onse aŵiri wodwala ndi dokotala pamene mwazi ungalingaliridwe kukhala wofunikira.

Chitsimikizo Chakuti Amagwira Ntchito

Sonya anali mwana wanzeru wa zaka 13 zakubadwa pamene, kuchiyambi kwa 1989, anadziŵa kuti anali ndi chotupa cha kansa pansi pa diso limodzi. Sing’anga wotumbula anafotokozera Sonya ndi makolo ake kufunikira kwamsanga kwa opareshoni. Popeza kuti chotupacho chinkakula mofulumira, kutumbula sikunafunikire kukanidwa. Mankhwala mwachiwonekere akafunikira pambuyo pake, ndipo dokotala anati makolo ake akafunikira kuvomereza kuthira mwazi. Koma banjalo silinavomerezane ndi chimenecho chifukwa cha zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Dokotala wotumbula waluso wosamalira Sonya anali wofunitsitsa kuchotsa chotupa cha kansacho, ndichidaliro chakuti akachita tero popanda kuthira mwazi. Komabe, chifukwa cha malamulo achipatala, dokotala wotumbulayo sanapeze katswiri wothandizira kupha ululu woti amthandize.

Jonathan ndimwana wamkulu wa Michael ndi Valerie. Kumapeto kwa 1989, pamene anali wa zaka 16, adokotala anaŵadziŵitsa kuti Jonathan anali ndi chotupa chachikulu m’kapamba wake. Adokotala anali ozengereza kumtumbula popanda kugwiritsira ntchito mwazi, komatu anatero molimba mtima, akumalemekeza kaimidwe kachipembedzo ka banjalo. M’nyengo ya kuchira, mavuto owopsa anabuka. Mphamvu ya mwazi wa Jonathan inatsika kwambiri, ndipo mwazi wake unaperewera. Mu opareshoni yachiŵiri, iye anataikiridwa mwazi wambiri, msanganizo wa m’mwazi wake wotchedwa hemoglobin unatsika nkufika pa chiŵerengero cha 5.5, ndicho pafupifupi mbali imodzi mwa zitatu za mlingo wabwino. Katswiri wa mankhwala am’mimba anafuula kuti: “Mkhalidwe wa mwana wanu ukuipiraipira. Tiri mumkhalidwe wa kayakaya. Ngati salandira mwazi, angafe!” Kodi akanachitanji?

Makomiti otigwirizanitsa anapereka thandizo lofunika m’matenda onse aŵiriwa m’Canada. Ina inatsimikizira banja la Sonya kuti kutakhala koyenerera, iwo akathandiza kupanga makonzedwe kuti iye asamutsidwire ku chipatala china chokhala m’dziko lina. Koma kodi chinachake chikanachitidwa kotero kuti dokotala wotumbula wamkazi wozoloŵerana kale ndi matenda ake apitirize ndi izi? Kwenikweni, dokotala wotumbulayu anamkonda kwambiri Sonya kwakuti anadzipereka kukhala mmodzi wa gulu la adokotala otumbula kulikonse kumene opareshoniyo ikachitikira. Komabe, kusamutsidwa sikunali kofunikira. Ziŵalo za komiti zinali zokhoza kusonkhezera antchito zamankhwala akumaloko kuti agwirizane ndi sing’anga wotumbulayo. Mogwirizana ndi dokotalayo, pambuyo pa opareshoni ya maola asanu ndi atatu ndi theka, mawu oyamba a Sonya anali funso lodera nkhaŵa lofuna kudziŵa kaya ngati mwazi unakakamizidwa pa iye. Kunali kosangalatsa chotani nanga kwa Sonya kumva yankho lakuti ayi!

M’matenda a Jonathan, pamene mwazi wake unatsikira pachiŵerengero cha 5.5 pambuyo pa maopareshoni aŵiri, adokotala anali okhutiritsidwa kuti kuthira mwazi kunali kofunika kupulumutsa moyo wake, ndipo anali okonzekera kupempha chilolezo cha khoti kuti amkakamize mwazi. Koma chikhulupiriro cholimba cha Jonathan ndikukana kwake kugwiritsira ntchito mwazi kunaŵafoketsa. Jonathan akusimba kuti: “Ndinagwira kolala ya Dr.— ndikumyang’ana m’maso ndikuti, ‘CHONDE, sindifuna mwazi kapena zam’mwazi!’” Komiti ya abale ophunzitsidwa inathandizira kukonzekera kuti Jonathan asamutsidwe pa ndege kunka ku chipatala chamankhwala chachikulu. Atafika kumeneko, chiŵalo cha komiti chinali pachipatalapo ndipo chidali chitalankhula kale ndi asing’anga okamgwirirapo ntchito. Tsiku lotsatira msanganizo wa m’mwazi wotchedwa hemoglobin wa Jonathan unakhazikika. Mwazi wake unawongokera mokhazikika, ndipo anatulutsidwa masiku 15 pambuyo pa kuchitidwa opareshoni koyamba.

Mowonekera bwino, pokhala ndi chiŵerengero chowonjezerekawonjezereka cha antchito za m’chipatala ndi antchito zamayanjano ofunitsitsa kugwira ntchito ndi Makomiti Otigwirizanitsa ndi Zipatala a Mboni za Yehova, chipambano chabwino chopitirizabe chingayembekezeredwe.

[Mawu a M’munsi]

a Losindikizidwanso pamasamba 27-9 a How Can Blood Save Your Life?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Tsopano muli Makomiti Otigwirizanitsa ndi Zipatala 100 m’United States, 31 m’Canada, 67 m’Falansa, ndi owonjezereka m’maiko ena kuzungulira dziko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena