Nyimbo 205
Kristu Chitsanzo Chathu
1. Nchikondi chotani Yehova asonya,
Kutumi zira Mwanake!
Kristu monga Mkate, Kuti anthu adye
Kupeza moyo wosatha.
2. Kristu anasonya Njira yopemphera:
‘Dzinalo liyeretsedwe.
Ufumuwo udze. Chifuniro chanu
Chichitidwe pansi pano.’
3. Anaphunzitsatu Cho’nadi mwachangu
Kwa omvera mawu ake.
Nafera pamtengo Kuombo la anthu
Kukwanitsa mawu a Ya.
4. Tikayamikira Nsembeyo ya Yesu,
Tiri onga ngati “nkhosa.”
Titamande M’lungu Nthaŵi zonse, ndipo,
Ndi Kristu, tipeze mphotho.