Nyimbo 152
Kuyamikira Chifundo cha Mulungu
1. Chuma, nzeru ndi kudziŵa
Zikhala ndi Mulungu!
Ali wosasanthulika!
Muziweruzo zake!
Kodi ife tamlangiza
Kapena kumthandiza,
Kukhala nafe mangaŵa
Kuti tibwezeredwe?
2. Ndichifundo cha
Yehova Tikhale oyamika
Kupereka kwa Mulungu
Matupi amoyowa.
Pokhala tadzipereka,
Tikhaletu owona,
Ndi kudziŵa kwathu konse
Tichite zothekera.
3. Osayenda mwa dzikoli,
Tikonze maganizo
Mwa mphamvu ya chowonadi
Ndi chikhulupiliro.
Mopemphera kosaleka,
Titumike mofatsa
Kusonyezana chikondi;
Tidzapeza mtendere.