Nyimbo 179
Tiyenera Kuyembekezera Yehova
1. ‘Kagulu ka nkhosako.’
Kayembekezera Ya.
Adzachita ufumu;
Ayembekezeradi.
Kristu alamula;
Ali woyenera.
Adzapereka mphotho
Kwa anthu akewo
Olengeza ’Fumu.
2. Mabwenzi awo ndiwo
Khamu la “nkhosa zina.”
Onse chokhumba chawo
Ndikusunga umphumphu.
Kuŵala kukula
Adikilirabe
Kusonyezatu ana
Kodzetsa mtendere,
Indedi mtendere.
3. Ya walonjeza anthu
Za dziko latsopano.
Mokhala kulungama,
Pobadwa Ufumuwo.
Timalakalaka,
Pomwe tiphunzira.
Timadalira mwa Ya;
Timuyembekeze.
Timuyembekeze.